Zokhudza Ufumu wa Mulungu
Zimene Tikuphunzira kwa Yesu
Zokhudza Ufumu wa Mulungu
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
Ufumu wa Mulungu ndi boma limene lidzalamulira dziko lonse lapansi. Yesu anati: “Inu muzipemphera motere: . . . ‘Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.’”—Mateyo 6:9, 10; Danieli 2:44.
Kodi ndani amene adzakhala olamulira mu Ufumu wa Mulungu?
Yesu anabadwa kuti adzakhale Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. Mngelo anauza mayi a Yesu kuti: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu.” (Luka 1:30-33) Komanso Yesu anasankha ena mwa otsatira ake kuti adzalamulire naye limodzi. Iye anauza atumwi ake kuti: “Inu ndinu amene mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga. Choncho ndikuchita nanu chipangano, mmene Atate wanga wachitira chipangano cha ufumu ndi ine.” (Luka 22:28, 29; Danieli 7:27) Otsatira a Yesu okwana 144,000 adzalamulira naye limodzi.—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1.
Kodi boma limeneli lidzakhala kuti?
Ufumu wa Mulungu udzalamulira kuchokera kumwamba. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndikapita kukakukonzerani malo [kumwamba], ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko. . . . Ine ndikupita kwa Atate.”—Yohane 14:2, 3, 12; Danieli 7:13, 14.
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani ndi zinthu zoipa?
Yesu adzawononga anthu oipa onse padziko lapansili. Iye anati: “Mwana wa munthu [Yesu] akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake, Mateyo 25:31-34, 46.
pamenepo adzakhala pa mpando wake wachifumu waulemerero. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye, ndipo adzalekanitsa anthu . . . Ndipo [oipa] adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama kumoyo wosatha.”—Kodi ndani amene adzalamuliridwa ndi Ufumu umenewu padziko lapansi?
Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5; Salmo 37:29; 72:8) Padziko lonse lapansi padzakhala anthu okhawo amene panopa akuyesetsa kukonda anzawo. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.”—Yohane 13:34, 35.
Kodi Ufumu wa Mulungu udzawachitira chiyani anthu padziko lapansili?
Yesu adzathetsa matenda onse. Pamene anali padziko lapansili, Yesu anauza anthu ambiri “za ufumu wa Mulungu, ndipo anachiritsa amene anafunikira kuchiritsidwa.” (Luka 9:11) Mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza Yesu ataukitsidwa. Iye ananena kuti: “Ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. . . . Kenako, ndinamva mawu ofuula kuchokera ku mpando wachifumu, akuti: ‘Taonani! chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.’”—Chivumbulutso 21:1-4.
Ufumu wa Mulungu udzabwezeretsa paradaiso padziko lapansi. Ndipotu, munthu wochita zoipa amene anapachikidwa pamodzi ndi Yesu anati: “‘Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.’ Ndipo Yesu anati kwa iye: ‘Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala nane m’Paradaiso.’”—Luka 23:42, 43; Yesaya 11:4-9.
Kuti mumve zambiri, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * pamutu 8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 16 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.