Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anawateteza Pamene Ankazemba M’mapiri

Yehova Anawateteza Pamene Ankazemba M’mapiri

MAYI wina atatuluka m’nyumba m’mawa anapeza pakhomo pali kenakake koma sanaone munthu aliyense amene anasiyapo. Anazindikira kuti kanthuko kayenera kuti kasiyidwapo usiku. Ndiyeno atatola n’kutsegula anaona kuti ndi mabuku ofotokoza Baibulo amene pa nthawiyo anali oletsedwa. Choncho analowa nawo m’nyumba mwamsanga. Mayiyu anayamikira kwambiri n’kuyamba kuthokoza Yehova kuti wamuthandiza kupeza zinthu zofunika kwambiri zimenezi.

Zoterezi zinkachitikachitika ku Germany m’ma 1930. Hitler ndi chipani cha Nazi atayamba kulamulira mu 1933, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa m’madera ambiri a dziko la Germany. M’bale Richard Rudolph, * yemwe pano ali ndi zaka zoposa 100, anati: “Tinkadziwiratu kuti ntchito yolengeza za Yehova ndi dzina lake singaime chifukwa cha lamulo la munthu. Mabuku athu ndi amene ankatithandiza pophunzira Baibulo komanso kulalikira. Koma ntchito yathu italetsedwa, mabukuwa ankasowa kwambiri. Tinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ntchito yathuyi ipitirira bwanji?’” Ndiyeno Richard anatulukira njira ina yothandizira anthu kuti azipeza mabuku. Anaona kuti akhoza kuzembetsa mabukuwo kudzera m’mapiri.—Ower. 9:36.

ANKADUTSA M’TINJIRA TA M’MAPIRI

Ngati munthu akutsatira mtsinje wa Elbe (kapena kuti Labe) kulowera kumtunda angafike kumapiri otchedwa Giant (kapena kuti Krkonoše). Mapiriwa ali m’malire a dziko la Czech Republic ndi la Poland ndipo ndi aatali mamita 1,600 okha koma kumazizira kwambiri. Kwa miyezi 6 pa chaka kumakhala chipale chofewa chofika mamita atatu kupita m’mwamba. Nthawi zina kumachita nkhungu kwambiri moti anthu sangaone patali.

Kwa zaka zambirimbiri, mapiri amenewa akhala ngati malire pakati pa mayiko. M’mbuyomu, apolisi ankavutika kuyenda m’mapiriwa choncho anthu ozembetsa katundu ankadutsa kumeneko. M’ma 1930, pamene mapiriwa anali malire a  dziko la Czechoslovakia ndi la Germany, a Mboni za Yehova akhama anayamba kudutsanso m’tinjira ta anthu ozembetsa katundu. Ankachita zimenezi kuti azembetse mabuku ofotokoza Baibulo kuchokera m’mayiko ena. Richard anali m’gulu lochita zimenezi.

Abale ndi alongo ankavala ngati anthu okangoona malo kuti azembetse mabuku m’mapiri

MAULENDO OOPSA

Richard anati: “Loweruka ndi Lamlungu tinkauyamba ulendo wakumapiri titavala ngati anthu ongokaona malo. Tinkakhala achinyamata angapo mwina 7. Tikanyamuka ku Germany, tinkayenda maola atatu kuti tidutse mapiriwa n’kufika kumalo ena a ku Czechoslovakia ndipo unali ulendo wa makilomita 16 ndi hafu. Pa nthawiyo, anthu ambiri a ku Germany ankakhala kumalo amenewa. Munthu wina anali mlimi ndipo anavomera kuthandiza abale athu. Iye anali ndi ngolo imene anthu okaona malo ankakwera. Ndiyeno abale ku Prague ankatumiza makatoni a mabuku pa sitima. Makatoniwa ankafikira m’tauni ina, ndipo munthuyo ankawanyamula kumeneko n’kupita nawo kufamu yake. Iye ankawabisa pansi pa zakudya za ziweto ndipo abale ankabwera kudzawatenga n’kupita nawo ku Germany.

Richard anapitiriza kuti: “Tikafika kufamuyo tinkaika mabukuwo m’zikwama zikuluzikulu zoberekera zomwe zinali zolimba kwambiri. Aliyense ankanyamula katundu wolemera pafupifupi makilogalamu 50.” Kuti asagwidwe, ankanyamuka dzuwa litalowa kuti akafike dzuwa lisanatuluke. M’bale Ernst Wiesner, yemwe pa nthawiyo anali woyang’anira dera ku Germany, anafotokoza zimene abalewa ankachita. Anati: “Abale awiri ankakhala patsogolo mwina pa mtunda wa mamita 100 ndipo akakumana ndi munthu ankayatsa matochi awo. Zikatero abale amene ankabwera ndi zikwama ankalowa m’tchire n’kubisala. Sankatulukamo mpaka abale awiriwo atabweranso n’kutchula mawu enaake. Mawu otchulidwawo ankasinthidwa mlungu uliwonse.” Koma maulendowo anali oopsa pa zifukwa zinanso.

Richard anati: “Tsiku lina ndinaweruka mochedwa kuntchito choncho ndinanyamuka anzanga atapita kale. Kunali mdima komanso nkhungu ndipo ndinkayenda pa mvula yozizira koopsa. Ndinasochera m’nkhalango ndipo ndinakhala ndikufufuza  njira kwa maola ambiri. Anthu ambiri oyenda m’mapiri ankafa zoterezi zikachitika. Ndiyeno anzangawo ndinakumana nawo chakum’mawa akubwerera.”

Ulendo wodutsa m’mapiri a Giant unali woopsa chifukwa kunkakhala chipale chofewa chambiri

Abale olimba mtimawa ankayenda ulendo wam’mapiriwu mlungu uliwonse kwa zaka pafupifupi zitatu. M’nyengo yozizira, abalewa ankayenda ndi katunduyu pogwiritsa ntchito zipangizo zoyendera pa chipale chofewa. Nthawi zina abale ambiri, mwina okwana 20, ankayenda masana kudzera m’tinjira ta anthu okaona malo. Kuti anthu asawakayikire, ankapita ndi alongo omwe. Ena ankakhala patsogolo ndipo akaona anthu okayikitsa, ankaponya zipewa m’mwamba kuti enawo adziwe zochita.

Kodi chinkachitika n’chiyani anthuwo akafika ku Germany? Pankakhala dongosolo loti mabukuwo azikaperekedwa kwa abale nthawi yomweyo. Ndiye ankapereka bwanji? Ankapakira m’makatoni ngati sopo n’kukakweza sitima ku Hirschberg. Makatoniwo ankatumizidwa m’madera osiyanasiyana m’dzikolo ndipo abale ndi alongo ena ankanyamula mochenjera n’kumakapereka kwa Akhristu anzawo usiku ngati mmene tafotokozera kumayambiriro kuja. Abale amene ankathandiza pa ntchito yozembetsayi ankachita zinthu mogwirizana kwambiri moti ngati mmodzi atangogwidwa ndiye kuti zinthu zikanasokonekera kwambiri. Koma tsiku lina zinthu zinaipa mosayembekezereka.

Mu 1936, anthu ena anatulukira mabuku athu pamalo ena pafupi ndi mzinda wa Berlin. Pa zinthu zimene anapeza panalinso katundu wochokera ku Hirschberg koma munthu amene anatumiza katunduyo sanadziwike. Apolisi anaona zimene zinalembedwa pakatunduyo n’kufufuza munthu amene amalemba choncho. Ndipo m’bale amene ankachita zambiri pa ntchito yozembetsa mabuku anamangidwa. Kenako Richard Rudolph limodzi ndi m’bale wina anamangidwanso. Abale omangidwawo anavomereza kuti iwowo ndi amene ankagwira ntchito yonse yozembetsa mabuku. Choncho abale ena otsalawo anatha kupitiriza ntchito yoopsayi.

KODI TIKUPHUNZIRAPO CHIYANI?

A Mboni ku Germany ankadalira kwambiri mabuku ofotokoza Baibulo amene anthu ankawazembetsa m’mapiriwo. Koma sikuti ankangowazembetsa m’mapiriwo basi. Ankalowetsanso mabuku mu Germany kuchokera ku Czechoslovakia pogwiritsa ntchito njira zina mpaka mu 1939 pamene asilikali a ku Germany analowa m’dzikolo. A Mboni ochokera kumayiko enanso a pafupi ndi Germany monga France, Netherlands ndi Switzerland ankaikanso moyo wawo pa ngozi. Iwo ankachita zimenezi pofuna kuthandiza abale awo amene ankazunzidwa kuti apeze mabuku.

Masiku ano, ambirife tingapeze mabuku ofotokoza Baibulo okwanira m’njira zosiyanasiyana. Tikhoza kupeza mabuku atsopano ku Nyumba ya Ufumu kapena kukopera pa webusaiti ya jw.org. Koma kaya tipeza bwanji mabukuwo ndi bwino kuganizira zonse zimene zinachitika kuti apezeke. N’zoona kuti sanachite kuwazembetsa m’mapiri ozizira usiku koma Akhristu anzathu anagwira ntchito modzipereka kwambiri kuti tipeze mabukuwo.

^ ndime 3 Anatumikira mumpingo wa mumzinda wa Hirschberg, kudera la Silesia. Panopa mzindawu umatchedwa Jelenia Góra ndipo uli kum’mwera chakumadzulo kwa Poland.