JULY 11, 2019
GREECE
Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Athens, Greece
Masiku: 5 mpaka 7 July, 2019
Malo: Athens Olympic Stadium ku Athens, Greece
Zinenero: Chiabaniya, Chingelezi, Chigiriki, Chinenero Chamanja cha ku Greece, Chiromane (cha kum’mwera kwa Greece), Chirasha
Chiwerengero cha Osonkhana: 36,873
Chiwerengero cha Obatizidwa: 406
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,000
Nthambi Zoitanidwa: Albania, Armenia, Australasia, Bulgaria, Central America, Central Europe, Fiji, Japan, Kyrgyzstan, North Macedonia, Turkey, United States
Zina Zomwe Zinachitika: Munthu wina yemwe amagwira ntchito yopanga dongosolo la maulendo a anthu anati: “Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa moyo wanga wonse koma sindinaonepo kulikonse padzikoli anthu opanga bwino dongosolo la anthu omwe ali paulendo ngati inuyo. Ndinagoma kwambiri ndi zimene ndinaona mukuchita dzulo. Munapanga dongosolo la mayendedwe la anthu 2,600 m’maola ochepa m’njira yabwino kwambiri kuposa anthu ambiri omwe ndi akatswiri pa ntchitoyi. Koma chinthu chosangalatsa kwambiri ndi kumwetulira kwanu. Zimene ndikunenazi n’zoona chifukwa ndagwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri ndipo ndimadziwa ngati munthu akungomwetulira chifukwa choti akufunika kutero pa ntchito yake kapena ngati akumwetulira zenizeni kuchokera mumtima. Koma nonsenu mumamwetulira kuchokera mumtima.”
Ena mwa abale ndi alongo oposa 4,000 ongodzipereka omwe anagwira ntchito yokonza sitediyamu pokonzekera msonkhano.
Achinyamata akulandira alendo omwe anabwera kumsonkhanowu ku Greece
Mmodzi mwa abale ndi alongo atsopano 406 akubatizidwa
Alongo olankhula Chiromane akujambulitsa pamalo a msonkhano. Umenewu unali msonkhano wa mayiko woyamba ku Greece womwe unachitikanso m’chinenero cha Chiromane
Alendo ali limodzi muutumiki ndi abale ndi alongo a ku Greece
Alendo akuona mabwinja akale a ku Greece
Akuchita sewero la m’Baibulo pa nthawi yomwe anthu anakumana pamodzi madzulo. Seweroli linali lofotokoza za utumiki wa Mtumwi Paulo ku Greece.
Abale ndi alongo akusonyeza alendo mmene amavinira gule wotchuka wa Syrtaki
Mlongo akuimba chida choimbira cha ku Greece chotchewa bouzouki
Alendo akuphunzira mawu a chinenero cha Chigiriki
M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani ya m’Baibulo yomaliza pa tsiku lachiwiri la msonkhano ndipo nkhaniyi inamasuliridwa mu Chigiriki
Abale ndi alongo omwe ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera akubayibitsa pa tsiku lomaliza la msonkhanowu