Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Brasília, Brazil

15 OCTOBER 2024
BRAZIL

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Brazil Lagamula Kuti Odwala Ali Ndi Ufulu Wosankha Thandizo Lachipatala Limene Akufuna

Oweruza Onse Anagwirizana pa Milandu Iwiri Yokhudza a Mboni za Yehova

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Brazil Lagamula Kuti Odwala Ali Ndi Ufulu Wosankha Thandizo Lachipatala Limene Akufuna

Pa 25 September 2024, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Brazil linapereka chigamulo chosaiwalika choti wodwala ali ndi ufulu wokana kuikidwa magazi ndipo akhoza kusankha thandizo lina lachipatala losakhudzana ndi magazi. Khotili linagamulanso kuti Unduna wa Zaumoyo uyenera kuwonetsetsa kuti wodwala aliyense amene akukana kuikidwa magazi kaya pa zifukwa zayekha kapena chifukwa cha zimene amakhulupirira, ayenera kulandira thandizo lachipatala losakhudzana ndi magazi.

Chigamulochi chikukhudza milandu ya a Mboni za Yehova awiri a ku Brazil. Mu 2018, Mlongo Malvina Silva atakana kusaina chikalata chovomereza kuti aikidwe magazi pa nthawi imene ankafunika kuti amupange opaleshoni ya mtima, madokotalawo ananena kuti samupanga opaleshoniyo. Panadutsa zaka pafupifupi ziwiri kuti Mlongo Malvina alandire thandizo lachipatala logwirizana ndi zimene anasankha.

Mu 2014, M’bale Heli de Souza ankafunika kupangidwa opaleshoni. Koma chipatala cha m’dera lawo chinalibe zipangizo zokwanira kuti amupange opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Koma iye atapempha kuti amutumize kuchipatala china chomwe chinali chokonzeka kumupanga opaleshoniyo mogwirizana ndi zimene amakhulupirira, boma linakana pempho lakelo. Heli akudikirabe kuti apangidwe opaleshoni. A Mboni za Yehova ambiri a ku Brazil akukumananso ndi mavuto ofanana ndi amenewa kuphatikizapo kuikidwa magazi ngakhale eniakewo atanena kuti sakufuna kuikidwa magaziwo.

Mlongo Malvina Silva ndi M’bale Heli de Souza

Pamene ankapereka chigamulo, pulezidenti wa khotili, Justice Luís Roberto Barroso ananena kuti: “Ufulu wokana kuikidwa magazi potengera zimene munthu amakhulupirira ndi wogwirizana ndi mfundo za m’malamulo zokhudza ufulu wachibadwidwe ndi ufulu wachipembedzo. Choncho, ponena za ufulu wokhala ndi moyo komanso thanzi labwino, [a Mboni za Yehova] akuyenera ndipo ali ndi ufulu wosankha okha thandizo lina lachipatala losakhudzana ndi magazi.”

Makhoti ena onse a ku Brazil akuyenera kulemekeza chigamulo chatsopanochi choti aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha thandizo lachipatala lomwe angafune. Chigamulo chimenechi ndi chofanana ndi zigamulo zinanso zomwe zaperekedwa ndi makhoti akuluakulu m’mayiko ena monga, Australia, Canada, Japan, South Africa ndi United States. Chigamulo chimenechi chikufanananso ndi chimene Khoti Lalikulu Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linapereka pa 17 September 2024, chomwe chinanena kuti mayiko 46 a ku Europe akuyenera kumalemekeza ufulu wa wodwala pa nkhani yosankha thandizo lachipatala.

Pa nthawi yomwe mlanduwu unkazengedwa pa 25 September 2024

Ndife osangalala kwambiri kuti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Brazil lagamula mokomera aliyense kuti ali ndi ufulu wolandira thandizo lachipatala limene angafune potengera zimene amakhulupirira.