A Mboni Anathandiza Ana Ena ku Thailand Kuti Zinthu Ziziwayendera Bwino Kusukulu
Kuyambira mu December 2012, a Mboni za Yehova ku Thailand, anagwira ntchito yapadera yothandiza ana ena kuti zinthu ziziwayendera bwino kusukulu. A Mboni 20 anapita m’sukulu zonse za m’dera la Bangkok. Pasukulu iliyonse a Mboniwo ankakumana ndi oyang’anira ndipo ankapatsa aphunzitsi ndi ana asukulu magazini ya Galamukani! ya October 2012. Magaziniyi pachikuto chake panali mutu wakuti “Kodi mungatani Kuti Zizikuyenderani ku sukulu?”
Ntchitoyi itayenda bwino, a Mboni anakonza zoti magaziniyi igawidwe m’sukulu zonse za m’dzikoli. Patapita chaka ndi hafu, a Mboni anayendera sukulu zokwana 830 ndipo anapeza kuti ana asukulu ankafunitsitsa kulandira magaziniwo moti anakonza zoti magaziniwa asindikizidwenso. Poyamba ofesi ya ku Thailand inaodetsa makope 30,000 a magaziniyi. Koma chifukwa chakuti ana asukulu anawakonda kwambiri, panakonzedwa zoti magazini ena asindikizidwenso, moti magazini oposa 650,000 anagawidwa.
Aphunzitsi ndi akuluakulu a m’sukuluzo anaona kuti magaziniyi ndi yothandiza kwambiri moti mphunzitsi wina anati: “Magaziniyi ithandiza kwambiri ana asukulu kuti azigwirizana kwambiri ndi athu a m’banja lawo komanso kuti azidziwa zimene akufuna kudzachita akamaliza sukulu.” M’sukulu zina anakonza zoti magaziniyi iphatikizidwe pa mabuku amene anawo aziwaphunzira. Ndipo aphunzitsi a m’sukulu zina anakonza zoti azigwiritsa ntchito magaziniwo paphunziro lophunzitsa kuwerenga. Pa sukulu inanso aphunzitsi anauza ana a sukulu kuti alembe lipoti pogwiritsa ntchito nkhani ya m’magaziniyi ndipo amene analemba lipoti labwino kwambiri analandira mphoto.
Mtsikana wa pa sukulu ina anayamikira kwambiri magaziniyi atawerenga nkhani yakuti “Kuthana ndi Vuto la Kunenepa Kwambiri.” Iye ananena kuti anthu ambiri ali ndi vutoli koma anzake amaona kuti n’zochititsa manyazi kumakambirana za vutoli. Mtsikanayo anati: “Zikomo kwambiri chifukwa chotipatsa malangizo othandiza ndiponso osavuta kuwagwiritsa ntchitowa.”
Makolo nawonso anayamikira kwambiri magaziniyi moti mayi wina anauza a Mboni amene anafika panyumba yake kuti: “Magaziniyi ili ndi mfundo zoti zithandiza kwambiri mwana wanga kuti azikhoza kusukulu.”
Bambo Pichai Petratyotin, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Thailand anati: “Kuyambira kale magazini ya Galamukani! imakhala ndi mfundo za m’Baibulo zimene zimathandiza anthu. A Mboni za Yehova amaona kuti maphunziro ndi ofunika kwambiri n’chifukwa chake tinaona kuti magaziniyi tiipereke kwa aliyense kwaulere.”