Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Zothandiza Powerenga Baibulo

Njira Zothandiza Powerenga Baibulo

Baibulo lili ndi mfundo zothandiza kwambiri. Mukamaliwerenga ndi kuganizira mwakuya zimene mwawerengazo, komanso kugwiritsa ntchito zomwe mwaphunzirazo, mudzakhala “ndi moyo wopambana.” (Yoswa 1:8; Salimo 1:1-3) Mudzamudziwanso bwino Mulungu ndi Mwana wake Yesu ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti mudzapulumuke.​—Yohane 17:3.

Kodi mungakonde kutsatira ndondomeko iti powerenga Baibulo? Pamenepatu mungasankhe. Ndandanda yowerengera Baibuloyi ikuthandizani kuti muwerenge Baibulo potsatira ndondomeko ya mmene mabuku ake alili kapena potsatira nkhani zomwe mwasankha. Mwachitsanzo, mutha kuwerenga nkhani zokuthandizani kukhala ndi chithunzi cha mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi Aisiraeli. Mutha kuwerenga mbali zina za Baibulo kuti mudziwe mmene mpingo wachikhristu unayambira komanso mmene unakulira. Mukamawerenga machaputala omwe agawidwa kalewo tsiku lililonse, mutha kumaliza kuwerenga Baibulo lonse chaka chimodzi.

Ndandandayi ingakuthandizeni kwambiri kaya mukufuna kumangowerenga Baibulo tsiku lililonse, kukhala ndi cholinga chomaliza kuwerenga Baibulo chaka chimodzi kapena kutsatira ndondomeko yowerengera Baibulo ya anthu omwe angoyamba kumene. Pangani dawunilodi ndandanda yowerengera Baibulo, ndipo yambani lero.