Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi angelo amathandiza anthu masiku ano?

Angelo anathandiza Danieli yemwe anali mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Masiku anonso angelo amathandiza anthu kuti amve uthenga wabwino

Yehova analenga angelo mamiliyoni ambirimbiri asanalenge anthu. (Yobu 38:4, 7) Angelo ndi amphamvu kwambiri ndipo amatumikira Mulungu. Nthawi zina Mulungu amawagwiritsa ntchito potsogolera komanso poteteza atumiki ake padziko lapansi. (Salimo 91:10, 11) Masiku ano, angelo amathandiza anthu kudziwa za uthenga wabwino umene otsatira a Yesu amalalikira.—Werengani Chivumbulutso 14:6, 7.

Kodi tiyenera kupemphera kwa angelo kuti atithandize? Ayi, chifukwa tikamapemphera timakhala kuti tikulambira ndipo Yehova yekha ndi amene tiyenera kumulambira. (Chivumbulutso 19:10) Popeza angelo ndi atumiki a Mulungu, iwo amachita zinthu zimene Mulungu wawauza osati zimene anthu awapempha. Choncho, nthawi zonse tiyenera kupemphera kwa Mulungu kudzera mwa Yesu.—Werengani Salimo 103:20, 21; Mateyu 26:53.

Kodi pali angelo ena oipa?

Mofanana ndi anthu, angelo analengedwa ndi ufulu wosankha zochita, ndipo akhoza kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti angelo ena anasankha kusamvera Mulungu. (2 Petulo 2:4) Mngelo woyamba kusamvera anali Satana, ndipo kenako angelo enanso anamutsatira ndipo anakhala ziwanda. Patapita nthawi, Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi.—Werengani Chivumbulutso 12:7-9.

Zinthu zoipa komanso zachiwawa zakhala zikuwonjezeka padzikoli kuyambira 1914. Zimenezi ndi umboni woti Mulungu awononga Satana ndi ziwanda zake posachedwapa.Kenako Mulungu adzakonzanso dzikoli n’kukhala paradaiso.—Werengani Chivumbulutso 12:12; 21:3, 4.