Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nthawi Zina Mumaimba Mulungu Mlandu?

Kodi Nthawi Zina Mumaimba Mulungu Mlandu?

BAMBO wina wa ku Brazil, dzina lake Sidnei, anavulala kwambiri pamene ankachita masewera a pamtsetse moti panopa amagwiritsa ntchito njinga ya olumala. Nthawi zonse ankadzifunsa kuti, “Ndinalakwa chiyani? N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zindichitikire?”

Zinthu ngati ngozi, matenda, imfa ya munthu amene timamukonda, ngozi zachilengedwe kapenanso nkhondo zingachititse kuti anthu azivutika. Komanso zimenezi zingachititse kuti anthuwo aziimba Mulungu mlandu. Komatu zimenezi sizinayambe lero. M’mbuyomo, munthu wina dzina lake Yobu, anakumanapo ndi mavuto aakulu. Chifukwa cha mavutowa, Yobu anayamba kuimba Mulungu mlandu. Iye anati: “Ndimafuulira kwa inu kuti mundithandize, koma simundiyankha. Choncho ndaimirira kuti mundimvere. Mwasintha n’kukhala wankhanza kwa ine. Ndi mphamvu yonse ya dzanja lanu, mwandisungira chidani.”—Yobu 30:20, 21.

Yobu sankadziwa chimene chinkachititsa kuti akumane ndi mavuto. Komabe mosiyana ndi Yobu, Baibulo limatithandiza kudziwa chifukwa chake timavutika komanso zimene tingachite tikakumana ndi mavuto.

KODI MULUNGU ANACHITA KUKONZA KUTI TIZIVUTIKA?

Baibulo limanena za Mulungu kuti: “Ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” (Deuteronomo 32:4) Ndiyetu n’zosamveka kunena kuti Mulungu amene ndi “wolungama” komanso “wokhulupirika,” ndi amene anakonza zoti anthufe tizivutika. Ndipo zingakhalenso zosamveka kuti Mulungu atibweretsere mavuto ngati chilango kapena ngati njira yotiphunzitsira tikalakwitsa.

Ndipo mosiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri amaganiza, Baibulo limati: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Komanso, Baibulo limanena kuti Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola, momwe munali zonse zomwe ankafunikira komanso anawapatsa ntchito yabwino yoti azigwira. Kenako Mulungu anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” Choncho Adamu ndi Hava analibe chifukwa choimbira Mulungu mlandu chifukwa zonse zinali bwino.—Genesis 1:28.

Koma panopo zinthu zafika poipa kwambiri. Ndipotu kungoyambira kale anthu akhala akukumana ndi mavuto adzaoneni. Mpake kuti Baibulo limanena kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Koma kodi chinachitika n’chiyani kuti zinthu zifike pamenepa?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAVUTIKA?

Kuti tidziwe zimenezi, tiyeni tione zimene zinachitika m’munda wa Edeni. Satana Mdyerekezi amene poyamba anali mngelo wa Mulungu, ananyengerera Adamu ndi Hava n’kuwapangitsa kuti asamvere lamulo limene Mulungu anawapatsa. Mulungu anawauza kuti asadye “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Koma Satana anatsutsa zimenezo ndipo anawauza kuti ngati atadya zipatsozo, sadzafa koma adzafanana ndi Mulungu. Choncho apa tinganene kuti Satana ankanena kuti Mulungu ndi wabodza. Komanso zinakhala ngati akunena kuti Mulungu amapondereza ufulu wa anthu wosankha chimene akuona kuti n’chabwino kapena choipa. (Genesis 2:17; 3:1-6) Satana anasonyezanso kuti zinthu zikhoza kumayenda bwino ngati anthu atamadzilamulira okha. Zimenezi zinayambitsa nkhani yaikulu kwambiri. Nkhani yake inali yofuna kudziwa amene ali woyenera kulamulira.

Kenako Satana anayambitsanso nkhani ina. Ananena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Ponena za Yobu, Satana anauza Mulungu kuti: “Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo? Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. . . . Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!” (Yobu 1:10, 11) Ngakhale kuti m’nkhaniyi Satana anatchula Yobu, komabe iye ankatanthauza kuti munthu aliyense amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera.

KODI MULUNGU ANATANI KUTI ATHETSE NKHANIYI?

Kodi nkhani imeneyi ikanathetsedwa bwanji? Popeza Mulungu ndi wanzeru kuposa aliyense, anasankha njira yabwino yothetsera nkhaniyi. Njira imene anasankhayi imatithandizanso kuti tisamamuimbe mlandu. (Aroma 11:33) Mulungu analola kuti anthu azidzilamulira okha n’cholinga choti pakadzapita nthawi, woyenera kulamulira adzadziwike.

Mavuto amene tikukumana nawo masiku ano ndi umboni wosonyeza kuti anthu alephereratu kudzilamulira. Maboma a anthu alephera kukhazikitsa mtendere, kuthandiza kuti anthu azisangalala, ndipo awonongeratu dzikoli. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathandize anthu kukhala mwamtendere komanso mosangalala. Ndipo mtsogolomu anthu adzakhaladi mosangalala chifukwa zimenezo ndi zimene Mulungu amafuna.—Yesaya 45:18.

Koma kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto amene tikukumana nawo panopa? Paja Yesu anauza otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Choncho Mulungu adzathetsa mavuto onse padzikoli pogwiritsa ntchito Ufumu wake. (Danieli 2:44) Mavuto monga umphawi, matenda komanso imfa, zidzakhala mbiri yakale. Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu “adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,” zomwe zikusonyeza kuti umphawi sudzakhalakonso. (Salimo 72:12-14) Komanso limanena kuti: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Nanga bwanji anthu amene anamwalira? Yesu ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka. Amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo. Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” (Yohane 5:28, 29) Imeneyotu idzakhala nthawi yabwino kwambiri.

Tikamakhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa zimene anatilonjeza, zimatithandiza kukhala osangalala komanso kuti tisamamuimbe mlandu

KODI MUNGATANI KUTI MUSAMAIMBE MULUNGU MLANDU?

Patapita zaka 17 chichitireni ngozi, Sidnei amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino anati: “Sikuti ndinkaona kuti Mulungu ndiye anachititsa kuti ndivulale pa ngozi ija, komabe ndinkamuimba mlandu wolola kuti zimenezi zindichitikire. Nthawi zina ndimakhala wokhumudwa ndipo ndimalira ndikaganizira kuti panopo ndine wolumala. Komabe ndinaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti ngozi imene inandichitikira sichinali chilango chochokera kwa Mulungu. Ndipotu Baibulo limaphunzitsa kuti ‘nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimatigwera tonse.’”—Mlaliki 9:11; Salimo 145:18; 2 Akorinto 4:8, 9, 16.

Tikadziwa chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika komanso mmene adzachotsere mavutowa, zimatichititsa kuti tisamamuimbe mlandu. Sitikayikira kuti Mulungu ‘adzapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.’ Palibe munthu aliyense amene amakhulupirira Mulungu komanso Mwana wake amene adzagwire fuwa lamoto.—Aheberi 11:6; Aroma 10:11.