Ntchito Zanu N’zodabwitsa
Pangani Dawunilodi:
1. Ntchito za ufumu zadziwikadi konse,
Mwaphunzitsa cho’nadi kuyambira m’mbuyo monse.
Kapolo wanu wanzeru, amawunikira
Amandipatsa ‘busawa ondilimbikitsa.
Zomwe timadikira zimachitikadi.
Msonkhanotu uliwonse, umaposa yonse!
Mlungu uliwonse timaphunzira za inu
Ndiponso kulalikira anthu kulikonse.
(KOLASI)
Ntchito zanu zonse
N’zodabwitsadi Yehova.
Ufumu wayamba,
Ndipo timazindikira ndinudi Mulungu.
Tikudikira Madalitso a ufumuwu.
2. Mwatilemekeza pogwira nanu ntchito.
Ndi utumikiwu timasonyeza chikondi.
Mwatipatsa mtendere, tadziwanso zozama
Zimathandiza kukhala anthu abwinodi.
Ndikamvera nyimbo zathu ndimamva bwino
Kulambira kwa pabanjanso n’kothandizadi.
Ubale wathu padziko lonse ukutheka,
Izi n’zochititsa chidwi, n’zosowa m’dzikoli.
(KOLASI)
Ntchito zanu zonse
N’zodabwitsadi Yehova.
Ufumu wayamba,
Ndipo timazindikira ndinudi Mulungu.
Tikudikira Madalitso a ufumuwu.