Ndikukhulupirireni
Pangani Dawunilodi:
1. Ngati mtengo wodzalidwa,
Ndi mmene mawuwa
Achitira mumtimamu, ndapeza mtendere.
Chiyeso chingabwere,
Koma ndimakumbuka,
Nzeru yochoka kumwamba yandithandiza
(KUKONZEKERA KOLASI)
Kuti ndisaope.
Ndiyembekeze Yehova.
(KOLASI)
Mavuto ndapirira,
Ndalimba ndi mawuwa.
Tsiku ndi tsiku ndikhulupirire inu.
2. Mayesero akhoza
Kundifooketsadi,
Ndimakumbukira kuti muli nane
Ndikamaganizira—
Ndimasunga mawuwa
Mumtima kuti anditsogoleredi—
(KUKONZEKERA KOLASI)
Kuti ndisaope.
Ndiyembekeze Yehova.
Mavuto, ndipirire ndithu.
Ndiziganizira za mphoto.
(KOLASI)
Mavuto ndapirira,
Ndalimba ndi mawuwa.
Tsiku ndi tsiku ndikhulupirire inu—
Inu.
(KUKONZEKERA KOLASI)
Kuti ndisaope.
Ndiyembekeze Yehova.
Mavuto, ndipirire ndithu.
Ndiziganizira za mphoto.
(KOLASI)
Mavuto ndapirira,
Ndalimba ndi mawuwa.
Tsiku ndi tsiku ndikhulupirire inu.