Muzigwira Bwino Ntchito Yanu Yolalikira
“Gwira ntchito ya mlaliki, ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.”—2 TIM. 4:5.
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi mlaliki wamkulu komanso woyamba?
MLALIKI ndi munthu amene amalengeza uthenga wabwino. Mlaliki wamkulu komanso woyamba ndi Yehova Mulungu. Makolo athu oyambirira atangopanduka, Yehova analengeza uthenga wabwino wakuti njoka, kapena kuti Satana Mdyerekezi, idzawonongedwa. (Gen. 3:15) Kwa zaka zambiri, Yehova anauza anthu okhulupirika kuti alembe nkhani zofotokoza mmene iye adzayeretsere dzina lake ndiponso kukonza zimene Satana wawononga. Anawauzanso kuti alembe zimene iye adzachite pothandiza anthu kupeza madalitso amene Adamu ndi Hava anataya.
2. (a) Kodi angelo amathandiza bwanji pa ntchito yolalikira? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa alaliki?
2 Nawonso angelo ndi alaliki. Iwo amalengeza uthenga wabwino ndiponso amathandiza anthu kulengeza uthengawo. (Luka 1:19; 2:10; Mac. 8:26, 27, 35; Chiv. 14:6) Nanga bwanji Yesu, yemwe ndi Mikayeli mkulu wa angelo? Pamene iye anali padziko lapansi, anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa alaliki. Iye ankaika patsogolo ntchito yolalikira uthenga wabwino.—Luka 4:16-21.
3. (a) Kodi timalalikira uthenga wabwino uti? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Yesu analamula ophunzira ake kuti azilalikira. (Mat. 28:19, 20; Mac. 1:8) Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Gwira ntchito ya mlaliki, ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.” (2 Tim. 4:5) Kodi Akhristufe timalalikira uthenga wabwino uti? Mfundo ina yolimbikitsa ya uthenga umene timalalikirawu ndi yakuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, amatikonda kwambiri. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 5:7) Ufumu wa Mulungu ndi njira imodzi imene Yehova akusonyezera kuti amatikonda kwambiri. Choncho timasangalala kuuzanso anthu kuti akamagonjera Ufumuwo, kumvera Mulungu ndiponso kuchita chilungamo, adzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulunguyo komanso anthu ake. (Sal. 15:1, 2) Cholinga cha Yehova n’chakuti athetseretu mavuto onse. Iye adzatithandiza kuti tisamavutikenso mumtima chifukwa chokumbukira mavuto amene tinakumana nawo. Umenewutu ndi uthenga wabwino kwambiri. (Yes. 65:17) Popeza ndife alaliki, tiyeni tikambirane mafunso awiri ofunika kwambiri awa: N’chifukwa chiyani anthu akufunikira kumva uthenga wabwino masiku ano? Kodi tingatani kuti tizigwira bwino ntchito yathu yolalikira?
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AKUFUNIKIRA KUMVA UTHENGA WABWINO?
4. Kodi anthu amauzidwa mabodza ati onena za Mulungu?
4 Tiyerekeze kuti mwauzidwa kuti bambo anu ananyanyala banja lanu. Ndiyeno anthu amene amawadziwa bambo anuwo akunena kuti anali munthu wodzikonda, wobisa zinthu ndiponso wankhanza. Anthu ena akunenanso kuti musayese kuwafufuza chifukwa anamwalira. Izi ndi zimene anthu ena amauzidwa ponena za Mulungu. Iwo amauzidwa kuti munthu sangadziwe Mulungu ndipo iye ndi wankhanza. Mwachitsanzo, atsogoleri ena achipembedzo amanena kuti Mulungu adzalanga anthu powazunza kwamuyaya. Ena amanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa masoka achilengedwe. Ngakhale kuti masokawo amapha anthu abwino ndi oipa omwe, iwo amati ndi chilango chochokera kwa Mulungu.
5, 6. Kodi zikhulupiriro zabodza zasokoneza bwanji anthu?
5 Anthu ena amanena kuti kulibe Mulungu. Ambiri amene amakhulupirira zimenezi amanena kuti zinthu sizinachite kulengedwa koma zinangokhalako zokha. Ena amati anthufe tangokhala mtundu wina wa nyama ndipo tisamadabwe tikaona ena akuchita zinthu ngati nyamazo. Iwo amanena kuti anthu amphamvu akamapondereza anthu ofooka amakhala akungochita zimene zamoyo zonse zimachita mwachibadwa. Choncho anthu ambiri amakhulupirira kuti padzikoli sipangakhale chilungamo. Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo sizinachite kulengedwa sakhala ndi chiyembekezo chilichonse.
6 Zikhulupiriro zabodza ngati zimenezi zawonjezera mavuto amene anthu amakumana nawo m’masiku otsiriza ano. (Aroma 1:28-31; 2 Tim. 3:1-5) Zikhulupiriro zimenezi sizipereka uthenga wabwino. Koma monga mtumwi Paulo ananena, zimachititsa kuti anthu akhale ‘mu mdima wa maganizo ndiponso otalikirana ndi moyo wa Mulungu.’ (Aef. 4:17-19) Kuwonjezera pamenepo, zikhulupirirozi zachititsa kuti anthu ena asamvetsere uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu.—Werengani Aefeso 2:11-13.
7, 8. Kodi ndi njira iti imene ingathandize anthu kumvetsetsa uthenga wabwino?
7 Kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ayenera kukhulupirira kuti iye aliko. Ayenera kukhulupiriranso kuti m’pofunika kukhala naye pa ubwenzi. Kulimbikitsa anthu kuganizira za chilengedwe kungawathandize kukhulupirira zimenezi. Anthu amene ali ndi mtima wofunitsitsa kudziwa choonadi akamaphunzira za chilengedwe, amazindikira kuti Mulungu ndi wanzeru ndiponso wamphamvu. (Aroma 1:19, 20) Kuti tithandize anthu kulemekeza kwambiri Mlengi wathu wamkulu chifukwa cha zimene wachita, tingagwiritse ntchito nkhani zopezeka m’magazini ndi mabuku athu. Mwachitsanzo, tingagwiritse ntchito nkhani yakuti “Kodi Maganizo Olondola Ndi Ati?” mu Galamukani! ya November 2011 kapena nkhani yakuti “Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Mulungu?” mu Galamukani! ya February 2010. * Komabe anthu sangapeze mayankho a mafunso ena ovuta kwambiri pongoganizira za chilengedwe. Mwachitsanzo, sangapeze yankho la funso lakuti: N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Kapena lakuti: Kodi Mulungu analengeranji dzikoli? Ndiponso lakuti: Kodi Mulungu amandikonda ineyo pandekha?
8 Njira imodzi yokha imene ingathandize anthu kudziwa uthenga wabwino wonena za Mulungu ndiponso cholinga chake ndi kuphunzira Baibulo basi. Tili ndi mwayi waukulu wothandiza anthu kupeza mayankho a mafunso awo. Komabe powathandiza, tisamangowauza zinthu koma tiziphunzira nawo m’njira yakuti afike pokhulupirira zimene tikuwauzazo. (2 Tim. 3:14) Izi zikhoza kutheka ngati titatsatira chitsanzo cha Yesu. Kodi Yesu ankaphunzitsa bwanji kuti awafike anthu pa mtima? Njira imodzi ndi yakuti ankafunsa mafunso mwaluso. Kodi tingamutsanzire bwanji?
ALALIKI ABWINO AMAFUNSA MAFUNSO MWALUSO
9. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize anthu amene timawalalikira?
9 N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani yofunsa mafunso tikamalalikira? Tiyerekeze kuti dokotala wanena kuti ali ndi uthenga wabwino woti akuuzeni. Iye akuti mukhoza kuchira matenda anu ngati mutachitidwa opaleshoni yaikulu. N’kutheka kuti mungamukhulupirire. Koma kodi mungamukhulupirire ngati iye atanena zimenezo asanakufunseni mmene mukumvera? N’zokayikitsa kuti mungamukhulupirire. Ngakhale atakhala wodziwa kwambiri ntchito yake, dokotala amafunika kufunsa mafunso ndiponso kumvetsera kuti adziwe bwino matenda anu asanapereke thandizo lililonse. Kuti ifenso tithandize anthu kukhulupirira uthenga wabwino wa Ufumu, tiyenera kuwafunsa mafunso mwaluso. Tingathe kuwathandiza pambuyo podziwa bwinobwino mavuto awo.
Tiyenera kuthandiza anthu kuti afike pokhulupirira zimene tikuwauzazo
10, 11. Kodi chingachitike n’chiyani tikamatsanzira Yesu pophunzitsa?
10 Yesu ankadziwa kuti mafunso abwino sikuti amangothandiza mphunzitsi kudziwa za munthu amene akuphunzira naye koma amathandizanso wophunzirayo kuti azilankhulapo. Mwachitsanzo, pamene Yesu ankafuna kuphunzitsa ophunzira ake kuti azikhala odzichepetsa, choyamba anawafunsa funso lowathandiza kuganiza. (Maliko 9:33) Pa nthawi ina, pofuna kuthandiza Petulo kuti aganizire mfundo inayake, iye anamufunsa funso lokhala ndi mayankho awiri kuti asankhepo. (Mat. 17:24-26) Pa nthawi inanso, Yesu ankafuna kudziwa maganizo a ophunzira ake, choncho anawafunsa mafunso angapo. (Werengani Mateyu 16:13-17.) Pophunzitsa, Yesu ankafunsa mafunso ndiponso kufotokoza mfundo momveka bwino. Izi zinkathandiza kuti anthu amvetse mfundozo komanso ziwafike pa mtima n’kuyamba kuchita zinthu mogwirizana ndi uthenga wabwino.
11 Tikamafunsa mafunso mwaluso ngati mmene Yesu ankachitira, timachita zinthu zitatu. Timadziwa njira yabwino imene tingathandizire anthu, timatha kuphunzira ndi anthu amene sankafuna kukambirana ndiponso timathandiza anthu odzichepetsa kuti ayambe kutsatira zimene akuphunzira. Tiyeni tikambirane zitsanzo zitatu zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mafunso mwaluso.
12-14. Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kukhala wolimba mtima pouza anzake uthenga wabwino? Perekani chitsanzo.
12 Chitsanzo choyamba: Tiyerekeze kuti ndinu kholo ndipo mwana wanu akuopa kufotokozera mnzake wakusukulu zimene amakhulupirira pa nkhani yoti zamoyo zinachita kulengedwa. Sitikukayikira kuti mungafunitsitse kuti mwana wanuyo aziuza anzake uthenga wabwino molimba mtima. Choncho m’malo momukalipira kapena kufulumira kumuuza zoyenera kunena, mungachite bwino kutsanzira Yesu pomufunsa mafunso kuti mudziwe maganizo ake. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
13 Pambuyo powerenga ndi mwana wanuyo nkhani yakuti “Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Mulungu?” mu Galamukani! ya February 2010, mungamufunse kuti anene mfundo zimene akuona kuti n’zothandiza. M’thandizeni kuti apeze yekha zifukwa zimene zimamuchititsa kukhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu. Anenenso zimene zikumuchititsa kuganiza kuti ndi bwino kuchita zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:2) Muuzeni kuti zifukwa zimene angatchule sizifunika kukhala zofanana ndendende ndi zanu.
14 Ndiyeno muuzeni mwanayo kuti akamakambirana ndi mnzakeyo, akachite mmene mwachitiramo. Apa tikutanthauza kuti akawerenge nkhaniyi ndi mnzakeyo kenako n’kumufunsa mafunso othandiza kuti adziwe maganizo ake. Mwachitsanzo, angapemphe mnzakeyo kuti awerenge ndime yachiwiri pansi pa kamutu kakuti “DNA Ndiponso Ubongo wa Munthu” patsamba 23. Kenako mwanayo angafunse mnzakeyo kuti, ‘Kodi n’zoona kuti DNA imasunga zinthu zambiri kuposa zimene makompyuta angasunge?’ N’zodziwikiratu kuti mnzakeyo angayankhe kuti inde. Ndiyeno angamufunse kuti, ‘Ngati akatswiri opanga makompyuta sangakwanitse kupanga kompyuta yotha kusunga zinthu zambiri ngati mmene imachitira DNA, kodi ukuganiza kuti DNA inangokhalako popanda woipanga?’ Kuti muthandize mwana wanu kukhala wolimba mtima pokambirana ndi anzake zimene amakhulupirira, muzipeza nthawi yoyesezera. Mukamamuthandiza kuti azitha kufunsa mafunso mwaluso, mwanayo azigwira bwino ntchito yake yolalikira.
15. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso poyesa kuthandiza anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu?
15 Chitsanzo chachiwiri: Tiyerekeze kuti tili mu utumiki ndipo takumana ndi munthu amene amakayikira zoti kuli Mulungu. Mwina watiuza kuti sakhulupirira ngakhale pang’ono zoti Mulungu alipo. Sitiyenera kugwa ulesi n’kusiya kukambirana naye. Tingachite bwino kumufunsa mwaulemu kuti tidziwe zoti wakhala akukhulupirira zimenezo kwa nthawi yaitali bwanji, ndipo chinam’chititsa n’chiyani kuti ayambe kukhulupirira zimenezo. Ndiyeno mvetserani mayankho ake ndiponso muyamikireni chifukwa choti anaganizira nkhaniyo mozama. Kenako mungamufunse ngati angafune kuona umboni wosonyeza kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Ngati munthuyo akufunadi kudziwa zoona zenizeni, mwina sangakane kuona umboni woterowo. Kenako tingamuuze kuti tibweranso kuti tidzakambirane naye nkhani yosonyeza umboni umenewu. Tizikumbukira kuti mafunso abwino komanso ofunsidwa mwaluso angathandize kuti uthenga wabwino ufike munthu pa mtima.
16. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhutira ngati wophunzira amangowerenga ndendende mayankho a m’ndime?
16 Chitsanzo chachitatu: Pochititsa phunziro la Baibulo, mwina munthu amene tikuphunzira nayeyo amangowerenga ndendende mayankho amene ali m’ndime. Ngati zimenezi zitapitirira, mfundo za m’Baibulo sizingamufike pa mtima. Tikutero chifukwa chakuti munthu woteroyo saganizira mozama zimene akuyankha ndipo sangakhulupirire ndi mtima wonse zimene akuphunzirazo. Iye angakhale ngati mbewu imene sinazike mizu ndipo akhoza kufooka mosavuta akayamba kutsutsidwa kapena kuzunzidwa. (Mat. 13:20, 21) Kuti tipewe zimenezi, tiyenera kufunsa munthuyo kuti anene maganizo ake pa zimene tikuphunzira naye. Tiziyesetsa kuti tidziwe ngati akugwirizana ndi mfundo zimene tikuphunzira. Chofunika kwambiri ndi kumupempha kuti afotokoze chifukwa chake akugwirizana nazo kapena ayi. Kenako tingamuthandize kuganizira malemba ena kuti afike yekha pozindikira zoona zake za nkhaniyo. (Aheb. 5:14) Tikamagwiritsa ntchito mafunso mwaluso, tidzathandiza ophunzira kudziwa mfundo za m’Baibulo komanso kuzikhulupirira. Zikatero, iwo sangafooke ngati atakumana ndi anthu otsutsa kapena amene angafune kuwasocheretsa. (Akol. 2:6-8) Kodi tingachitenso chiyani kuti tizigwira bwino ntchito yathu yolalikira?
ALALIKI ABWINO AMATHANDIZANA
17, 18. Kodi tingatani kuti tizithandizana ndi munthu amene tikulalikira naye?
17 Yesu ankatumiza anthu awiriawiri kukalalikira. (Maliko 6:7; Luka 10:1) Nayenso Paulo anatchula ‘antchito anzake’ amene ‘anayesetsa limodzi naye pa ntchito ya uthenga wabwino.’ (Afil. 4:3) Potsatira nkhani za m’Malemba zimenezi, mu 1953, gulu linakonza pulogalamu yoti ena aziphunzitsa anzawo mu utumiki.
18 Kodi inuyo mungatani kuti muzithandizana ndi munthu amene mukulalikira naye. (Werengani 1 Akorinto 3:6-9.) Mnzanu akamawerenga Baibulo, inunso muzitsegula lanu. Muziyang’ana ndiponso kumvetsera pamene mnzanuyo kapena munthu winayo akulankhula. Muzitsatira bwino nkhani imene akukambirana kuti ngati munthuyo akutsutsa, muthe kuthandiza mnzanuyo. (Mlal. 4:12) Koma muyenera kusamala kuti musamam’dule pakamwa mnzanuyo akamafotokoza bwinobwino mfundo inayake. Mwina mungachite izi pofuna kuthandiza koma vuto ndi lakuti mukhoza kukhumudwitsa mnzanuyo komanso kusokoneza munthu winayo. Komabe nthawi zina mukhoza kulankhulapo. Koma polankhula, ndi bwino kungotchula mwachidule mfundo imodzi kapena ziwiri basi. Kenako perekani mpata kuti mnzanuyo apitirize.
19. Kodi tingachite bwino kukumbukira chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?
19 Kodi mungatani kuti muzithandizana pochoka panyumba ina kupita ina? Mukhoza kukambirana zimene mungafunike kusintha kuti muphunzitse bwino panyumba yotsatira. Koma muyenera kupewa kulankhula zinthu zokhumudwitsa zokhudza anthu a m’dera lanu. Muzipewanso kulankhula zimene Akhristu anzanu amalakwitsa. (Miy. 18:24) Tingachite bwino kukumbukira kuti tili ngati zonyamulira zoumbidwa ndi dothi. Koma Yehova watikomera mtima kwambiri potipatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino. (Werengani 2 Akorinto 4:1, 7.) Choncho tiyeni tonse tiziyamikira mwayi umenewu n’kumayesetsa kugwira bwino ntchito yathu yolalikira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Ngati munthu amene mukulankhula naye akudziwa Chingelezi, mukhoza kugwiritsa ntchito timabuku takuti Was Life Created? ndi The Origin of Life—Five Questions Worth Asking.