Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Umboni Waukulu Wakuti Mulungu Amatikonda

Umboni Waukulu Wakuti Mulungu Amatikonda

Yandikirani Mulungu

Umboni Waukulu Wakuti Mulungu Amatikonda

Genesis 22:1-18

ABULAHAMU ankakonda Mulungu. Kholo lokhulupirika limeneli linkakondanso mwana wake Isake, mwana amene anabala atakalamba. Koma Isake ali ndi zaka pafupifupi 25, Abulahamu anayesedwa pomupempha kuchita zimene bambo sangachite mwachibadwa. Mulungu anamupempha kupereka nsembe mwana wake. Komabe, Isake sanaphedwe. Abulahamu atangotsala pang’ono kupha mwana wake, Mulungu anatumiza mngelo kudzamuletsa. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi, yopezeka pa Genesis 22:1-18, imalosera za chikondi chachikulu chimene Mulungu ali nacho pa ife.

Vesi 1 limanena kuti: “Mulungu anamuyesa Abulahamu.” Abulahamu anali wokhulupirika koma apa chikhulupiriro chake chinayesedwa kuposa kale lonse. Mulungu anati: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, . . . num’pereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.” (Vesi 2) Kumbukirani kuti Mulungu salola atumiki ake kuti ayesedwe kufika pamene sangapirire. Choncho kuyesedwa kwa Abulahamu kunasonyeza kuti Mulungu anali kumudalira.​—1 Akorinto 10:13.

Abulahamu anamvera nthawi yomweyo. Baibulo limati: “Abrahamu analawira m’mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isake mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe, nauka, nanka.” (Vesi 3) Zikuoneka kuti Abulahamu sanauze aliyense zimene anauzidwa kuchitazi.

Iwo anayenda ulendo wa masiku atatu ndipo zimenezi zinamupatsa mpata wokwanira woti aganizire mofatsa nkhaniyi. Komabe Abulahamu sanasinthe maganizo ake. Zimene ananena zimasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Ataona phiri limene Mulungu anamuuza kukaperekera nsembeyo, anauza anyamata ake kuti: “Khalani kuno . . . , ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.” Isake atafunsa kuti nkhosa yoti apereke nsembeyo ili kuti, Abulahamu anati: “Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa.” (Vesi 58) Abulahamu ankayembekezera kuti abwerera ndi mwana wakeyo. N’chifukwa chiyani amaganiza choncho? Chifukwa “anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu yomuukitsadi [Isake] kwa akufa.”​—Aheberi 11:19.

Ali paphiripo, Abulahamu anatenga “mpeni kuti amuphe mwana wake” koma mngelo anamuletsa. Kenako Mulungu anapereka nkhosa yamphongo yomwe inakodwa mu ziyangoyango imene Abulahamu anapereka nsembe “m’malo mwa mwana wake.” (Vesi 10-13) Kwa Mulungu zinali ngati kuti Isake waperekedwa kale nsembe. (Aheberi 11:17) Katswiri wina wa Baibulo anati: “Kwa Mulungu, kufunitsitsa kwa Abulahamu kupereka mwana wake nsembe kunali kofanana ndi kum’perekadi nsembe mwanayo.”

Mpake kuti Yehova anadalira Abulahamu. Ndipo iye anadalitsidwa chifukwa chodalira Yehova. Mulungu anabwereza komanso anawonjezera zimene anapangana ndi Abulahamu. M’pangano limeneli, Mulungu analonjeza kuti adzadalitsa anthu a mitundu yonse.​—Vesi 15-18.

Pamapeto pake Mulungu analetsa Abulahamu kupereka nsembe mwana wake koma patapita nthawi, Mulungu iyemwini anaperekadi mwana Wake nsembe. Kufunitsitsa kwa Abulahamu kupereka nsembe Isake kunaimira zimene Mulungu anachita popereka mwana wobadwa yekha, Yesu, chifukwa cha machimo athu. (Yohane 3:16) Nsembe ya Khristu ndi umboni waukulu wakuti Yehova amatikonda. Popeza Mulungu anatiperekera nsembe imeneyi ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wofunitsitsa kudzimana chiyani kuti ndisangalatse Mulungu?’