Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Salowerera Ndale?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Salowerera Ndale?

 A Mboni za Yehova salowerera ndale chifukwa cha mfundo za m’Baibulo zimene amakhulupirira. Sitisapota chipani kapena munthu aliyense, sitichita zinthu zofuna kusintha malamulo, sitiponya nawo mavoti posankha zipani kapena olamulira, ndiponso sitipikisana nawo pa zisankho kapena kuchita nawo zinthu zilizonse zofuna kusintha boma. Pali zifukwa zomveka zochokera m’Baibulo zimene timachitira zimenezi.

  •   Timatsanzira chitsanzo cha Yesu yemwe anakana udindo wandale. (Yohane 6:15) Iye anauza ophunzira ake kuti asakhale “mbali ya dziko” ndipo anafotokoza momveka bwino kuti sayenera kulowerera ndale.​—Yohane 17:14, 16; 18:36; Maliko 12:13-17.

  •   Tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu umene Yesu anaufotokoza pamene ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mateyu 24:14) Ndife anthu amene tikuimira Ufumu wa Mulungu ndipo tapatsidwa ntchito yolalikira za kubwera kwa ufumuwu. Choncho sitilowerera ndale m’mayiko osiyanasiyana ngakhalenso m’dziko limene tikukhala.​—2 Akorinto 5:20; Aefeso 6:20.

  •   Kusalowerera ndale kumatithandiza kukhala ndi ufulu wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu a zipani zandale zosiyanasiyana. Timayesetsa kuti zimene timalankhula komanso kunena zizisonyeza kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto padzikoli.​—Salimo 56:11.

  •   Ndife ogwirizana ndipo timapanga ubale wapadziko lonse lapansi chifukwa chakuti sitilowerera ndale. (Akolose 3:14; 1 Petulo 2:17) Izitu n’zosiyana ndi zimene zipembedzo zina zimachita polowerera ndale ndipo anthu awo amagawanika.​—1 Akorinto 1:10.

 Timalemekeza boma. Ngakhale kuti sitilowerera ndale, timalemekezabe boma limene likulamulira m’dziko limene tikukhala. Zimenezi zikugwirizana ndi lamulo la m’Baibulo lakuti: “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.” (Aroma 13:1) Timachita izi pomvera malamulo aboma, kupereka misonkho ndiponso timagwirizana ndi boma pa ntchito zachitukuko m’dziko. Sitichita nawo zinthu zosintha ulamuliro koma timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizipempherera “mafumu ndi anthu onse apamwamba,” makamaka ngati akuchita zinthu zimene zingakhudze ufulu wathu wolambira.​—1 Timoteyo 2:1, 2.

 Timalemekezanso ufulu wa anthu ena pa nkhani za ndale. Mwachitsanzo, sitichita chilichonse chosokoneza pa nthawi ya mavoti kapena kuletsa anthu kuvota.

 Kodi ndife anthu oyamba kusalowerera ndale? Ayi. Atumwi ndiponso Akhristu oyambirira sankalowerera ndale koma ankalemekeza boma. Buku lina linanena kuti: “Ngakhale kuti Akhristu oyambirira ankadziwa kuti ayenera kulemekeza olamulira a boma, iwo sankalowerera ndale.” (Beyond Good Intentions) Buku linanso linanena kuti Akhristu oyambirira “sankakhala pa udindo uliwonse wandale.”​—On the Road to Civilization.

 Kodi kusalowerera ndale kumasokoneza mtendere m’dziko? Ayi. Ndife anthu okonda mtendere ndipo akuluakulu aboma sayenera kuchita nafe mantha. Taganizirani lipoti limene bungwe lina ku Ukraine linatulutsa m’chaka cha 2001. Pofotokoza zokhudza kusalowerera ndale, lipotili linati: “Masiku ano anthu ena samvetsa chifukwa chimene a Mboni za Yehova salowerera ndale. Chimenechi n’chifukwa chachikulu chimene chinachititsa kuti a Mboni azizunzidwa ndi chipani cha Nazi komanso maboma ena ankhanza.” Ngakhale pa nthawi imene ankazunzidwa ndi ulamuliro wankhanza wa Soviet, a Mboni “ankamverabe boma. Iwo ankagwira ntchito mwakhama m’minda ndi m’mafakitale ndipo sankaopseza olamulira a boma.” Lipotili linamaliza ponena kuti masiku anonso zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira komanso kuchita “siziopseza chitetezo cha dziko komanso olamulira a boma.”