BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Ndinkayenda ndi Mfuti Kulikonse
CHAKA CHOBADWA: 1958
DZIKO: ITALY
POYAMBA: NDINALI M’GULU LA ZIGAWENGA
KALE LANGA:
Ndinabadwira mumzinda wa Rome m’dera limene kunkakhala anthu ambiri osauka. Ndinakulira m’matauni osiyanasiyana a mumzinda womwewu ndipo tinkakhala movutika kwambiri. Mayi anga enieni sindinkawadziwa, ndipo sindinkagwirizana kwenikweni ndi bambo anga. Kudera limene tinkakhalali kunkachitika zinthu zachiwawa zambiri moti ndinangozizolowera.
Mmene ndinkakwanitsa zaka 10, n’kuti nditayamba kale kuba ndipo ndili ndi zaka 12, ndinachoka panyumba. Sindinkati ndamangidwa liti moti nthawi zambiri bambo anga ankakanditenga kupolisi n’kubwerera nane kunyumba. Ndinali wachiwawa komanso ndinkalusira aliyense moti ndinkangokhalira kukangana ndi anthu. Ndili ndi zaka 14, ndinachokeratu panyumba ndipo sindinabwererenso. Ndinkakhala m’misewu ndipo ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthawi zambiri ndinkagona m’magalimoto a anthu n’kuchokamo m’bandakucha. Ndikatero ndinkafufuza madzi oti ndisukusule.
Ndinajaila kuba moti ndinkaba chilichonse, kaya m’zikwama za anthu kapena kuthyola nyumba usiku. Anthu onse a m’dera lathu ankandidziwa kuti ndine mbava. Pasanapite nthawi ndinalowa m’gulu lina la zigawenga ndipo izi zinachititsa kuti ndiphunzirenso kuba m’mabanki. Chifukwa choti ndinkaoneka woopsa komanso ndinali wankhanza, anthu onse a m’gululi ankandipatsa ulemu. Paliponse ndinkakhala ndi mfuti moti usiku, inkakhala ili pansi pa pilo. Zinthu monga chiwawa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuba, kutukwana komanso kuchita chiwerewere, zinali kudya kwanga. Apolisi ankangokhalira kundisakasaka ndipo ndinali kabwerebwere wa kundende.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Nthawi ina nditatuluka kundende, ndinapita kukaona mayi anga aang’ono. Sindinkadziwa kuti iwowo komanso ana awo awiri anali atakhala a Mboni za Yehova. Tsiku lina, anandipempha kuti ndipite nawo ku misonkhano yawo ku Nyumba ya Ufumu. Ndinapitadi, n’cholinga choti ndikangoona kuti kumachitika zotani. Titafika, ndinaumirira kukhala pafupi ndi khomo n’cholinga choti ndiziona aliyense wolowa ndi wotuluka. Ndipotu mfuti yanga ija inali ili pambali panga.
Zimene zinachitika kumsonkhanowu zinasintha moyo wanga. Ndinkangoona ngati ndili m’dziko lina. Anthu onse anali osangalala ndi aubwenzi ndipo anandipatsa moni mwansangala. Anthuwa ankaonekanso kuti anali okoma mtima komanso achikondi chopanda mpeni kumphasa. Zimenezi zinali zachilendo kwambiri kwa ine.
Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Zimene ndinkaphunzira zinandithandiza kuona kuti ndiyenera kusintha moyo wanga. Mwachitsanzo, ndinazindikira kuti ndiyenera kusiya kucheza ndi anthu a m’gulu la zigawenga lija. Choncho ndinatsatira malangizo a palemba la Miyambo 13:20 akuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Kuchita zimenezi sinali nkhani yophweka, komabe Yehova anandithandiza moti ndinasiyadi kucheza nawo.
Ndinayamba kudziletsa kuchita zinthu zoipa
Koma panalinso zinthu zambiri zimene ndinkafunika kusintha. Mwachitsanzo, ndinayesetsa mpaka ndinasiya kusuta fodya komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndinametanso tsitsi langa lomwe linali lalitali, ndinasiya kutukwana, kuvala ndolo ndiponso ndinayamba kudziletsa kuchita zinthu zoipa.
Mwachibadwa sindinkakonda kuwerenga komanso kuphunzira, choncho zinkandivuta kwambiri kuwerenga Baibulo komanso kumvetsa zimene ndikuwerengazo. Komabe ndinachita khama ndipo ndinaona kuti zimenezi zinandithandiza kuti ndiyambe kukonda Yehova. Ndinaonanso kuti zomwe ndinkawerengazo zinayamba kusintha moyo wanga moti ndinayamba kuona kufunika kochita zabwino. Nthawi zambiri ndinkakhala ndi maganizo oti mwina Yehova sangandikhululukire zinthu zoipa zomwe ndinachita. Koma ndinkaganizira nkhani ya Mfumu Davide, yemwe anachita machimo akuluakulu ndipo atalapa, Yehova anamukhululukira. Zimenezi zinkandilimbitsa mtima ndipo ndinkaona kuti nanenso Yehova angathe kundikhululukira.—2 Samueli 11:1–12:13.
Chinthu china chomwe chinandivuta kwambiri kuchita, ndi kulalikira kunyumba ndi nyumba limodzi ndi a Mboni anzanga. (Mateyu 28:19, 20) Ndinkaopa kuti mwina ndingakumane ndi anthu amene m’mbuyomo ndinawachitira zoipa. Koma patapita nthawi ndinasiya kuchita mantha ndipo ndinkalalikira mosavuta. Ndinkasangalala kwambiri kuthandiza anthu kuphunzira zokhudza Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wokhululuka.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Ndikuona kuti kuphunzira za Yehova kwapulumutsa moyo wanga. Anzanga ambiri akale aja ali m’ndende ndipo ena anamwalira, koma ineyo ndine wosangalala komanso ndili ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Ndaphunzira kukhala wodzichepetsa, womvera komanso wodziletsa. Zimenezi zathandiza kuti ndizikhala bwino ndi anthu. Ndinakwatira mkazi wokongola, dzina lake Carmen, ndipo banja lathu ndi losangalala kwambiri. Ine ndi mkazi wangayu timasangalala kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo.
Panopa ndimapitanso kubanki, osati kukaba koma kukagwira ntchito yoyeretsa m’bankimo.