Kodi Mitundu ya Kaonekedwe ka Zinthu Imakukhudzani Bwanji?
Mukamayang’ana zinthu zosiyanasiyana, maso ndi ubongo wanu zimagwirira ntchito limodzi. Mukaona chipatso, nthawi yomweyo mumasankha kuchidya kapena ayi. Mukayang’ana kumwamba, mumatha kuzindikira ngati kungagwe mvula kapena ayi. Ndipo pamene mukuyang’ana mawu a m’nkhaniyi, maganizo anu akutha kuzindikira tanthauzo lake. Pamene mukuchita zimenezi mumakhala mukutsatira mitundu ya kaonekedwe ka zinthu. Koma mwina mukukayikira ngati zimenezi zili zoona.
Kaonekedwe ka chipatso kangakuthandizeni kuzindikira ngati chapsa komanso ngati chingakome kuchidya. Mmene kumwamba kukuonekera ndiponso mtundu wa mitambo zakuthandizani kudziwa nyengo. Pamene mukuwerenga nkhaniyi, maso anu akutha kusiyanitsa mtundu wa zilembo ndi mtundu wa pepala. Zimenezi zikusonyeza kuti, mosadziwa, mitundu ya zinthu ikukuthandizani kuzindikira zinthu zosiyanasiyana zimene muli nazo pafupi. Koma mitundu ya zinthu imathanso kukhudza maganizo athu komanso mmene timaonera zinthu.
MMENE KAONEKEDWE KA ZINTHU KAMAKHUDZIRA KAGANIZIDWE KATHU
Mukamayenda musitolo, mumaona zinthu zosiyanasiyana monga tizitini, mabokosi ndiponso mapepala oikamo zinthu omwe anakonzedwa mokopa kwambiri. Kaya mukudziwa kapena ayi, otsatsa malonda amayesetsa kusankha mitundu yomwe mungakopeke nayo malinga ndi msinkhu wanu komanso potengera kuti ndinu mwamuna kapena mkazi. Anthu okonza zinthu zokongoletsera m’nyumba, osoka zovala, ndiponso akatswiri ojambula amadziwanso kuti mtundu umene angasankhe ungakhudze maganizo a munthu.
Anthu amaona mosiyanasiyana mitundu ya zinthu potengera miyambo ndi chikhalidwe chawo. Mwachitsanzo, anthu ena a ku Asia amakhulupirira kuti zinthu zofiira zimabweretsa mwayi ndipo n’zofunika kugwiritsa ntchito pachisangalalo, pomwe anthu am’madera ena a ku Africa kuno amaona kuti zinthu zofiira n’zoyenera kugwiritsa ntchito pamaliro. Komabe, pali mitundu ina imene anthu onse amaiona mofanana. Tiyeni tione mitundu itatu ndiponso mmene ingakhudzire maganizo anu.
Zinthu ZOFIIRA zimaonekera patali kwambiri. Nthawi zambiri anthu akaona zinthu zofiira amaganizira za mphamvu, nkhondo, ndiponso zinthu zoopsa. Mtundu umenewu ndi wamphamvu kwambiri ndipo umathandiza thupi kugaya bwino chakudya, kupuma bwino, ndiponso umawonjezera kuthamanga kwa magazi.
M’Baibulo, mawu achiheberi omwe anawatanthauzira kuti “kufiira” anachokera ku mawu omwe amatanthauza “magazi.” Baibulo limanena za mtundu wofiira kwambiri pofuna kutithandiza kuona m’maganizo mwathu hule lankhanza lovala zovala zofiirira, lomwe lakwera “pachilombo chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu.”—Chivumbulutso 17:1-6.
Anthu akaona zinthu ZAGILINI, kapena kuti zobiriwira, amaganizira za zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene amaganizira akaona zinthu zofiira. Zinthu zagilini zimachedwetsa kagayidwe ka chakudya ndiponso zimathandiza munthu kuti mtima wake ukhale m’malo. N’chifukwa chake timasangalala tikaona malo amene pali maluwa obiriwira komanso mapiri. Buku la Genesis limasonyeza kuti Mulungu analenga udzu ndi zomera zobiriwira n’cholinga choti anthu asangalale nazo.—Genesis 1:11, 12, 30.
Anthu akaona zinthu ZOYERA amaganizira za kuwala, chitetezo ndiponso ukhondo. Anthu akaona zinthu zoyera amaganiziranso za makhalidwe ngati ubwino, kusalakwa, ndiponso kusakhala ndi chilichonse chodetsa. Mtundu umenewu ndi umene umatchulidwa kwambiri m’Baibulo. M’masomphenya, anthu komanso angelo amaoneka atavala zovala zoyera posonyeza kuti ndi olungama komanso kuti ndi oyera mwauzimu. (Yohane 20:12; Chivumbulutso 3:4; 7:9, 13, 14) Masomphenya osonyeza anthu okwera pamahatchi oyera atavalanso zovala zoyera bwino, amaimira nkhondo yolungama ya Mulungu. (Chivumbulutso 19:14) Mulungu amagwiritsa ntchito kuyera pofuna kutsindika mfundo yakuti iye ndi wokonzeka kukhululukira anthu machimo awo. Mwachitsanzo, iye ananena kuti: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.”—Yesaya 1:18.
MITUNDU IMATITHANDIZA KUKUMBUKIRA ZINTHU
Mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mitundu ya zinthu zimasonyeza kuti Mulungu amadziwa mmene anthu amakhudzidwira ndi mitundu ya zinthu. Mwachitsanzo, buku la Chivumbulutso linaneneratu za zinthu zimene zikuchitika masiku ano, monga nkhondo, njala, ndiponso imfa zobwera chifukwa cha matenda ndi kusowa kwa chakudya. Pofuna kutithandiza kukumbukira ulosiwu, bukuli limanena za anthu okwera pamahatchi a mitundu yosiyanasiyana.
Poyamba amafotokoza za hatchi yoyera, yomwe imaimira nkhondo yolungama ya Yesu Khristu. Kenako amafotokoza za hatchi yofiira, yomwe imaimira nkhondo za pakati pa mayiko. Pambuyo pa hatchi imeneyi pamabwera hatchi yakuda, yomwe imaimira njala. Kenako pamabwera “hatchi yotuwa [ndipo] wokwerapo wake dzina lake anali Imfa.” (Chivumbulutso 6:1-8) Mtundu wa hatchi iliyonse umatipangitsa kuti tiziganizira zinthu zofanana ndi zimene hatchiyo ikuimira. Zimenezi zimatithandiza kuti tizikumbukira mosavuta mahatchi amenewa komanso zomwe akutiphunzitsa masiku ano.
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza kuti Baibulo limagwiritsa ntchito mitundu yosiyanasiyana pofuna kutithandiza kuona nkhaniyo m’maganizo mwathu. Mulungu, yemwe analenga kuwala, mitundu ya zinthu, komanso maso athu, amatha kugwiritsa ntchito mwaluso mitunduyi ngati njira yotithandizira kumvetsa komanso kukumbukira zimene timawerenga. Mitundu imatithandizanso kuti tizizindikira komanso kukumbukira zinthu mosavuta. Imakhudzanso mmene timamvera komanso imatithandiza kukumbukira zinthu zofunika. Choncho mitundu ya zinthu ndi mphatso yomwe Mlengi anatipatsa kuti tizisangalala ndi moyo.