Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zotheka Kuchita Zinthu Mwachilungamo M’Dziko Laziphuphuli?

Kodi N’zotheka Kuchita Zinthu Mwachilungamo M’Dziko Laziphuphuli?

“Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—AHEBERI 13:18.

NGAKHALE kuti pali Mdyerekezi, uchimo komanso tikukhala m’dziko loipali, tingathe kuchita zinthu mwachilungamo. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichita zinthu mwachilungamo? Tiyenera kuyesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kutsatira mfundo za m’Mawu ake, Baibulo. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musamatsanzira makhalidwe oipa a dziko lino lapansi.”—Aroma 12:2, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.

Zimene zinachitikira munthu wina: Guilherme amakhala ku Brazil ndipo ali ndi bizinezi yaikulu. Iye anafotokoza kuti kukhala woona mtima n’kovuta kwambiri. Iye anati: “Munthu akamachita bizinezi amayamba kuchita zinthu zachinyengo mwina pofuna kukwaniritsa zolinga za kampani yake kapena pofuna kuti kampaniyo ipitirizebe kuyenda bwino. Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto ndi kuchita ziphuphu. Komanso ukakhala kuti wangoyamba kumene bizinezi ndipo uli ndi ngongole zambiri, zimavuta kuti uzichita zinthu moona mtima.”

Ngakhale zili choncho, Guilherme amayesetsa kuchita zinthu moona mtima. Iye anati: “Ngakhale kuti anthu ambiri amaona kuti munthu sangapange bizinezi popanda kuchita zachinyengo, ine ndimaona kuti n’zotheka kuchita zinthu moona mtima. Chofunika n’kukhala ndi mfundo zimene umayendera. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwandithandiza kuti ndikhale ndi chikumbumtima chabwino, ndikhale ndi mtendere wamumtima komanso kuti anthu azindilemekeza. Ukamachita zinthu moona mtima umakhala chitsanzo chabwino kwa anthu ena.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto. Pakuti kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”—1 Timoteyo 6:9, 10.

Zimene zinachitikira munthu wina: André ali ndi kampani ya zachitetezo. Mmodzi mwa makasitomala ake, ndi timu ina yaikulu ya mpira wamiyendo. Tsiku lina mpira utatha André anapita kumaofesi a timuyi kuti akatenge ndalama za ntchito imene kampani yake inagwira pa tsikulo. Anthu ogwira ntchito m’dipatimenti yoyang’anira za chuma anali otanganidwa n’kuwerengetsera ndalama zimene timuyi inapeza pa masewerawo. Popeza nthawi inali itatha, woyang’anira wa dipatimentiyi analipira André komanso anthu onse amene makampani awo anagwira ntchito.

André anati: “Ndikupita kunyumba, ndinazindikira kuti woyang’anira wa dipatimenti uja anandipatsa ndalama zambiri. Ndinadziwa kuti iye sangadziwe munthu amene wamupatsa ndalama zambiri ndipo zimenezi zikanachititsa kuti iyeyo apereke ndalama za m’thumba mwake polipira ndalama zimene anandiwonjezerazo. Choncho ndinaganiza zobwerera kukabweza ndalamazi. Ndinayesetsa kudutsa m’chigulu cha anthu mpaka ndinakam’peza n’kumubwezera ndalamazo. Iye anadabwa kwambiri chifukwa munthu sanamubwezerepo ndalama.”

André ananenanso kuti: “Zimenezi zinachititsa kuti woyang’anirayo azindilemekeza kwambiri. Papita zaka zambiri kuchokera pamene zimenezi zinachitika ndipo pa makampani onse amene ankapatsidwa ntchito ndi timuyi, ndi kampani yanga yokha imene ikupitirizabe kugwira ntchito za timuyi. Ndikuona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kwandithandiza kukhala ndi mbiri yabwino.”

N’zolimbikitsa kudziwa kuti, ndi thandizo la Mulungu, tingathe kupewa khalidwe lochita ziphuphu. Komabe panopa khalidwe loipali silingatheretu m’dzikoli. Zili choncho chifukwa anthu opanda ungwiro sangathe kuchotsa zimene zimayambitsa ziphuphu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti ziphuphu sizidzatha? Nkhani yotsatira ili ndi yankho la m’Baibulo lolimbikitsa la funso limeneli.