Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

3. Lolani Kuti Ena Akuthandizeni

3. Lolani Kuti Ena Akuthandizeni

Zimene Mungachite Kuti Muzimvetsa Baibulo

3. Lolani Kuti Ena Akuthandizeni

Munthu wina wofufuza malo dzina lake Edward John Eyre, anayenda ulendo wodutsa m’chipululu cha Nullarbor Plain. Iye analola kuti anthu a m’chipululumo amuphunzitse mmene amapezera madzi mumchenga ndiponso m’mitengo inayake. Eyre sanafe ndi ludzu chifukwa choti anamvera zimene anthu omwe amalidziwa bwino deralo anamuuza.

CHITSANZO chimenechi chikusonyeza bwino mfundo yakuti munthu akafuna kugwira ntchito inayake yovuta, ayenera kuthandizidwa ndi winawake amene amadziwa bwino ntchitoyo. N’chimodzimodzinso ndi kuwerenga Baibulo.

Yesu ankadziwa kuti otsatira ake sangamvetse Baibulo popanda kuthandizidwa. Panthawi ina, iye “anawatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” (Luka 24:45) Yesu ankadziwa kuti anthu amafunikira kuthandizidwa kuti amvetse zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kodi Ndani Angakuthandizeni?

Yesu anapereka udindowu kwa otsatira ake oona. Iye asanapite kumwamba, anawalamula kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyo 28:19, 20) Ntchito yaikulu ya Akhristu ndi kuphunzitsa anthu Baibulo. Zimenezi zikuphatikizapo kufotokozera anthu mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wawo. Choncho, Akhristu oona ayenera kuthandiza anthu kumvetsa Baibulo.

Patangodutsa nthawi yochepa Yesu atapatsa otsatira ake ntchito imeneyi, panachitika chinthu chinachake chochititsa chidwi kwambiri. Baibulo limanena za mdindo wina wa ku Itopiya yemwe ankawerenga ulosi wa m’buku la Yesaya. Munthuyu akuwerenga ulosi umenewu, sanamvetse mavesi ena. Mavesi amene sanawamvetsewo amati: “Iye anam’tengera kokamupha ngati nkhosa. Ngatinso mwana wa nkhosa wongokhala chete pamene akum’meta, iye sanatsegule pakamwa pake. Panthawi ya kunyazitsidwa kwake, chiweruzo chomuyenera chinachotsedwa kwa iye. Ndani adzafotokoza tsatanetsatane wa mzera wake wobadwira? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”​—Machitidwe 8:32, 33; Yesaya 53:7, 8.

Mdindoyu anafunsa Filipo, yemwe anali Mkhristu wodziwa bwino Malemba kuti: “Kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iye mwini kapena za munthu wina?” (Machitidwe 8:34) Panthawiyi, munthu wa ku Itopiya woopa Mulungu ameneyu, ankachokera ku Yerusalemu komwe anakalambira. Zikuoneka kuti iye asanakumane ndi Filipo, anapemphera kuti athandizidwe kumvetsa malemba amene ankawerengawo. Ziyenera kuti iye ankawerenga mwachidwi kwambiri ndiponso anali ndi maganizo oyenera. Komabe, mdindoyu sanamvetse mavesiwo, choncho anadzichepetsa n’kupempha Filipo kuti amuthandize. Mdindoyu anasangalala kwambiri ndi mmene Filipo analongosolera mavesiwo moti anakhala Mkhristu.​—Machitidwe 8:35-39.

Mboni za Yehova zikupitirizabe kugwira ntchito imene Filipo komanso Akhristu oyambirira ankagwira. Mbonizo zikuthandiza anthu kumvetsa choonadi chimene Baibulo limaphunzitsa ndipo zikugwira ntchito imeneyi m’mayiko oposa 235. Zimakambirana ndi anthu nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku ofotokoza Baibulo. *​—Onani bokosi lakuti,  “Mayankho Ogwira Mtima a m’Baibulo.”

“Mafunso Anga Onse Anayankhidwa”

Patapita nthawi Steven, Valvanera, ndiponso Jo-Anne, omwe tawatchula m’nkhani yoyambirira ija anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Steven anena kuti: “Ndinadabwa kuona kuti tinkapeza mayankho mosavuta tikangowerenga ndiponso kuyerekezera mfundo kapena nkhani zingapo za m’Baibulo. Koma ndisanayambe kuphunzira Baibulo, palibe amene anandithandizapo chonchi. Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti n’zotheka kupeza mayankho a m’Baibulo, m’malo momangokangana ndiponso kutsutsana pankhani za m’Baibulo.”

Nayenso Valvanera anafotokoza kuti: “Zonse zimene ndinaphunzira ndi Mboni za Yehova zinali zogwirizana ndiponso zomveka bwino. Tinkapeza umboni wotsimikizira kuti zimene tikuphunzirazo ndi zoona, osati kungokhulupirira zinthu chifukwa choti ‘tchalichi’ n’chimene chanena.” Nayenso Jo-Anne anafotokoza kuti: “Ndinayamba kulemekeza kwambiri Mulungu chifukwa choti mafunso anga onse anayankhidwa m’Baibulo. Ndimaona kuti Mulungu anadziwiratu kuti anthu adzakhala ndi mafunso ambirimbiri, n’chifukwa chake anaika mayankho ogwira mtima m’Baibulo.”

Kodi pali munthu wina aliyense wa Mboni za Yehova amene mumamudziwa? Bwanji osam’pempha kuti akusonyezeni mmene amaphunzirira Baibulo ndi anthu? Koma ngati simukudziwa aliyense wa Mboni za Yehova, lembani kalata pogwiritsa ntchito adiresiyi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 4 la magazini ino. Monga mmene taonera, kuti muzimvetsa Baibulo, muyenera kupempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera, kuwerenga muli ndi maganizo oyenera ndiponso kulola kuti munthu wina wodziwa bwino Baibulo akuthandizeni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lathandiza anthu ambiri kuphunzira Baibulo.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

 Mayankho Ogwira Mtima a m’Baibulo

Zina mwa nkhani za m’Baibulo zimene mungaphunzire ndi Mboni za Yehova ndi zakuti:

• Kodi Mulungu ali nalo cholinga chotani dziko lapansili?

• Kodi akufa ali kuti?

• Kodi tili ‘m’masiku otsiriza’?

• N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

• Zimene mungachite kuti banja lanu likhale ndi moyo wosangalala

[Zithunzi patsamba 7]

Kuti muzimvetsa Baibulo, muyenera kupempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera, kuwerenga muli ndi maganizo oyenera ndiponso kulola kuti ena akuthandizeni