Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | MABODZA OMWE AMALEPHERETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Choonadi Chidzakumasulani

Choonadi Chidzakumasulani

Tsiku lina Yesu ali ku Yerusalemu ankalankhula za Yehova, yemwe ndi Atate ake. Iye anadzudzula atsogoleri achipembedzo chonyenga amene analipo pa nthawi imeneyo. (Yohane 8:12-30) Zimene ananena pa tsikuli zimatiphunzitsa mmene tiyenera kuonera zikhulupiriro zokhudza Mulungu zimene anthu ambiri amazikhulupirira. Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:31, 32.

Ponena kuti “mukamasunga mawu anga,” Yesu anatchula mfundo imene ingatithandize kuzindikira ngati ziphunzitso zachipembedzo zili zolondola. Munthu wina akamakufotokozerani nkhani yokhudza Mulungu, muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene munthuyu akunena zikugwirizana ndi zimene Yesu ananena? Kodi n’zogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena?’ Mungachite bwino kutengera chitsanzo cha anthu amene ankamvetsera Paulo akulankhula, omwe “anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.”—Machitidwe 17:11.

Marco, Rosa ndi Raymonde, amene mawu awo ali m’nkhani yoyambirira ija, anafufuza mosamala zimene ankakhulupirira kuti aone ngati zinali zoona. Iwo anachita zimenezi pophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kodi anthuwa anaphunzira zotani?

Marco: “Munthu amene ankatiphunzitsa Baibulo anayankha mafunso onse amene ine ndi mkazi wanga tinali nawo pogwiritsa ntchito Baibulo. Tinayamba kukonda Yehova, komanso ine ndi mkazi wanga tinayamba kukondana kwambiri.”

Rosa: “Poyamba ndinkaganiza kuti Baibulo ndi buku lofotokoza za Mulungu limene anthu analemba pogwiritsa ntchito nzeru zawo. Koma m’kupita kwa nthawi ndinayamba kupeza mayankho a mafunso amene ndinali nawo kuchokera m’Baibulo. Panopa ndimaona kuti Yehova ndi weniweni. Tsopano ndili ndi Mulungu amene ndingamudalire.”

Raymonde: “Ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuphunzira za iye. Pasanapite nthawi, ine ndi mwamuna wanga tinayamba kuphunzira Baibulo ndipo zimenezi zinatithandiza kudziwa zolondola zokhudza Yehova. Tinasangalala kwambiri titazindikira kuti Mulungu ndi wachikondi.”

Baibulo silimangotithandiza kuzindikira mabodza okhudza Mulungu, koma limatiuzanso za makhalidwe abwino amene Mulunguyo ali nawo. Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu ndipo limatithandiza “kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.” (1 Akorinto 2:12) Bwanji nanunso osaphunzira Baibulo kuti mupeze mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza Mulungu, cholinga chake komanso madalitso amene tidzalandire m’tsogolo? Mungawerenge ena mwa mayankho a mafunsowa pa webusaiti ya www.mt1130.com. Pitani pamene palembedwa kuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa > Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” Mungathenso kupempha pa webusaitiyi kuti wa Mboni wina azikuphunzitsani Baibulo kapena mungafunse wa Mboni za Yehova aliyense. Tikukhulupirira kuti ngati mutachita zimenezi mudzaona kuti n’zotheka kukonda Mulungu.