Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?

N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?

“Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—1 AKOR. 11:24.

1, 2. Kodi Yesu anachita chiyani usiku wa pa Nisani 14 mu 33 C.E.? (Onani chithunzi pamwambapa.)

USIKU wa pa Nisani 14 mu 33 C.E. mwezi wathunthu unkaoneka ku Yerusalemu. Pa nthawiyo, Yesu ndi atumwi ake anachita Pasika pokumbukira kuti Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo zaka zoposa 1,500 zapitazo. Kenako anayambitsa mwambo wapadera ndi atumwi ake 11 okhulupirika. Mwambowu unali wokumbukira imfa yake ndipo anauza ophunzira ake kuti aziuchita chaka chilichonse. *Mat. 26:1, 2.

2 Poyambitsa mwambowu, Yesu anapemphera n’kupatsa ophunzira ake mkate wopanda zofufumitsa ndipo ananena kuti: “Eni, idyani.” Kenako anatenga kapu n’kuyamikanso ndipo anati: “Imwani nonsenu.” (Mat. 26:26, 27) Atapatsa ophunzira ake zizindikiro zapaderazi, Yesu anawauza zinthu zambiri zofunika.

3. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?

3 Izi ndi zimene Yesu anachita poyambitsa mwambo wokumbukira imfa yake. Mwambowu umatchedwanso kuti “chakudya chamadzulo cha Ambuye.” (1 Akor. 11:20) Koma anthu ena akhoza kufunsa kuti: N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira imfa ya Yesu? Kodi mkate ndi vinyo zimaimira chiyani? Kodi tingakonzekere bwanji mwambowu? Kodi ndani ayenera kudya zizindikirozi? Nanga kodi Akhristu amasonyeza bwanji kuti amayamikira madalitso amene akuyembekezera?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAKUMBUKIRA IMFA YA YESU?

4. Kodi imfa ya Yesu yatithandiza bwanji?

4 Anthufe tinatengera uchimo ndi imfa kwa Adamu. (Aroma 5:12) Popeza munthu aliyense ndi wochimwa, palibe amene angadziwombole kapena kuwombola anzake. (Sal. 49:6-9) Koma Yesu anali wangwiro, choncho imfa yake inali dipo loyenerera lowombolera anthu. Iye atapita kumwamba, anapereka kwa Mulungu nsembe imene ingatimasule ku uchimo ndi imfa. Zimenezi zinatipatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.—Aroma 6:23; 1 Akor. 15:21, 22.

5. (a) Kodi Yehova ndi Yesu asonyeza bwanji kuti amatikonda? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu?

5 Zimene Mulungu anachita popereka dipo zimasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. (Yoh. 3:16) Nayenso Yesu anasonyeza kuti amatikonda pololera kupereka moyo wake. Baibulo limasonyeza kuti Yesu asanabwere padzikoli anali “mmisiri waluso” wa Mulungu ndipo ‘ankasangalala kwambiri ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:30, 31) Tiyenera kupezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu posonyeza kuti timayamikira Yehova ndi Mwana wake. Paja Yesu anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—1 Akor. 11:23-25.

KODI MKATE NDI VINYO ZIMAIMIRA CHIYANI?

6. Kodi Yesu ananena chiyani popereka mkate ndi vinyo?

6 Pamene Yesu ankayambitsa mwambowu, sanasinthe mkate ndi vinyo kukhala thupi lake lenileni kapena magazi ake enieni. Koma ananena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa.” Ananenanso kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a pangano,’ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri.” (Maliko 14:22-24) Choncho mkate ndi vinyo ndi zizindikiro basi.

7. Kodi mkate wa pa Chikumbutso umaimira chiyani?

7 Pa mwambowu mu 33 C.E., Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda zofufumitsa umene unatsala atachita Pasika. (Eks. 12:8) M’Malemba, nthawi zina zofufumitsa zimaimira uchimo. (Mat. 16:6, 11, 12; Luka 12:1) Choncho mkate wopanda zofufumitsa umaimira thupi la Yesu lopanda uchimo. (Aheb. 7:26) Ndiyeno mkate woterewu ndi umene timagwiritsa ntchito pa Chikumbutso.

8. Kodi vinyo wa pa Chikumbutso amaimira chiyani?

8 Vinyo amene Yesu anagwiritsa ntchito pa Nisani 14 mu 33 C.E., komanso amene timagwiritsa ntchito masiku ano, amaimira magazi a Yesu. Iye anaphedwa kunja kwa Yerusalemu pamalo otchedwa Gologota ‘kuti machimo athu akhululukidwe.’ (Mat. 26:28; 27:33) Choncho mkate ndi vinyo zimaimira nsembe yamtengo wapatali kwambiri ya Yesu yomwe anaipereka pofuna kupulumutsa anthu omvera. Popeza timayamikira kwambiri nsembeyi, chaka chilichonse tiyenera kukonzekera bwino mwambo wa Chikumbutso.

ZIMENE TINGACHITE POKONZEKERA

9. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira ndandanda yowerenga Baibulo pokonzekera Chikumbutso? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za dipo?

9 M’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku muli ndandanda ya kuwerenga Baibulo pokonzekera Chikumbutso. Kutsatira ndandandayi kungatithandize kuti tiganizire zimene Yesu anachita atatsala pang’ono kuphedwa. Izi zingatithandize kukonzekeretsa mitima yathu. * Mlongo wina analemba kuti: “Timachita kulakalaka nthawi ya Chikumbutso. Ndimaona kuti Chikumbutso chilichonse ndi chapadera kuposa chimene ndinapanga kale. Ndikukumbukira kuti bambo anga atamwalira . . . , ndinayang’ana thupi lawo n’kuyamba kuganizira kufunika kwa dipo. . . . Ndinkadziwa malemba onse okhudza dipo komanso ndinkatha kuwafotokoza bwino. Koma izi zitachitika ndinaganizira madalitso amene tidzalandire chifukwa cha dipo ndipo ndinayamba kumva bwino mumtima.” Choncho pokonzekera Chikumbutso, tiyenera kuganizira mmene nsembe ya Yesu imatimasulira ku uchimo ndi imfa.

Gwiritsani ntchito bwino mabuku athu pokonzekeretsa mtima wanu musanapite ku Chikumbutso (Onani ndime 9)

10. Fotokozani zinthu zina zimene tingachite pokonzekera Chikumbutso.

10 Kuwonjezera nthawi yolalikira kungatithandizenso kukonzekera Chikumbutso. Ngati n’kotheka mwina tingachite upainiya wothandiza. Pa nyengoyi, timaitanira anthu ku mwambo umenewu. Izi zimatipatsa mpata wouza anthu za Yehova ndi Mwana wake. Timawauzanso madalitso amene Yehova adzapereke kwa anthu amene amamumvera ndiponso kumulemekeza.—Sal. 148:12, 13.

11. Kodi ku Korinto kunali vuto liti?

11 Pokonzekera mwambowu, ndi bwino kuganizira zimene Paulo anauza Akhristu a mumpingo wa Korinto. (Werengani 1 Akorinto 11:27-34.) Iye ananena kuti aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za m’kapuyi mosayenerera “adzakhala ndi mlandu wokhudza thupi ndi magazi a Ambuye” Yesu Khristu. Choncho odzozedwa asanadye zizindikiro ayenera ‘kudzifufuza kuti aone ngati ali oyenerera.’ Ngati atadya mosayenerera ndiye kuti ‘akudya ndi kumwa chilango chawo’ kapena kuti adzaweruzidwa. Akhristu ena ku Korinto sankachita bwino ndipo izi zinachititsa kuti akhale ‘ofooka ndi odwaladwala ndipo angapo anafa’ mwauzimu. N’kutheka kuti ena ankadya ndiponso kumwa kwambiri asanapite ku Chikumbutso kapena pa mwambo weniweniwo moti ankalephera kuchita zinthu mozindikira. Iwo ankadya zizindikirozo mosayenerera ndipo Mulungu sanasangalale nazo.

12. (a) Kodi Paulo anayerekezera mwambo wa Chikumbutso ndi chiyani? (b) Kodi Paulo anapereka chenjezo liti? (c) Kodi munthu amene amadya zizindikiro ayenera kutani ngati wachita tchimo lalikulu?

12 Paulo anayerekezera mwambowu ndi chakudya chodyera limodzi. Iye anauza Akhristu amene ankadya kuti: “Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.” (1 Akor. 10:16-21) Ngati munthu amene amadya zizindikiro wachita tchimo lalikulu, ayenera kupempha thandizo. (Werengani Yakobo 5:14-16.) Ndiyeno ngati Mkhristu wotereyu ‘atasonyeza kuti walapa’ sakunyoza nsembe ya Yesu ngati atadya zizindikiro pa Chikumbutso.—Luka 3:8.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera komanso kuganizira chiyembekezo chathu?

13 Pamene tikukonzekera Chikumbutso, tiyenera kupemphera ndiponso kuganizira mofatsa chiyembekezo chathu. Si bwino kuchita zinthu zimene zinganyozetse nsembe ya Yesu. Mwachitsanzo, sitiyenera kudya nawo zizindikiro pamene tilibe umboni weniweni wakuti tadzozedwa. Koma kodi munthu angadziwe bwanji ngati ali woyenera kudya zizindikiro?

KODI NDANI AYENERA KUDYA ZIZINDIKIRO?

14. Popeza odzozedwa ali m’pangano latsopano, kodi amachita chiyani pa Chikumbutso?

14 Anthu amene amadya zizindikiro sakayikira ngakhale pang’ono zoti ali m’pangano latsopano. Ponena za vinyo, Yesu anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga.” (1 Akor. 11:25) Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova ananena kuti adzachita pangano latsopano losiyana ndi pangano la Chilamulo limene anachita ndi Aisiraeli. (Werengani Yeremiya 31:31-34.) Yehova wachita pangano latsopanoli ndi Aisiraeli auzimu. (Agal. 6:15, 16) Imfa ya Khristu inachititsa kuti panganoli liyambe kugwira ntchito. (Luka 22:20) Yesu ndi mkhalapakati wa pangano latsopano ndipo odzozedwa okhulupirika amene ali m’panganoli amakakhala ndi Yesu kumwamba.—Aheb. 8:6; 9:15.

15. (a) Kodi ndani ali m’pangano la Ufumu? (b) Kodi iwo akuyembekezera mwayi uti?

15 Akhristu odzozedwa amadziwanso kuti ali m’pangano la Ufumu. (Werengani Luka 12:32.) Yesu anachita panganoli ndi ophunzira ake okhulupirika, omwe anadzadzozedwa. Iwo ndi amene ‘anagawana naye m’masautso ake.’ (Afil. 3:10) Popeza odzozedwa okhulupirika ali m’pangano la Ufumu, adzakalamulira ndi Khristu kumwamba mpaka muyaya. (Chiv. 22:5) Anthuwa ndi oyenerera kudya zizindikiro pa Chikumbutso.

16. Fotokozani mwachidule zimene lemba la Aroma 8:15-17 limatanthauza.

16 Anthu odzozedwa sakayikira zoti ndi ana a Mulungu. Iwo okha ndi amene ayenera kudya zizindikiro pa Chikumbutso. (Werengani Aroma 8:15-17.) Paulo ananena kuti anthu amenewa amafuula kuti: “Abba, Atate!” Mawu achiaramu akuti “Abba” ndi aulemu komanso osonyeza kukonda bambo ako. Mawuwa amasonyeza kuti anthu akadzozedwa amakhala pa ubale wapadera ndi Yehova chifukwa chakuti amakhala ana ake. Mzimu wa Mulungu ‘umawachitira umboni’ kuti iwo ndi ana ake odzozedwa ndipo sakayikira zimenezi ngakhale pang’ono. Sikuti anthuwo amangotopa ndi moyo wapadzikoli n’kumafuna kupita kumwamba. Amadziwa kuti akakhalabe okhulupirika, adzalamulira limodzi ndi Yesu kumwambako. M’gulu limeneli muli anthu 144,000 amene ‘adzozedwa ndi woyerayo.’ Panopa, anthuwa angotsala ochepa kwambiri padzikoli. (1 Yoh. 2:20; Chiv. 14:1) Iwo amakhala pa ubwenzi wapadera ndi Yehova moti amamutchula kuti: “Abba, Atate!”

TIMAYAMIKIRA KWAMBIRI MADALITSO AMENE TIKUYEMBEKEZERA

17. Kodi Akhristu odzozedwa akuyembekezera chiyani ndipo amaona bwanji mwayi umenewu?

17 Ngati ndinu wodzozedwa, muyenera kuti mukamapemphera panokha mumatchula mwayi wanu wokalamulira kumwamba. Mukamva malemba onena za opita kumwamba mumadziwiratu kuti akunena za inuyo. Mwachitsanzo, mumadziwa kuti muli m’gulu la anthu amene ‘alonjezedwa ukwati’ ndi Yesu Khristu ndipo mumayembekezera zimenezi kwambiri. (2 Akor. 11:2; Yoh. 3:27-29; Chiv. 21:2, 9-14) Mukawerenga m’Baibulo mawu a Mulungu osonyeza kuti amakonda ana ake auzimu, mumadziwa kuti akulankhula za inuyo. Mukawerenganso malangizo a Yehova opita kwa ana ake odzozedwa, mumamvera podziwa kuti akukuuzaninso inuyo. Mzimu wa Mulungu ‘umachitira umboni limodzi ndi mzimu wanu’ kuti mudzapita kumwamba.

18. Kodi a “nkhosa zina” akuyembekezera chiyani ndipo amaona bwanji mwayiwu?

18 Koma ngati muli m’gulu la “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” ndiye kuti Mulungu wakupatsani mwayi wodzakhala padziko lapansi. (Chiv. 7:9; Yoh. 10:16) Choncho mumafunitsitsa kukhala m’Paradaiso ndipo mumakonda kuganizira madalitso apadzikoli amene Baibulo limafotokoza. Mumayembekezera kudzakhala padzikoli mwamtendere limodzi ndi achibale anu komanso anthu ena olungama. Mumalakalaka nthawi imene njala, matenda, imfa komanso mavuto ena sadzakhalaponso. (Sal. 37:10, 11, 29; 67:6; 72:7, 16; Yes. 33:24) Mumafunitsitsa kudzaonananso ndi anzanu amene anamwalira. (Yoh. 5:28, 29) Muyenera kuti mumayamikira kwambiri mwayi umene Yehova wakupatsani wodzakhala padziko lapansi. Ngakhale kuti simudya zizindikiro, mumapezeka pa Chikumbutso chifukwa choyamikira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.

KODI MUDZAPEZEKA PA MWAMBOWU?

19, 20. (a) Kodi muyenera kutani kuti mudzalandire madalitso amene mukuyembekezera? (b) N’chifukwa chiyani mudzapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu?

19 Kuti mudzalandire madalitso amene mukuyembekezera, muyenera kukhulupirira Yehova, Yesu Khristu komanso dipo. Kupezeka pa Chikumbutso kudzakuthandizani kuganizira kwambiri madalitsowo komanso kufunika kwa nsembe ya Yesu. Choncho yesetsani kuti mudzapezeke pa mwambo umenewu. Mwambowu udzachitika Lachisanu, pa April 3, 2015 dzuwa litalowa, ku Nyumba za Ufumu kapena malo ena amene angasankhidwe.

20 Kupezeka pa mwambowu kudzakuchititsani kuyamikira kwambiri nsembe ya dipo ya Yesu. Ndi bwino kumvetsera mwatcheru nkhani imene idzakambidwe. Zimenezi zidzakulimbikitsani kuti muuze anthu ena mfundo zokhudza chikondi cha Yehova komanso cholinga chake padzikoli. (Mat. 22:34-40) Choncho musadzalephere kupezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu zivute zitani.

^ ndime 1 Yesu anaphedwa tsiku lomwelo la Nisani 14. Aheberi ankaona kuti tsiku limayamba dzuwa litalowa n’kutha dzuwa likadzalowanso.

^ ndime 9 Onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, mutu 16.