Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndani?

Kodi Mulungu Ndani?

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi Mulungu Ndani?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Mulungu ndani?

Mulungu woona ndiye Mlengi wa zinthu zonse. Baibulo limanena kuti iye ndi “Mfumu yamuyaya,” kutanthauza kuti alibe chiyambi ndiponso sadzakhala ndi mapeto. (Chivumbulutso 15:3) Popeza Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse, tiyenera kulambira iye yekha basi.​—Werengani Chivumbulutso 4:11.

2. Kodi Mulungu ndi wotani?

Palibe amene anaonapo Mulungu chifukwa iye ndi Mzimu. Zimenezi zikutanthauza kuti iye ndi wapamwamba kwambiri ndipo sangafanane ndi cholengedwa chilichonse padziko pano. (Yohane 1:18; 4:24) Zinthu zimene Mulungu analenga zimasonyeza makhalidwe ake. Mwachitsanzo, tikaganizira mmene iye analengera mwaluso mitundu yosiyanasiyana ya zipatso ndi maluwa timaona kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru kwambiri. Komanso kuchuluka ndi kukula kwa zinthu zakuthambo ndiponso dziko lapansi zimatisonyeza kuti Mulungu ndi wamphamvu.​—Werengani Aroma 1:20.

Tingaphunzirenso zambiri zokhudza makhalidwe a Mulungu m’Baibulo. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza zimene Mulungu amakonda komanso zimene amadana nazo, mmene amachitira zinthu ndi anthu komanso mmene amachitira zinthu pa zochitika zosiyanasiyana.​—Werengani Salimo 103:7-10.

3. Kodi Mulungu ali ndi dzina?

Yesu ananena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mayina audindo ambiri, koma kwenikweni dzina lake ndi limodzi. Dzinali limatchulidwa mosiyanasiyana m’zilankhulo zosiyanasiyana. Mwachitsanzo m’Chichewa dzinali nthawi zambiri timalitchula kuti “Yehova” ndipo nthawi zina “Yahweh.”​—Werengani Salimo 83:18.

M’Mabaibulo ambiri, pamene panali dzina la Mulungu limeneli analichotsapo n’kuikapo dzina laudindo monga Ambuye kapena Mulungu. Koma pamene Baibulo linkalembedwa munali dzina la Mulungu maulendo pafupifupi 7,000. Yesu anachititsa kuti anthu adziwe dzina la Mulungu chifukwa ankalitchula powafotokozera Mawu a Mulungu. Choncho iye anathandiza anthu kudziwa Mulungu.​—Werengani Yohane 17:26.

4. Kodi Yehova amatidera nkhawa?

Yehova amasonyeza kuti ali nafe chidwi chifukwa amamvetsera mapemphero athu. (Salimo 65:2) Koma kodi kuchuluka kwa mavuto padzikoli ndi umboni wakuti Mulungu satidera nkhawa? Ena amanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika n’cholinga chakuti atiyese, koma zimenezi sizoona. Baibulo limanena kuti: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe.”​—Yobu 34:10; werengani Yakobo 1:13.

Mulungu anapatsa anthu ufulu wosankha. Kodi simukuyamikira kuti muli ndi ufulu wosankha kutumikira Mulungu? (Yoswa 24:15) Padzikoli pali mavuto ambiri chifukwa chakuti anthu ambiri amasankha kuchitira ena zoipa. Koma zimenezi zimam’pweteka kwambiri Yehova.​—Werengani Genesis 6:5, 6.

Posachedwapa Yehova adzagwiritsa ntchito Yesu kuchotsa mavuto onse pamodzi ndi anthu onse amene amachititsa mavutowo. Padakali pano Yehova ali ndi zifukwa zabwino kwambiri zololera kuti kwakanthawi anthu azivutika. Nkhani ina ya ngati ino, idzafotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti padzikoli pakhale mavuto.​—Werengani Yesaya 11:4.

5. Kodi Mulungu amafuna kuti tizichita chiyani?

Yehova anatilenga mwa njira yoti tikhoza kumudziwa ndiponso kumukonda. Iye amafuna kuti tiphunzire choonadi chokhudza iyeyo. (1 Timoteyo 2:4) Tikamaphunzira Baibulo tingathe kumudziwa Mulungu ndipo angakhale Bwenzi lathu.​—Werengani Miyambo 2:4, 5.

Popeza Yehova ndi amene anatipatsa moyo, tiyenera kumukonda kuposa aliyense. Tikamapemphera kwa Mulungu komanso kuchita zimene iye amafuna, timasonyeza kuti timamukonda. (Miyambo 15:8) Yehova amafuna kuti pochita zinthu ndi anthu anzathu, tizisonyeza chikondi.​—Werengani Maliko 12:29, 30; 1 Yohane 5:3.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 1 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi pangakhale chifukwa chabwino chololera kuti munthu amene mumamukonda avutike kwakanthawi?