Kodi Tizingokhulupirira Zinthu Zooneka Basi?
Kodi Tizingokhulupirira Zinthu Zooneka Basi?
Anthu ena amaganiza kuti “n’zosatheka kudziwa zoona zenizeni pankhani zina monga zokhudza Mulungu komanso moyo wa m’tsogolo, ngakhale kuti zimenezi ndi nkhani zimene zipembedzo zachikhristu ndiponso zipembedzo zina zimaona kuti n’zofunika kwambiri. Ndipo anthu omwe amaganiza kuti n’zosathekawa amati ngati zingadzatheke mwina ndi m’tsogolo, osati panopa.”—ANATERO BERTRAND RUSSELL, MU 1953.
MUNTHU wina amene anafotokozapo za anthu a maganizo okayikirawa ndi Thomas Huxley yemwe anali katswiri wa maphunziro a nyama zakutchire. Iye anabadwa mu 1825 ndipo anakhalapo m’nthawi ya Charles Darwin, komanso ankagwirizana ndi maganizo akuti anthufe tinachita kusanduka kuchokera ku zinyama. Mu 1863, Huxley analemba kuti sanali kuona umboni ulionse woti kuli Mulungu amene “amatikonda ndiponso kutisamalira monga m’mene Akhristu amaphunzitsira.”
Anthu ambiri angagwirizane ndi maganizo a anthu otchukawa ndipo anganene kuti angakhulupirire zinthu zooneka basi. Iwo anganenenso kuti kukhulupirira munthu kapena chinthu popanda umboni wosonyeza kuti chinthucho chilipo n’kupanda nzeru.
Kodi Baibulo limatiuza kuti tizingokhulupirira Mulungu popanda umboni ulionse wosonyeza kuti iye alipo? Ayi si choncho. Baibulo limasonyeza kuti n’kupanda nzeru, kapenanso kupusa kumene, kukhulupirira zinthu zimene zilibe umboni. Ndipo limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.
Nanga bwanji pankhani yokhulupirira kuti kuli Mulungu? Kodi pali umboni ulionse wosonyeza kuti kuli Mulungu yemwe amatikonda ndiponso kutisamalira?
Makhalidwe a Mulungu Akuonekera
Polankhula ndi anthu ophunzira kwambiri a ku Atene, Paulo, yemwe analemba nawo Baibulo, ananena kuti Mulungu ndi “amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu.” Ndipo iye anauzanso anthuwo, omwe ankakayikira zoti kuli Mulungu, kuti Mulunguyo amasamalira anthu ndiponso “sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:24-27.
N’chifukwa chiyani Paulo ankakhulupirira kuti Mulungu alipo ndiponso kuti amasamalira anthu? M’kalata imene analembera Akhristu a ku Roma iye anafotokoza chifukwa chimodzi. Ponena za Mulungu, iye anati: “Chilengedwere dziko kumka m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe . . . m’zinthu zimene anapanga.”—Aroma 1:20.
Nkhani zotsatirazi zifotokoza makhalidwe atatu a Mulungu amene tingathe kuwaona bwino m’zinthu zimene analenga. Powerenga nkhani zimenezi dzifunseni kuti, ‘Kodi kuphunzira za makhalidwe atatu a Mulungu amenewa kukundithandiza bwanji?’
[Mawu Otsindika patsamba 3]
Baibulo silitiuza kuti tizingokhulupirira Mulungu popanda umboni ulionse wosonyeza kuti iye alipo