Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mary_Ukraine/stock.adobe.com

KHALANI MASO

Anthu Ayamba Kusiya Kukhulupirira Andale—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Anthu Ayamba Kusiya Kukhulupirira Andale—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 M’mayiko osiyanasiyana padziko lonse, muchitika zisankho m’chaka cha 2024. Komabe, anthu ambiri ayamba kusiya kukhulupirira anthu andale.

  •   Anthu ambiri a ku America omwe anayankha nawo mafunso pa kafukufuku wina ananena kuti “andale ambiri amafuna kukhala pa udindo ndi zolinga zadyera” m’malo modzipereka kuti athandize anthu onse.” a—Pew Research Center, September 19, 2023.

 Achinyamata ambiri asiya kukhulupirira anthu andale.

  •   “Masiku ano achinyamata amakonda kudera nkhawa kwambiri zopeza njira zothetsera mavuto, koma akafunsidwa mafunso pa kafukufuku wokhudza zandale akumayankha kuti andale sakutha kupeza njira zothetsera mavuto.”—The New York Times, January 29, 2024.

  •   “Kafukufuku wina akusonyeza kuti achinyamata akumakhulupirira anthu amene akumaposita mavidiyo pa intaneti kuposa mmene amakhulupirira andale.”—The Korea Times, January 22, 2024.

 Kodi tiyenera kukhulupirira kuti andale angathe kukonza zinthu kuti tsogolo lathu likhale labwino? Kodi tiyenera kukhulupirira ndani?

Muzisamala ndi anthu omwe mumawakhulupirira

 Ndi bwino kuti anthu azisamala ndi anthu omwe amawakhulupirira. Baibulo limanena kuti “munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—Miyambo 14:15.

 Komanso, ngakhale andale ataoneka kuti ndi oona mtima komanso ali ndi zolinga zabwino, sangakwanitse kuchita zonse zimene akufuna. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti:

  •   “Musamakhulupirire anthu olemekezeka kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.”—Salimo 146:3.

Mtsogoleri yemwe mungamukhulupirire

 Baibulo limafotokoza kuti Mulungu wasankha mtsogoleri wodalirika kwambiri, Yesu Khristu. (Luka 1:32, 33) Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma lomwe likulamulira kumwamba.—Mateyu 6:10.

a Pew Research Center, “Americans’ Dismal Views of the Nation’s Politics,” September 2023.