Mexico
A Mboni za Yehova Amtundu wa Huichol Anathamangitsidwa M’dera la Jalisco ku Mexico
Gulu la anthu linaukira a Mboni za Yehova n’kuwathamangitsa m’nyumba zawo. Abale anakadandaula nkhaniyi kwa akuluakulu a boma kuti awathandize.
A Mboni za Yehova ndi Okonzeka Kuyamba Ntchito Yomanganso Nyumba Zoonongeka ndi Chivomezi ku Guatemala ndi ku Mexico
A Mboni za Yehova ayamba ntchito yayikulu yothandiza a Mboni anzawo a ku Mexico ndi ku Guatemala amene anakhudzidwa ndi zivomezi ziwiri zomwe zinaononga kwambiri.
Boma Linathokoza a Mboni Chifukwa Chophunzitsa Akaidi ku Mexico
Akuluakulu a boma anathokoza Mboni za Yehova chifukwa chophunzitsa Baibulo akaidi a m’ndende za ku Baja California.
A Mboni za Yehova Anachita Nawo Chionetsero Chachikulu cha Mabuku a Chisipanishi
Pa chionetsero cha mabuku ku Guadalajara panaonetsedwa mabuku amene anthu amalemba kuzungulira dziko lonse ndiponso mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chinenero cha Chitsotsilu Linatulutsidwa ku Mexico
A Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu (Chipangano Chatsopano) la Chinenero cha Chitsotsilu. Chinenerochi chimayankhulidwa ndi anthu a mtundu wa Maya omwe amakhala m’madera okwera a chigawo chapakati ku Chiapas.
Akuluakulu a Mzinda wa Mexico Anathokoza a Mboni za Yehova Chifukwa Choyeretsa Bwalo la Masewera
Pa June 7 2014, a Mboni za Yehova oposa 250 anadzipereka kugwira ntchito yoyeretsa bwalo la masewera lotchedwa Baldomero “Melo” Almada, ndipo akuluakulu a boma anayamikira kwambiri zimene a Mboniwa anachita.