Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 46

NYIMBO NA. 49 Tizisangalatsa Mtima wa Yehova

Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mtumiki Wothandiza?

Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mtumiki Wothandiza?

“Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”​—MAC. 20:35.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi ilimbikitsa abale obatizidwa kuti ayesetse kukhala atumiki othandiza.

1. Kodi mtumwi Paulo ankawaona bwanji atumiki othandiza?

 ATUMIKI othandiza amagwira ntchito zofunika kwambiri mumpingo. N’zoonekeratu kuti mtumwi Paulo ankayamikira kwambiri amuna okhulupirikawa. Mwachitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Filipi, iye anapereka moni kwa akulu komanso atumiki othandiza.​—Afil. 1:1.

2. Kodi M’bale Luis amamva bwanji chifukwa chokhala mtumiki wothandiza?

2 Abale ambiri obatizidwa, kaya achikulire kapena achinyamata, amasangalala kwambiri akakhala atumiki othandiza. Mwachitsanzo, Devan anali ndi zaka 18 pamene anakhala mtumiki wothandiza. Pomwe M’bale Luis anakhala mtumiki wothandiza ali ndi zaka za m’ma 50. Pofotokoza mmene anamvera, M’bale Luis ananena kuti: “Ndikaganizira chikondi chimene mpingo umandisonyeza, ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala mtumiki wothandiza.” Umu ndi mmenenso abale ambiri amamvera.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi mungayesetse kuti mukhale mtumiki wothandiza? Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kuti mufune kukhala mtumiki wothandiza? Kodi Baibulo limati ndi makhalidwe ati amene muyenera kukhala nawo kuti mukhale mtumiki wothandiza? Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso amenewa. Koma choyamba, tiyeni tikambirane ntchito zimene atumiki othandiza amagwira.

KODI ATUMIKI OTHANDIZA AMAGWIRA NTCHITO ZITI?

4. Kodi atumiki othandiza amagwira ntchito ziti? (Onaninso chithunzi.)

4 Mtumiki wothandiza amakhala m’bale wobatizidwa yemwe amaikidwa ndi akulu kuti aziwathandiza pa ntchito zina mumpingo. Atumiki othandiza ena amaonetsetsa kuti ofalitsa ali ndi magawo olalikira okwanira komanso mabuku oti azigwiritsa ntchito mu utumiki. Ena amathandiza pokonza ndi kuyeretsa Nyumba ya Ufumu. Atumiki othandiza amalandiranso alendo komanso amasamalira zipangizo zokuzira mawu ndi kuonetsera mavidiyo pamisonkhano. Ngakhale kuti nthawi zambiri amagwira ntchito zimenezi, chofunika kwambiri n’chakuti ayenera kukhala anthu amene amakonda Yehova ndiponso kutsatira mfundo zake zolungama. Iwo amafunikanso kukonda kwambiri abale ndi alongo awo. (Mat. 22:37-39) Kodi m’bale wobatizidwa angatani kuti akhale mtumiki wothandiza?

Atumiki othandiza akutsanzira Yesu potumikira ena (Onani ndime 4)


5. Kodi m’bale angatani kuti akhale mtumiki wothandiza?

5 Baibulo limafotokoza makhalidwe amene munthu ayenera kukhala nawo kuti akhale mtumiki wothandiza. (1 Tim. 3:8-10, 12, 13) Kuti mukhale mtumiki wothandiza muyenera kuphunzira makhalidwe amenewa n’kumayesetsa kuwasonyeza. Koma choyamba, muyenera kufufuza chimene chikukuchititsani kufuna kukhala mtumiki wothandiza.

N’CHIFUKWA CHIYANI MUKUFUNA KUKHALA MTUMIKI WOTHANDIZA?

6. N’chiyani chimakulimbikitsani kuti muzitumikira abale ndi alongo anu? (Mateyu 20:28; onaninso chapachikuto.)

6 Yesu Khristu ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Iye ankachita zinthu chifukwa chokonda Atate wake komanso anthu. Chikondi chimenechi chinkamulimbikitsa kugwira ntchito mwakhama ngakhale ntchito zooneka ngati zonyozeka. (Werengani Mateyu 20:28; Yoh. 13:5, 14, 15) Ngati inunso mumachita zinthu chifukwa cha chikondi, Yehova adzakudalitsani kuti mukwaniritse cholinga chanu chofuna kukhala mtumiki wothandiza.​—1 Akor. 16:14; 1 Pet. 5:5.

Yesu akupereka chitsanzo kwa atumwi ake pa nkhani yotumikira ena modzichepetsa m’malo mofuna udindo wapamwamba (Onani ndime 6)


7. N’chifukwa chiyani m’bale ayenera kupewa mtima wonyada?

7 M’dzikoli, anthu amasirira anthu amene amafuna kukhala apamwamba. Koma si mmene zilili m’gulu la Yehova. M’bale amene amachita zinthu chifukwa cha chikondi ngati Yesu, salakalaka malo apamwamba, mphamvu kapena udindo. Munthu amene amafuna kukhala wapamwamba akapatsidwa udindo mumpingo, sangamalole kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka pothandiza anthu a Yehova. Atha kumaona kuti ntchito zimenezo si zoyenera kwa iyeyo. (Yoh. 10:12) Yehova samadalitsa aliyense amene amachita zinthu chifukwa cha kunyada.​—1 Akor. 10:24, 33; 13:4, 5.

8. Kodi ndi malangizo ati amene Yesu anapereka kwa atumwi ake?

8 Nthawi zina ngakhale ophunzira a Yesu ankafuna maudindo pa zifukwa zolakwika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yakobo ndi Yohane. Iwo anapempha Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Yesu sanawayamikire kuti iwo anachita bwino kupempha zimenezi. M’malomwake iye anauza atumwi onse 12 kuti: “Aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wa onse.” (Maliko 10:35, 43, 44) Abale amene amakhala ndi mtima wofuna kutumikira ena, amathandiza kwambiri mumpingo.​—1 Ates. 2:8.

KODI N’CHIYANI CHINGAKULIMBIKITSENI KUTI MUZITUMIKIRA ABALE NDI ALONGO ANU?

9. Kodi mungatani kuti mukhale ndi mtima wofuna kutumikira ena?

9 N’zosachita kufunsa kuti mumakonda Yehova ndipo mumafuna kutumikira ena. Koma mwina mulibe mtima wofuna kukhala mtumiki wothandiza. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi mtima wofuna kutumikira ena? Muziganizira chimwemwe chimene mungapeze chifukwa chotumikira abale ndi alongo anu. Paja Yesu anati: “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Ndipotu izi ndi zimene iye ankachita. Iye ankasangalala chifukwa chotumikira ena ndipo inunso mukhoza kumasangalala.

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda kutumikira ena? (Maliko 6:31-34)

10 Tiyeni tione chitsanzo chosonyeza kuti Yesu ankakonda kutumikira ena. (Werengani Maliko 6:31-34.) Pa nthawi ina, iye ndi ophunzira ake anatopa ndipo ankapita kwaokha kuti akapume. Koma gulu la anthu linafika kumeneko mwamsanga n’kumayembekezera kuti Yesu awaphunzitse. Yesu akanatha kukana kuwaphunzitsa. Ndipotu paja iye ndi ophunzira ake “analibe nthawi yoti apume ngakhalenso yoti adye chakudya.” Apo ayi, akanatha kungowaphunzitsa zochepa n’kuwauza kuti azipita. Koma chifukwa chokonda anthu, “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” Ndipo anapitiriza kuwaphunzitsa mpaka ‘nthawi inatha.’ (Maliko 6:35) Yesu anachita zimenezi osati chifukwa chakuti n’zimene ankafunika kuchita, koma “anawamvera chisoni.” Iye ankafuna kuwaphunzitsa chifukwa choti ankawakonda. Yesu ankasangalala kwambiri chifukwa chotumikira anthu ena.

11. Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu amene ankawaphunzitsa? (Onaninso chithunzi.)

11 Pa utumiki wake, Yesu anaphunzitsa anthu komanso kuwapatsa zofunika pa moyo. Iye anapereka chakudya ndipo anauza ophunzira ake kuti agawe chakudyacho kwa anthuwo. (Maliko 6:41) Pochita zimenezi, anaphunzitsa ophunzira ake kuti azitumikira ena. Iye anasonyeza kuti ntchito ngati zimene amagwira atumiki othandiza ndi zofunika. Atumwiwo ayenera kuti anasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi Yesu yopereka chakudya moti mpaka anthuwo “anadya n’kukhuta.” (Maliko 6:42) Aka sikanali koyamba kuti Yesu aike patsogolo zofuna za ena. Pa moyo wake wonse ankatumikira anthu ena. (Mat. 4:23; 8:16) Yesu ankasangalala kwambiri kuphunzitsa anthu komanso kuwathandiza kupeza zinthu zofunika. Inunso mudzasangalala kwambiri ngati mutayesetsa kuti mukhale mtumiki wothandiza.

Kukonda Yehova komanso kufunitsitsa kutumikira ena kudzakulimbikitsani kuti muzitumikira abale ndi alongo mumpingo (Onani ndime 11) a


12. N’chifukwa chiyani simuyenera kuganiza kuti simungathe kuchita chilichonse chothandiza mumpingo?

12 Ngati mukuona kuti mulibe luso linalake lapadera, musataye mtima. Chifukwa n’zosakayikitsa kuti muli ndi makhalidwe ena omwe angathandize anthu mumpingo. Kuwerenga malangizo a Paulo a pa 1 Akorinto 12:12-30 komanso kuipempherera nkhaniyo, kungakuthandizeni. Mawu a Paulo amasonyeza kuti inuyo, mofanana ndi mtumiki wa Yehova aliyense, ndinu wofunika mumpingo. Ngati panopa simukuyenerera kukhala mtumiki wothandiza, musataye mtima. M’malomwake, muzingochita zonse zomwe mungathe potumikira Yehova komanso abale ndi alongo anu. Dziwani kuti akulu adzakupatsani zochita mogwirizana ndi zimene mungathe.​—Aroma 12:4-8.

13. Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chingachititse munthu kuti apatsidwe udindo?

13 Chifukwa chimodzi chimene chingakuchititseni kuti mufune kukhala mtumiki wothandiza ndi chakuti makhalidwe amene amafunika kuti munthu akhale mtumiki wothandiza ndi ofunikanso kwa Akhristu onse. Akhristu onse amafunika kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kumasangalala chifukwa chopatsa ena zinthu komanso kukhala chitsanzo chabwino kwa ena. Ndiye kodi ndi zinthu ziti zimene m’bale angachite kuti akhale mtumiki wothandiza?

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKHALE MTUMIKI WOTHANDIZA

14. Kodi mawu akuti ‘wopanda chibwana’ amatanthauza chiyani? (1 Timoteyo 3:8-10, 12)

14 Tsopano tiyeni tikambirane makhalidwe omwe afotokozedwa pa 1 Timoteyo 3:8-10, 12. (Werengani.) Mtumiki wothandiza ayenera kukhala ‘wopanda chibwana.’ Mawu akuti “wopanda chibwana” angamasuliridwenso kuti “wolemekezeka.” Izi sizikutanthauza kuti simungaseke kapena kuchita nthabwala. (Mlal. 3:1, 4) M’malomwake muyenera kuchita khama pokwaniritsa udindo wanu. Anthu mumpingo akadziwa kuti ndinu wodalirika, amayamba kukulemekezani.

15. Kodi mawu akuti ‘wosanena pawiri’ komanso akuti ‘wosakonda kupeza phindu mwachinyengo’ amatanthauza chiyani?

15 ‘Wosanena pawiri.’ Mawu amenewa akusonyeza kuti muyenera kukhala woona mtima komanso wokhulupirika. Mumayesetsa kuchita zimene mwanena ndipo simunamiza ena. (Miy. 3:32) ‘Wosakonda kupeza phindu mwachinyengo.’ Mawu amenewa akusonyeza kuti muyenera kukhala oona mtima pa nkhani za bizinesi kapena ndalama. Simudzapezerapo mwayi pa ubwenzi wanu ndi Akhristu ena kuti mupeze ndalama.

16. (a) Kodi mawu akuti ‘wosamwa vinyo wambiri’ amatanthauza chiyani? (b) Kodi mawu akuti kukhala ndi “chikumbumtima choyera” akutanthauza chiyani?

16 ‘Wosamwa vinyo wambiri.’ Izi zikutanthauza kuti simuyenera kumamwa kwambiri mowa kapena kumadziwika monga chidakwa. Kukhala ndi “chikumbumtima choyera.” Mawu amenewa akusonyeza kuti muyenera kumatsatira mfundo za Yehova. Ngakhale kuti si inu wangwiro, mumakhala ndi mtendere umene umabwera chifukwa chakuti muli pa ubwenzi ndi Yehova.

17. Kodi m’bale angasonyeze bwanji kuti ndi wodalirika pamene ‘akuyesedwa kaye ngati ali woyenerera’? (1 Timoteyo 3:10; onaninso chithunzi.)

17 ‘Ayesedwe kaye ngati ali woyenerera.’ Mawu amenewa akutanthauza kuti mwayamba kale kusonyeza kuti ndinu wodalirika ndipo mungasamalire bwino maudindo anu. Choncho akulu akakupatsani zochita, muzitsatira mosamala malangizo awo komanso malangizo amene gulu limapereka. Mukamagwira bwino ntchito zimene mwapatsidwa, anthu ena mumpingo amaona ndipo amayamikira. Akulu ayenera kuyesetsa kuphunzitsa abale obatizidwa. (Werengani 1 Timoteyo 3:10.) Kodi mumpingo wanu muli achinyamata omwe sanakwanitse zaka 20? Kodi amayesetsa kuphunzira Baibulo paokha? Kodi amayankha pamisonkhano komanso kulowa mu utumiki? Ngati ndi choncho, muziwapatsa ntchito zogwirizana ndi msinkhu wawo komanso mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti ‘mukuwayesa kaye ngati ali oyenerera.’ Mukatero akhoza kukhala atumiki othandiza asanakwanitse zaka 20.

Akulu akamapereka zochita kwa abale obatizidwa amakhala ‘akuwayesa kaye ngati ali oyenerera’ (Onani ndime 17)


18. Kodi mawu akuti “opanda chifukwa chowanenezera” amatanthauza chiyani?

18 “Opanda chifukwa chowanenezera.” Mawu amenewa akutanthauza kukhala wopanda mlandu wochita tchimo lalikulu. N’zoona kuti nthawi zina Mkhristu akhoza kuimbidwa mlandu wabodza. Yesu anaimbidwa mlandu wabodza ndipo iye ananena kuti otsatira ake adzakumananso ndi zomwezo. (Yoh. 15:20) Komabe mukamayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino ngati Yesu, mudzakhala ndi mbiri yabwino mumpingo.​—Mat. 11:19.

19. Kodi kukhala ‘mwamuna wa mkazi mmodzi’ kumatanthauza chiyani?

19 ‘Mwamuna wa mkazi mmodzi.’ Ngati muli pa banja, muyenera kumatsatira zimene Yehova anakonza pachiyambi, zoti mwamuna mmodzi azikhala ndi mkazi mmodzi. (Mat. 19:3-9) Mwamuna yemwe ndi Mkhristu sayenera kuchita chiwerewere. (Aheb. 13:4) Koma si zokhazo. Iye ayenera kukhala wokhulupirika ndipo sayenera kukopana ndi akazi ena.​—Yobu 31:1.

20. Kodi mwamuna yemwe ‘amayang’anira bwino’ banja lake amachita zotani?

20 “Oyangʼanira bwino ana awo ndi mabanja awo.” Ngati ndinu mutu wa banja, muyenera kuchita khama pokwaniritsa udindo wanu. Nthawi zonse muzichita kulambira kwa pabanja. Muzilalikira pafupipafupi ndi anthu a m’banja lanu. Muzithandiza ana anu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Aef. 6:4) Mwamuna yemwe amasamalira bwino banja lake amasonyeza kuti akhozanso kusamalira bwino mpingo.​—Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 3:5.

21. Kodi mungatani ngati panopa si inu mtumiki wothandiza?

21 Ngati ndinu m’bale koma si inu mtumiki wothandiza, tikukulimbikitsani kuti muganizire mfundo za munkhaniyi komanso kuipempherera. Werengani zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale mtumiki wothandiza n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. Muziganizira mmene mumakondera Yehova komanso abale ndi alongo anu. Ndipo muziyesetsa kukhala ndi mtima wofuna kuwatumikira. (1 Pet. 4:8, 10) Mukayesetsa kuti mukhale mtumiki wothandiza mudzasangalala kutumikira abale ndi alongo anu mumpingo. Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukhale mtumiki wothandiza.​—Afil. 2:13.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

a MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Kumanzere, Yesu akutumikira ophunzira ake modzichepetsa; kumanja, mtumiki wothandiza akuthandiza m’bale wachikulire mumpingo.