NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?
Kuda Nkhawa Chifukwa cha Mavuto a M’banja
Janet ananena kuti: “Patangopita nthawi yochepa bambo anga atamwalira, mwamuna wanga anandiuza kuti akufuna kukwatira mkazi wina. Kenako anangotenga zovala zake n’kundisiya ndi ana athu awiri osatsanzika n’komwe.” Janet anapeza ntchito koma ankalandira ndalama zochepa moti sankakwanitsa kusamalira ana ake bwinobwino. Janet anakumana ndi mavuto enanso ambiri. Iye anati: “Ndinayamba kuda nkhawa kwambiri poganizira kuti ndili ndi udindo waukulu wolera ndekha ana. Ndinkadziimba mlandu chifukwa ndinkaona kuti ndikulephera kusamalira ana anga ngati mmene makolo ena amachitira. Ndipo ngakhale panopa ndimadabe nkhawa ndi mmene anthu amaonera ineyo ndi ana anga. Ndimaganiza kuti ena samandimvetsa ndipo amaganiza kuti ndinapasula banja ndi manja anga.”
Janet amakonda kupemphera kwa Mulungu. Zimenezi zimamuthandiza kuti azikondabe Mulungu komanso asamade nkhawa mopitirira malire. Iye anati: “Ndimavutika kwambiri ndi nkhawa makamaka usiku chifukwa ana amakhala atagona ndipo zoganiza zimandichulukira. Koma kupemphera ndi kuwerenga Baibulo kumandithandiza kuti ndipeze tulo. Lemba limene limanditonthoza kwambiri ndi la Afilipi 4:6, 7, lomwe limati: ‘Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.’ Ndimakonda kupemphera usiku uliwonse ndipo ndimaona kuti Yehova amanditonthoza ndi kundipatsa mtendere.”
Pa Ulaliki wa Paphiri, Yesu ananena mawu olimbikitsa okhudza kupemphera omwe angathandize anthu onse amene ali ndi nkhawa. Iye anati: “Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:8) Ngakhale kuti Yehova amadziwa zimene tikufuna, tiyenera kumupemphabe chifukwa pemphero ndi njira yofunika kwambiri kuti ‘tiyandikire Mulungu.’ Tikatero nayenso ‘adzatiyandikira.’—Yakobo 4:8.
Pemphero limathandizanso m’njira zambiri. Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amathandiza anthu onse amene amamufunafuna ndi chikhulupiriro. (Salimo 65:2) Mpake kuti Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti “azipemphera nthawi zonse, osaleka.” (Luka 18:1) Choncho tisasiye kupempha Mulungu kuti azititsogolera ndi kutithandiza, ndiponso tisamakayikire kuti adzatipatsa mphoto chifukwa chakuti timamukhulupirira. Tizikhulupiriranso kuti amafunitsitsa kutithandiza tikakhala pamavuto. Timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba ‘tikamapemphera mosalekeza.’—1 Atesalonika 5:17.
KODI KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO KUMATANTHAUZA CHIYANI?
Kodi kukhulupirira Mulungu kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza “kudziwa” Mulungu kuti ndi weniweni. (Yohane 17:3) Kuti zimenezi zitheke tiyenera kudziwa maganizo a Mulungu, ndipo tingawadziwe tikamaphunzira Baibulo. Kuphunzira Baibulo kungatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona aliyense payekha ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Kukhala ndi chikhulupiriro sikutanthauza kungodziwa zinazake zokhudza Mulungu. Koma kumatanthauzanso kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima. Kuti munthu winawake akhale mnzathu wapamtima zimatenga nthawi yaitali. Mofanana ndi zimenezi, pamatenganso nthawi kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukule. Chikhulupiriro chathunso ‘chimawonjezeka’ tikamaphunzira za iye, tikamachita “zinthu zomukondweretsa” komanso tikamaona mmene akutithandizira. (2 Akorinto 10:15; Yohane 8:29) Chikhulupiriro chotere ndi chimene chinathandiza Janet pa nthawi imene anali ndi nkhawa.
Janet anati: “Kuona mmene Yehova wandithandizira pa zinthu zosiyanasiyana ndi kumene kwandithandiza kuti ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Nthawi zambiri tinkachitidwa zinthu zopanda chilungamo zimene tinkaona ngati sitingathe kuzipirira. Tikapemphera, Yehova ankatithandiza kuti zinthu ziyambenso kutiyendera bwino kuposa mmene tinkaganizira. Ndikamapemphera pandekha, ndimamuthokoza ndipo zimenezi zimandithandiza kukumbukira zinthu zabwino zimene watichitira. Nthawi zambiri amatithandiza pamene zinthu zatikoka manja ndipo tasoweratu mtengo wogwira. Yehova wandipatsanso anzanga enieni omwenso ndi atumiki ake. Iwo amandithandiza nthawi zonse ndipo ali ndi makhalidwe osiririka amene ana anga angatengere.” *
“Panopa ndikumvetsa chifukwa chimene pa Malaki 2:16, Yehova ananena kuti ‘ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.’ Kwa anthu okwatirana, wosalakwayo amakhala ngati wagwiritsidwa fuwa lamoto. Tsopano patha zaka zambiri ndithu kuchokera pamene amuna anga anandithawa, koma nthawi zina ndimasowabe wocheza naye ndipo ndimaona kuti ndine munthu wosafunika. Ndikayamba kudziona chonchi, ndimayesetsa kuthandiza winawake ndipo zimenezi zimachititsa kuti ndisinthe mmene ndimadzionera.” Janet amayesetsa kutsatira mfundo yopezeka m’Baibulo yakuti sibwino kudzipatula. Ndipo zimenezi zimamuthandiza kuti asamade nkhawa mopitirira malire. *—Miyambo 18:1.
Mulungu ndi “Tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu.”—Salimo 68:5
Janet anati: “Mawu akuti Mulungu ndi ‘tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu’ amandilimbikitsa kwambiri. Ndimadziwa kuti iye sangatisiye ngati mmene amuna anga anatisiyira.” (Salimo 68:5) Janet amadziwanso kuti Mulungu satiyesa “ndi zinthu zoipa” koma amapereka nzeru “mowolowa manja kwa onse” ndiponso amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tisamade nkhawa kwambiri.—Yakobo 1:5, 13; 2 Akorinto 4:7.
Kodi tingatani ngati tili ndi nkhawa chifukwa chakuti moyo wathu uli pangozi?
^ ndime 10 Kuti mupeze mfundo zina zokuthandizani mukakhala ndi nkhawa, onani nkhani ya pachikuto ya mutu wakuti, “Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?” mu Galamukani! ya July 2015 yomwe ili pa www.mt1130.com/ny.