Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Yosiya Anachita Zabwino

Yosiya Anachita Zabwino

KODI ukuganiza kuti kuchita zabwino n’kovuta? *​— Ngati ukuti inde, anthu ambiri amaganizanso choncho. Anthu akuluakulu nawonso amavutika kuchita zabwino. Tiye tione chifukwa chake Yosiya anavutika kwambiri kuchita zabwino. Koma kodi ukudziwa kuti Yosiya anali ndani?​—

Yosiya anali mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, amene anabadwa bambo ake ali ndi zaka 16 zokha. Amoni anali munthu woipa kwambiri ngati bambo ake, Mfumu Manase. Ndipotu Manase anali wolamulira woipa kwambiri kwanthawi yaitali. Koma nthawi ina anagwidwa ndi Asuri n’kukaikidwa ku ndende kutali kwambiri, ku Babulo. Ali mu ndende, Manase anapempha Yehova kuti amukhululukire ndipo Yehova anakhululuka.

Atatuluka ku ndende, Manase anabwerera ku Yerusalemu ndipo anakhalanso mfumu. Nthawi yomweyo anayamba kukonza zinthu zoipa zimene anachita ndipo anathandiza anthu kuyamba kutumikira Yehova. Ziyenera kuti zinamukhudza kwambiri poona kuti mwana wake Amoni sanatsatire chitsanzo chake chabwino. Ndipo Yosiya anabadwa panthawi imeneyi. Baibulo silinena ngati Manase ankacheza kwambiri ndi mdzukulu wake Yosiya. Koma kodi ukuganiza kuti Manase anam’thandiza Yosiya kutumikira Yehova?​—

Manase anamwalira Yosiya ali ndi zaka 6 zokha, ndipo bambo ake, Amoni, anakhala mfumu. Amoni analamulira zaka ziwiri zokha ndipo anaphedwa ndi anyamata ake. Choncho Yosiya anakhala mfumu ya Yuda ali ndi zaka 8. (2 Mbiri, chaputala 33) Kodi ukuganiza kuti kenako chinachitika n’chiyani? Kodi Yosiya anasankha kutsatira chitsanzo choipa cha bambo ake, a Amoni, kapena anasankha kutsatira chitsanzo chabwino cha agogo ake, a Manase, amene analapawo?​—

Ngakhale kuti Yosiya anali mwana, ankadziwa kuti ayenera kutumikira Yehova. Choncho ankamvera anthu okonda Yehova, osati anthu amene anali anzawo a bambo ake. Yosiya anali ndi zaka 8 zokha, koma ankadziwa kuti ndi bwino kumvera anthu amene amakonda Mulungu. (2 Mbiri 34:1, 2) Kodi ukufuna kuwadziwa ena mwa anthu amene ankalangiza Yosiya, komanso kumusonyeza chitsanzo chabwino?​—

Mmodzi mwa anthu amene ankasonyeza chitsanzo chabwino kwa Yosiya anali mneneri Zefaniya. Iye anali mbale wake wa Yosiya, popeza ayenera kuti anali mbadwa ya abambo ake a Manase, amene anali mfumu yabwino, dzina lawo Hezekiya. Chakumayambiriro kwa ulamuliro wa Yosiya, Zefaniya analemba buku la m’Baibulo lokhala ndi dzina lake. Zefaniya anachenjeza za zinthu zoipa zimene zidzachitikire anthu ochita zoipa, ndipo n’zoonekeratu kuti Yosiya anamvera machenjezo amenewo.

Wina amene anasonyeza chitsanzo chabwino anali Yeremiya, amene mwina ukumudziwa kale. Yeremiya ndi Yosiya onse anali achinyamata ndipo amakhala moyandikana. Yehova anauzira Yeremiya kulemba buku la m’Baibulo lokhala ndi dzina lake. Yosiya atafa kunkhondo, Yeremiya analemba nyimbo yachisoni yosonyeza mmene anakhudzidwira. (2 Mbiri 35:25) Ndipo Zikuoneka kuti ankalimbikitsana kuti azitumikira Yehova mokhulupirika.

Kodi ukuganiza kuti ungaphunzire chiyani pankhani ya Yosiya?​— Utakhala kuti nawenso ulibe bambo wotumikira Yehova ngati zinalili ndi Yosiya, kodi pali wina amene angakuthandize kuphunzira za Mulungu? Mwina amayi ako, agogo ako kapena wachibale wako winawake angakuthandize. Mwinanso ungathandizidwe ndi munthu wina wotumikira Yehova, amene mayi ako amuuza kuti aziphunzira nawe Baibulo.

Ngakhale kuti Yosiya anali mwana, ankadziwa kuti ayenera kucheza ndi anthu amene amatumikira Yehova. Iwenso uzichita zimenezi kuti uthe kuchita zabwino.

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.