Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?

Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?

Inde, padziko lonse pali akazi ambirimbiri a Mboni za Yehova amene amaphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Iwo amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Lemba la Salimo 68:11 limanena kuti: “Yehova wapereka lamulo, ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”

Komabe zimene akazi a Mboni za Yehova amachitazi n’zosiyana kwambiri ndi zimene abusa aakazi amachita m’zipembedzo zina. Kodi zimasiyana bwanji?

Atsogoleri aakazi a zipembedzo zina, makamaka zachikhristu, amakhala ndi udindo mumpingo ndipo amaphunzitsa anthu a mumpingomo. Koma akazi a Mboni za Yehova saphunzitsa mumpingo, koma amaphunzitsa anthu amene amawapeza akamalalikira kunyumba ndi nyumba komanso kumalo ena.

Kusiyana kwina pakati pa akazi a Mboni za Yehova ndi akazi a m’zipembedzo zina n’kwakuti, akazi a Mboni za Yehova sakhala atsogoleri mumpingo. Akazi a zipembedzo zina amakhala atsogoleri m’mipingo yawo n’kumapereka malangizo kwa anthu a mumpingomo. Koma akazi a Mboni saphunzitsa mumpingo pokhapokha ngati palibe mwamuna wobatizidwa. Amuna oikidwa okha ndi amene amaphunzitsa mumpingo.​—1 Timoteyo 3:2; Yakobo 3:1.

Baibulo limasonyeza kuti amuna ndi amene amayenera kukhala ndi udindo woyang’anira mumpingo. Taonani dongosolo limene mtumwi Paulo anafotokoza pamene ankalembera kalata woyang’anira mnzake, dzina lake Tito. Iye anati: “Ndinakusiya ku Kerete kuti . . . uike akulu mumzinda uliwonse.” Paulo ananenanso kuti munthu woikidwayo “ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi.” (Tito 1:5, 6) Paulo anaperekanso malangizo ofanana ndi amenewa m’kalata yake imene analembera Timoteyo. Iye anati: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino. Woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, . . . wotha kuphunzitsa.”—1 Timoteyo 3:1, 2.

N’chifukwa chiyani amuna okha ndi amene ayenera kupatsidwa udindo woyang’anira mumpingo? Paulo ananena kuti: “Sindikuvomereza kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa mwamuna, koma azikhala chete. Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.” (1 Timoteyo 2:12, 13) Choncho zimene Mulungu anachita polenga mwamuna poyamba asanalenge mkazi, zikusonyeza kuti iye amafuna kuti amuna ndiye azikhala ndi udindo woyang’anira ndi kuphunzitsa mumpingo.

Amuna ndi akazi a Mboni za Yehova amatsatira chitsanzo cha Mtsogoleri wawo, Yesu Khristu. Pofotokoza zimene Yesu ankachita, Luka analemba kuti: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” Kenako Yesu anatumiza otsatira ake kuti akagwire ntchito yomweyi. Baibulo limati iwowo “ananyamuka ndi kulowa m’deralo m’mudzi ndi mudzi. Iwo anali kulengeza uthenga wabwino.”​—Luka 8:1; 9:2-6.

Masiku ano amuna ndi akazi a Mboni za Yehova amagwiranso ntchito imeneyi, yomwe Yesu analosera. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14.