Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?

Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?

 Zimene zikhoza kuthandiza munthu kuti akhale wa Mboni za Yehova zinafotokozedwa ndi Yesu pa Mateyu 28:19, 20. Lembali likusonyeza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wophunzira wa Khristu, zomwe zikuphatikizapo kulankhula komanso kuchitira umboni zokhudza Yehova.

 Choyamba: Muyenera kuphunzira Baibulo. Yesu anauza otsatira ake kuti ‘akaphunzitse anthu kuti akhale ophunzira ake.’ (Mateyu 28:19, 20) M’Baibulo muli mfundo zimene Yesu anaphunzitsa komanso mfundo zina zambiri ndipo zonsezi zingakuthandizeni kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala. (2 Timoteyo 3:16, 17) Tingakonde kukuthandizani kuphunzira Baibulo kwaulere.​—Mateyu 10:7, 8; 1 Atesalonika 2:13.

 Chachiwiri: Muzichita zimene mwaphunzirazo. Yesu ananena kuti anthu amene akuphunzira ayeneranso ‘kusunga zinthu zonse zimene anatilamulira.’ (Mateyu 28:20) Izi zikusonyeza kuti muyenera kugwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo n’kusintha mmene mumaganizira komanso khalidwe lanu. (Machitidwe 10:42; Aefeso 4:22-29; Aheberi 10:24, 25) Munthu amene amachita zimenezi amafika pofuna kukhala wotsatira wa Yesu ndiponso kudzipereka kwa Yehova Mulungu.​—Mateyu 16:24.

 Chachitatu: Muyenera kubatizidwa. (Mateyu 28:19) Baibulo limasonyeza kuti munthu akabatizidwa zimakhala ngati akuikidwa m’manda. (Yerekezerani ndi Aroma 6:2-4) Zili choncho chifukwa tikabatizidwa zimakhala ngati moyo wathu wakale watha ndipo tayamba moyo watsopano. Choncho mukabatizidwa, mumakhala kuti mukulengeza kwa anthu onse kuti mwatsatira mfundo ziwiri zoyambirira zimene Yesu ananena ndipo mukupempha Mulungu kuti akuthandizeni kukhala ndi chikumbumtima choyera.​—Aheberi 9:14; 1 Petulo 3:21.

Kodi ndingadziwe bwanji kuti ndikuyenera kubatizidwa?

 Muyenera kukalankhula ndi akulu a mumpingo. Akuluwo adzaonetsetsa kuti mukudziwa chifukwa chake anthu amabatizidwa. Adzaonetsetsanso kuti mukutsatira zimene munaphunzira komanso kuti munadziperekadi kwa Mulungu mwa kufuna kwanu.​—Machitidwe 20:28; 1 Petulo 5:1-3.

Kodi nawonso ana a Mboni ayenera kutsatira mfundozi asanabatizidwe?

 Inde. Ifeyo timayesetsa kulera ana athu “m’malangizo a Yehova” mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Aefeso 6:4) Koma anawo akamakula amafunika kusankha okha kuti aziphunzira Baibulo, kukhulupirira zimene aphunzirazo ndiponso kuzitsatira. Akachita zimenezi m’pamene angayenerere kubatizidwa. (Aroma 12:2) Kunena zoona, aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhani yolambira Mulungu.​—Aroma 14:12; Agalatiya 6:5.