Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Amatchedwanso Mikayeli, Mkulu wa Angelo?

Kodi Yesu Amatchedwanso Mikayeli, Mkulu wa Angelo?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Yesu Amatchedwanso Mikayeli, Mkulu wa Angelo?

▪ Mwachidule tingayankhe kuti inde. Sizachilendo masiku ano kuti munthu akhale ndi maina ambiri ndipo ndi mmenenso zilili ndi anthu ena otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yakobo ankatchedwanso ndi dzina lakuti Isiraeli. (Genesis 35:10) Mtumwi Petulo ankadziwika ndi maina asanu awa: Simoni, Sumeoni, Petulo, Kefa ndi Simoni Petulo. (Mateyo 10:2; 16:16; Yohane 1:42; Machitidwe 15:7, 14) Ndiyeno kodi tikudziwa bwanji kuti dzina lina la Yesu ndi Mikayeli? Tiyeni tione umboni wotsatirawu wochokera m’Baibulo.

M’Baibulo muli mavesi asanu omwe mngelo wina wamphamvu kwambiri amatchedwa Mikayeli. Atatu mwa mavesi amenewa amapezeka m’buku la Danieli. Mwachitsanzo, palemba la Danieli 10:13, 21, timawerenga kuti mngelo wina yemwe anatumidwa anapulumutsidwa ndi Mikayeli yemwenso amatchedwa “mmodzi mwa akalonga aakulu” ndiponso “kalonga wanu.” Kenako pa Danieli 12:1 timawerenga kuti panthawi yamapeto “adzauka Mikayeli kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako.”

Dzina lakuti Mikayeli limapezekanso pa Chivumbulutso 12:7, pomwe pamanena kuti “Mikayeli ndi angelo ake” anamenya nkhondo yaikulu yomwe inachititsa kuti Satana Mdyerekezi ndi angelo ake oipa athamangitsidwe kumwamba.

Onani kuti malemba omwe ali pamwambawa akusonyeza kuti Mikayeli ndi mngelo komanso mkulu wankhondo amene akumenya nkhondo pofuna kuteteza anthu a Mulungu. Mikayeli anafika mpaka pomenyana ndi Satana yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova.

Lemba la Yuda 9 limanena kuti Mikayeli ndi “mkulu wa angelo.” Lemba lina limene limatchula mkulu wa angelo ndi 1 Atesalonika 4:16 pomwe Paulo anafotokoza za Yesu atabwerera kumwamba. Iye ananena kuti: “Ambuye [Yesu] iye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo, ndi lipenga la Mulungu.” Choncho, lembali likusonyeza kuti Yesu Khristu ndi mkulu wa angelo.

Poona zimene takambiranazi, kodi tingati chiyani? Yesu Khristu ndi dzina linanso la Mikayeli, mkulu wa angelo. Maina akuti Mikayeli (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Mulungu?”) ndiponso lakuti Yesu (kutanthauza “Yehova Ndiye Chipulumutso”), amasonyeza udindo wake ngati mtsogoleri wa anthu omwe ali kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. Lemba la Afilipi 2:9 limati: “Mulungu anam’kwezera [Yesu mu ulemerero wake] pamalo apamwamba. Ndipo anam’komera mtima kum’patsa dzina loposa lina lililonse.”

Tiyeneranso kudziwa kuti Yesu analipo kale asanadzabadwe ngati munthu padziko lino lapansi. Iye asanabadwe, mngelo wina anapita kwa Mariya kukamuuza kuti adzakhala ndi pakati mwamphamvu ya mzimu woyera ndipo dzina la mwanayo lidzakhala Yesu. (Luka 1:31) Pamene amachita utumiki wake, nthawi zambiri Yesu ankanena kuti anali ndi moyo kumwamba asanabwere padziko lino lapansi.​—Yohane 3:13; 8:23, 58.

Choncho, Yesu asanabwere padziko lapansi ankatchedwa Mikayeli mkulu wa angelo. Komanso ataukitsidwa n’kubwerera kumwamba, Yesu anakapitiriza udindo wake monga Mikayeli, mkulu wa angelo ndipo amagwira ntchito imeneyi “polemekeza Mulungu Atate.”​—Afilipi 2:11.