Kodi Mukudziwa?
Kodi anthu a m’nthawi ya Yesu, ankapereka bwanji zopereka zawo?
Kukachisi wa Ayuda, mabokosi oponyamo ndalama ankapezeka m’bwalo limene kunkasonkhana azimayi. Buku lina limati: “Panali zipilala kuzungulira kachisi yense ndipo pafupi ndi khoma pankaimikidwa mabokosi 13 ooneka ngati malipenga mmene anthu ankaponyamo zopereka zawo.”—The Temple—Its Ministry and Services.
Mabokosiwa ankatchedwanso malipenga chifukwa ankaoneka ngati malipenga. Ankakhala akukamwa kwakung’ono ndipo kumunsi kwake kunkakhala kwakukulu. Bokosi lililonse linkalembedwa mawu osonyeza ntchito ya ndalama zoponyedwa m’bokosilo ndipo ndalama za m’bokosilo zinkagwiritsidwa ntchito pa cholinga chimenecho. Yesu anali pafupi ndi malo amene pankakhala mabokosiwa pomwe anaona anthu osiyanasiyana, kuphatikizapo mayi wamasiye, akuponya zopereka zawo.—Luka 21:1, 2.
Mabokosi awiri ankaponyamo ndalama za msonkho. Lina ankaponyamo ndalama za msonkho wa pakachisi wa chaka chimenecho ndipo linalo ankaponyamo ndalama za msonkho wa chaka chapita. Kuyambira bokosi lachitatu mpaka la 7, ankaponyamo ndalama zokwana kugulira njiwa, nkhunda, matabwa, zofukiza zonunkhira komanso zipangizo za golide zogwiritsa ntchito pakachisi. Ngati munthu anasunga ndalama zopitirira kugula nyama ya nsembe, ankaponya ndalama yotsalayo m’bokosi lililonse pa mabokosi otsalawo. Bokosi la 8 linali la ndalama zotsala ku nsembe zamachimo. Bokosi la 9 mpaka la 12, linali loponyamo ndalama za nsembe za kupalamula, za mbalame zopereka nsembe, zopereka za Anaziri komanso zopereka za anthu akhate. Ndipo bokosi la 13 linali la ndalama zimene anthu ankapereka mwa kufuna kwawo.
Kodi zimene zili m’Baibulo zomwe Luka analemba ndi zolondola?
Luka ndi amene analemba buku la Uthenga Wabwino limene limadziwika ndi dzina lake komanso buku la Machitidwe a Atumwi. Iye ananena kuti ‘anafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.’ Koma akatswiri ena amakayikira ngati zimene Luka analemba zilidi zolondola. (Luka 1:3) Kodi tingatsimikize bwanji kuti zimene analemba ndi zolondola?
Luka anatchula mfundo zina zomwe zimapezekanso m’mabuku a mbiri yakale. Mwachitsanzo, ponena za anthu ena, a ku Filipi, Tesalonika ndi Efeso, iye anagwiritsa ntchito maina a udindo, monga akuti, akuluakulu a boma, olamulira mzinda komanso oyang’anira zikondwerero ndi masewera. (Machitidwe 16:20; 17:6; 19:31) Luka anatchulanso kuti Herode Antipa anali wolamulira chigawo ndipo Serigio, Paulo anamutchula kuti anali bwanamkubwa wa ku Kupuro.—Machitidwe 13:1, 7.
Zimene Luka anachita, potchula mayina a udindo a olamulira, n’zochititsa chidwi kwambiri, chifukwa dera limene Aroma ankalamulira likasintha, maudindonso ankasintha. Koma mogwirizana ndi zimene katswiri wina wa Baibulo, dzina lake Bruce Metzger ananena, “nthawi zonse zimene zimapezeka m’buku la Machitidwe zimakhala zolondola mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa nthawiyo komanso malo amene zinachitikira.” Katswiri winanso, dzina lake William Ramsay, ananena kuti Luka anali “katswiri wolemba mbiri yakale.”