Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?

Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?

 M’mayiko ambiri, anthu akhala akuchita ziwonetsero chifukwa chosakhutira ndi mmene maboma awo akuyendetsera chuma. Vutoli linawonjezeka ndi mliri wa COVID-19 umene unachititsa anthu ambiri kukhala okwiya chifukwa cha ziletso zaboma, kusowa kwa zinthu, komanso kulephera kulandira chithandizo chamankhwala. Zonsezi zinachititsa kuti kusiyana pakati pa anthu olemera ndi osauka kukule kwambiri.

 Kodi mavuto azachuma amene anthu akuvutika nawo padziko lonseli adzatha? Inde adzatha. Baibulo limatiuza zimene Mulungu adzachite kuti athetse mavuto amene tikukumana nawowa.

Mavuto azachuma amene Mulungu adzathetse

 Vuto: Anthu alephera kuyendetsa chuma mokomera aliyense.

 Mmene vutoli lidzathere: Mulungu adzachotsa maboma a anthu kuti alowedwe m’malo ndi boma lake, limene limatchedwa Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu udzalamulira dziko lonse kuchokera kumwamba.—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.

 Zotsatira zake: Chifukwa chakuti Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi, udzayendetsa bwino kwambiri zochitika zapadzikoli. Anthu sadzakhalanso pa umphawi kapena kusowa zinthu zofunika pa moyo.(Salimo 9:7-9, 18) M’malomwake, adzasangalala ndi ntchito ya manja awo, n’kumakwanitsa kupeza zonse zofunikira kuti azikhala moyo wosangalala ndi mabanja awo. Baibulo linalonjeza kuti: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

 Vuto: Anthu sangapewe zinthu zimene zimabweretsa mavuto ndi umphawi.

 Mmene vutoli lidzathere: Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuthetsa zinthu zonse zimene zimachititsa anthu kukhala ndi mantha komanso nkhawa.

 Zotsatira zake: Mu Ufumu wa Mulungu simudzachitikanso zinthu zimene zimapangitsa anthu kupezeka kuti alibe zinthu zofunikira pa moyo wawo kapena wamabanja awo. Mwachitsanzo, sikudzakhalanso nkhondo, kuperewera kwa zakudya, ndi miliri. (Salimo 46:9; 72:16; Yesaya 33:24) Mulungu akulonjeza kuti: “Anthu anga adzakhala pamalo amtendere ndi pamalo otetezeka. Adzakhala m’malo abata ndiponso aphee!”—Yesaya 32:18.

 Vuto: Anthu odzikonda ndiponso adyera amadyera anzawo masuku pamutu.

 Mmene vutoli lidzathere: Anthu olamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu adzaphunzira kukonda anzawo kuposa mmene amadzikondera okha.—Mateyu 22:37-39.

 Zotsatira zake: Mu Ufumu wa Mulungu, aliyense azidzasonyeza chikondi ngati cha Mulungu, chimene “sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:4, 5) Baibulo limati: “Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera, chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova a ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Yesaya 11:9.

 Baibulo limafotokoza kuti panopa tikukhala m’masiku otsiriza a nthawi yathu ino ndipo posachedwa Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake n’kuthetsa mavuto onse azachuma. b (Salimo 12:5) Koma pakadali panopa, mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kulimbana ndi mavuto azachuma amene mukukumana nawo. Mwachitsanzo, onani nkhani zakuti “Kodi Mungasamale Bwanji Ndalama Zochepa Zimene Mumapeza?” komanso “Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?

a Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.

b Kuti mudziwe chifukwa chimene mungakhulupirire Baibulo, onani nkhani yakuti “Baibulo ndi Lodalirika Ndipo Limatiuza Choonadi.