Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Udzu wamera pamalo omwe anauma chifukwa chotentha.

KHALANI MASO

Ng’amba Yoopsa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Ng’amba Yoopsa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  •   “Dziko la China lati ‘chaka chino chakhala chotentha kwambiri komanso kwachitika ng’amba yoopsa yomwe siinachitikepo ndi kale lonse.’”—The Guardian, September 7, 2022.

  •   “Tsopano zaka 5 zikutha pomwe mayiko a ku Africa akupitirizabe kulimbana ndi ng’amba yoopsa.”—UN News, August 26, 2022.

  •   “Pali chiopsezo choti kukhala ng’amba m’mayiko ambiri a ku Europe. Ng’ambayi ikuyembekezeka kukhala yoopsa kwambiri pa ng’amba zonse zomwe zachitikapo m’zaka 500 zapitazi.”—BBC News, August 23, 2022.

 Akatswiri ambiri akunena kuti ng’ambazi zipitirira komanso zifika poipa kwambiri. Kodi tingayembekezere kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo? Kodi Baibulo limanena zotani?

Zomwe Baibulo Linaneneratu Zokhudza Ng’amba

 Zomwe Baibulo linaneneratu zokhudza masiku athu ano:

  •   “Kudzakhala . . . njala m’malo osiyanasiyana.”Luka 21:11.

 Nthawi zambiri ng’amba imachititsa kuti chakudya chisowe. Choncho kusowa kwa chakudyako, kuvutika komanso imfa zomwe zimabwera chifukwa cha njala, zimakwaniritsa ulosi wa m’Baibulo.—Chivumbulutso 6:6, 8.

Chifukwa chake mavuto a ng’amba akukulirakulirabe

 Baibulo limafotokoza chifukwa chenicheni chimene chikuchititsa kuti mavuto a ng’amba azikulirakulirabe. Limati:

  •   “Munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake.”Yeremiya 10:23.

 Zimenezi zikutanthauza kuti anthufe sitingathe ‘kudziwongolera’ bwinobwino kapena kuti kudzilamulira tokha. Kulephera kuyendetsa zinthu bwino kumeneku n’kumene kukuchititsa ng’amba komanso kusowa kwa madzi.

  •   Asayansi ambiri akuvomereza kuti zochita za anthu ndi zomwe zikuchititsa kuti dzikoli lizitentha kwambiri. Ndipo kutenthaku kukuchititsa kuti kulikonse padzikoli kukhale ng’amba.

  •   Anthu adyera komanso anthu omwe amakhazikitsa malamulo popanda kuganizira za m’tsogolo, akuchititsa kuti nkhalango komanso zinthu zina zam’chilengedwe ziwonongeke. Iwo akuchititsanso kuti anthu azigwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe molakwika. Chifukwa cha zimenezi madzi ambiri akuphwa.

 Komabe, chosangalatsa n’choti Baibulo limatipatsa chiyembekezo.

Kodi tingayembekezere kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo?

 Baibulo limatilonjeza kuti Mulungu adzathetsa mavuto akusowa kwa madzi. Kodi iye adzathetsa bwanji mavutowa?

  1.  1. Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Iye adzachotsa anthu oipa komanso adyera omwe akuwononga chilengedwe. (2 Timoteyo 3:1, 2) Paja zochita za anthuwa ndi zinanso zomwe zikuchititsa kuti chilengedwe chisokonekere.

  2.  2. “Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi.” (Yesaya 35:1, 6, 7) Mulungu adzakonza malo onse omwe anawonongeka chifukwa cha ng’amba. Iye adzasandutsanso dzikoli kukhala paradaiso ndipo sikudzakhalanso vuto la kusowa kwa madzi.

  3.  3. “Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka, mwalilemeretsa kwambiri.” (Salimo 65:9) Mulungu adzadalitsa dzikoli ndipo kulikonse kudzakhala chakudya chabwino chochuluka komanso madzi aukhondo okwanira aliyense.