Nyimbo 146
Munachitira Ine Amene
-
Nkhosa zina zomwe Yesu ali nazo,
zimatumikira ndi odzozedwa.
Zomwe nkhosa zina
zingawachitire
Yesu adzawabwezeratu zonse.
(KOLASI)
“Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.
Zonse zimene munawachitira
munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira.
munachitiranso ine amene.”
-
“Pamene ndinali wanjala, waludzu,
munandithandiza mwamsanga ndithu.”
“Mbuye, tinachita
liti zimenezi?”
Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:
(KOLASI)
“Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.
Zonse zimene munawachitira
munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira.
munachitiranso ine amene.”
-
“Zabwino mwachita mokhulupirika,
polalikira ndi abale anga.”
Choncho mfumuyo
idzauza nkhosazo:
“Landirani dziko, moyo wangwiro.”
(KOLASI)
“Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.
Zonse zimene munawachitira
munachitiranso ine amene.
Zonse zomwe munawachitira.
munachitiranso ine amene.”
(Onaninso Miy. 19:17; Mat. 10:40-42; 2 Tim. 1:16, 17.)