BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Lonjezo la Paradaiso Linasintha Moyo Wanga
CHAKA CHOBADWA: 1974
DZIKO: LATVIA
POYAMBA: NDINKAPANGA MPIKISANO WOKWERA NJINGA YAMOTO
KALE LANGA: Ndinabadwira mumzinda wa Riga, likulu la dziko la Latvia.
M’banja mwathu tinalipo ana awiri, ineyo ndi mchemwali wanga, ndipo tinkaleredwa ndi mayi. Ngakhale kuti mayi anga ndi akatolika, tinkapita kutchalitchi kukakhala zochitika zapadera basi. Kuyambira kale, ndimakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma ndili mwana ndinasokonezedwa ndi zinthu zina.
Pamene ndinkakula, amayi anga anazindikira kuti ndili ndi luso lotha kuphwasula chinthu n’kuchibwezeretsanso. Izi zinkachititsa kuti aziopa kundisiya ndekha panyumba chifukwa ankada nkhawa kuti mwina ndiphwasula zinthu. Choncho anandipatsa zoseweretsa zimene ndinkatha kumangira kanyumba, n’kukaphwasulanso. Ndinkakondanso kwambiri masewera okwera njinga yamoto. Chifukwa cha zimenezi mayi anandilipirira sukulu ina kuti ndiziphunzira mpikisano woyendetsa njinga yamoto. Poyamba ndinkachita mpikisanowu pogwiritsa ntchito njinga zangati zopalasa, koma kenako ndinayamba kugwiritsira ntchito njinga zamoto.
Ndinkaphunzira zinthu mwachangu moti pasanapite nthawi ndinakhala katswiri wa mpikisanowu. Kangapo konse ndinalandira mphoto chifukwa chopambana pa mpikisanowu. Koma masewerawa ndi oika moyo pachiswe.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Pa nthawi imene ndinkachita mpikisanowu, mtsikana amene ndinali naye pa chibwenzi, dzina lake Evija, anapatsidwa mabuku a Mboni za Yehova. M’mabukuwa anapezamo malo ena amene anasonyeza kuti angathe kulembapo, ngati akufuna kuti a Mboni za Yehova aziphunzira naye Baibulo. Iye analembadi, n’kutumiza ku ofesi ya Mboni za Yehova. Pasanapite nthawi, azimayi awiri a Mboni za Yehova anabwera n’kuyamba kuphunzira naye Baibulo. Ndinalibe nazo vuto zimenezi, kungoti ineyo pa nthawiyi ndinalibe chidwi kwenikweni ndi zinthu zauzimu.
Kenako, azimayi a Mboniwo anandipempha kuti ndizikhalapo akamaphunzira Baibulo ndi Evija kuti ndizimva nawo zimene akuphunzirazo. Ndinavomera, ndipo ndinkasangalala kwambiri ndi zomwe ndinkaphunzira. Chinthu china chimene chinandikhudza mtima kwambiri ndi lonjezo la m’Baibulo lonena za dziko lapansi la paradaiso. Mwachitsanzo, anandionetsa lemba la Salimo 37:10, 11, limene limati: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Lonjezo limeneli linandisangalatsa kwambiri.
Ndinayamba kuchita chidwi ndi zinthu zauzimu. Ndinazindikira kuti pali zinthu zabodza zambiri zimene matchalitchi amaphunzitsa. Koma ndinaona kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zosangalatsa komanso zomveka bwino.
Pamene ndinkapitiriza kuphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti Yehova amaona kuti moyo ndi chinthu chamtengo wapatali. (Salimo 36:9) Choncho ndinaganiza zosiya kuchita mpikisano uja chifukwa ndinaona kuti si bwino kumachita masewera oika moyo pangozi. Ndinkafuna kugwiritsa ntchito moyo wanga kutumikira Yehova. Ndinaona kuti kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri kuposa zonse zimene ndinkapeza pochita mpikisano.
Ndinazindikira kuti ndili ndi udindo wosamalira moyo umene Yehova anandipatsa
Mu 1996, ndinachita nawo msonkhano wa Mboni za Yehova wa anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Msonkhanowu unachitikira ku Tallinn, m’dziko la Estonia pafupi ndi sitediyamu yomwe kunkachitira mpikisano uja. Pamsonkhanowu ndinadabwa kuona kuti anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana anali ogwirizana kwambiri komanso ankakhala mwamtendere. Mwachitsanzo, nditamva kuti mayi wina wa Mboni wataya kachikwama kake kam’manja, ndinaganiza kuti basi kapita kameneko. Koma pasanapite nthawi, wa Mboni wina anatola kachikwamako n’kukapereka kwa mwiniwake ndipo palibe chimene chinasowamo. Zimenezi zinandidabwitsa kwambiri ndipo ndinazindikira kuti a Mboni amatsatiradi mfundo za m’Baibulo. Ine ndi Evija tinapitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo mu 1997, tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Anzanga ena anamwalira chifukwa chochita mpikisano wokwera njinga zamoto. Koma ineyo, kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuzindikira kuti ndili ndi udindo wosamalira moyo umene Yehova anandipatsa. Zimenezi zathandiza kuti ndisafe msanga.
Ine ndi Evija tinakhala ndi mwayi wotumikira pa maofesi a Mboni za Yehova ku Riga kwa zaka 4. Panopa tikusangalala kwambiri kuthandiza mwana wathu wamkazi, Alise, kuti nayenso azikonda Yehova. Masiku ano ndimapitabe ku ofesi ya Mboni yomasulira mabuku, tsiku limodzi pa mlungu, kukathandiza kukonza magalimoto. Ndimasangalala kwambiri kugwiritsira ntchito luso langa, lobwezeretsa zinthu lija, potumikira Yehova.
Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuuza ena zokhudza Mulungu woona yekha, ndipo ndimachita zimenezi ndi banja langa. Ndimazindikira kuti zonsezi zatheka chifukwa cha zimene ndaphunzira m’Baibulo. Ndithudi, lonjezo loti dziko lapansi lidzakhala paradaiso linasintha moyo wanga.