TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOBU
“Sindidzasiya Kukhala Ndi Mtima Wosagawanika.”
Munthu wina wakhala pansi atazyolika, ali ndi zilonda zopweteka kuchokera kumutu mpaka kuphazi. Mapewa ake ndi akugwa, ali yekhayekha ndipo alibenso mphamvu zothamangitsira ntchentche zomwe zikumusowetsa mtendere. Pofuna kusonyeza kuti akuvutika kwambiri, wakhala paphulusa ndipo akugwiritsa ntchito phale pokanda thupi lake la zilondalo. Poyamba anali munthu wolemekezeka koma panopa wasanduka munthu wachabechabe. Anzake komanso achibale ake anamuthawa. Aliyense kuphatikizapo ana akumamunyoza. Munthuyu akuganiza kuti Mulungu wake, Yehova, wamusiyanso. Komatu zimene akuganizazi n’zolakwika.—Yobu 2:8; 19:18, 22.
Munthu ameneyu ndi Yobu. Ponena za munthuyu Mulungu ananena kuti: “Palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi.” (Yobu 1:8) Ndipo patadutsa zaka, Yehova ankaonabe kuti Yobu anali mmodzi mwa amuna omwe anachita zinthu mwachilungamo.—Ezekieli 14:14, 20.
Ngati mukukumana ndi mavuto omwe mukuona kuti simungathe kuwapirira, nkhani ya Yobu ingakulimbikitseni kwambiri. Ingakuthandizeninso kumvetsa kufunika kokhala ndi mtima wosagawanika, khalidwe limene mtumiki wokhulupirika aliyense wa Mulungu ayenera kukhala nalo. Nthawi zambiri anthufe timasonyeza kuti tili ndi mtima wosagawanika tikakhalabe okhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene takumana ndi mavuto. Tiyeni tione zimene tingaphunzirepo pa nkhani ya Yobu.
Zimene Yobu Sankadziwa
Zikuoneka kuti patapita nthawi kuchokera pamene Yobu anamwalira, Mose yemwe anali mtumiki wokhulupirika ndi amene analemba nkhani ya Yobu. Mose anatsogoleredwa ndi mzimu woyera kulemba zinthu zomwe zinkachitika padziko lapansi pano zomwe zinakhudza moyo wa Yobu ndiponso zomwe zinkachitika kumwamba.
Nkhaniyi imasonyeza kuti poyamba Yobu ankakhala mosangalala. Anali wolemera, wotchuka ndipo ankalemekezedwa ndi anthu a ku Uzi, dziko lomwe mwina lili chakumpoto kwa Arabia. Iye anali wowolowa manja ndipo ankayesetsa kuthandiza osauka. Yobu ndi mkazi wake anali ndi ana 10. Ankakonda kwambiri Yehova kuposa chilichonse. Ankayesetsa kusangalatsa Mulungu ngati mmenenso anachitira abale ake ena monga Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Yosefe. Mofanana ndi anthu amenewa, nayenso Yobu anali ngati wansembe m’banja lake ndipo nthawi zonse ankapereka nsembe m’malo mwa ana ake.—Yobu 1:1-5; 31:16-22.
Koma zinthu zinasintha mosayembekezereka pa moyo wa Yobu. Tikamawerenga nkhani yake, timadziwa zomwe zinkachitika kumwamba komanso zomwe Yobu sakanatha kuzidziwa. Nkhaniyi imasonyeza kuti angelo okhulupirika a Yehova anasonkhana pamodzi ndipo kenako Satana, mngelo woukira, anafikanso. Yehova ankadziwa kuti Satana sakusangalala ndi Yobu yemwe anali munthu wokhulupirika. Ndiyeno anafotokozera Satana zokhudza kukhulupirika kwa Yobu. Koma Satana anayankha kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe? Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo? Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho.” Satana amadana ndi anthu okhulupirika. Choncho anthu akamatumikira Yehova Mulungu ndi mtima wonse, amapereka umboni wosonyeza kuti Satana alibe chikondi. Satana ananena kuti Yobu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera ndipo ngati katundu yense wa Yobu atawonongedwa, akhoza kutukwana Mulungu m’maso muli gwa!—Yobu 1:6-11.
Ngakhale kuti Yobu sankadziwa zomwe zikuchitika, Yehova anamudalira n’kumupatsa udindo waukulu woti asonyeze kuti Satana ndi wabodza. Satana analoledwa kuti achotse zonse zimene Yobu anali nazo kupatulapo moyo wake. Ndiyeno Satana anayamba kumubweretsera Yobu mavuto. Pa tsiku limodzi lokha Yobu anakumana ndi mavuto otsatizanatsatizana. Analandira uthenga woti ng’ombe, abulu, nkhosa ndiponso ngamila zaphedwa. Kuwonjezera pamenepo, abusa a ziwetozo nawonso anaphedwa. Pa anthu omwe ankapereka mauthengawa, munthu mmodzi anauza Yobu kuti chimene chapha nkhosa komanso abusa ake ndi “moto wa Mulungu,” ndipo n’kutheka kuti unali moto wa mphezi. Pa nthawiyi Yobu anali atasaukiratu ndipo asanaganize n’komwe zoti achite ndi anthu omwe afawo, panachitikanso zinthu zina zoimitsa mutu. Ana ake 10 akucheza m’nyumba ya m’bale wawo woyamba kubadwa, chimphepo chinawomba nyumbayo n’kuigwetseratu ndipo ana onsewo anafa.—Yobu 1:12-19.
N’zovuta kumvetsa tikaganizira mmene Yobu anamvera. Iye anang’amba zovala zake, anameta tsitsi lake ndipo kenako anagwada pansi. Yobu anayamba kunena kuti Mulungu anapereka ndipo Mulungu yemweyo watenga. Apa Satana anachititsa Yobu kuganiza kuti Mulungu ndi amene wamubweretsera mavutowo. Ngakhale zinali choncho, Yobu sanatukwane Mulungu monga mmene Satana ananenera. M’malomwake Yobu ananena kuti: “Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”—Yobu 1:20-22.
“Akutukwanani M’maso Muli Gwa!”
Satana anakwiya kwambiri moti sanasiye kumuyesa Yobu. Iye anapita kwa Yehova pa nthawi imene angelo anali ndi msonkhano. Pa nthawi imeneyinso Yehova anayamikira Yobu chifukwa cha mtima wake wosagawanika komanso chifukwa choti sanagonje pa mayesero onse amene Satanayo anamubweretsera. Satana anayankha mokwiya kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake. Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa.” Satana sankakayikira kuti ngati Yobu atadwala kwambiri, m’pamene angatukwane Mulungu. Popeza kuti Yehova ankamudalira kwambiri Yobu, analola kuti Satana amudwalitse, bola asamuphe.—Yobu 2:1-6.
Monga mmene tafotokozera kale kumayambiriro kuja, Yobu anakhala ndi zilonda thupi lonse. Pa nthawiyi mkazi wake anali wachisoni kwambiri chifukwa cha kumwalira kwa ana ake 10. Apa tsopano akuonanso mwamuna wake akumva ululu woopsa wa zilonda. Zimenezi zinamupweteka mumtima ndipo anafunsa Yobu kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala ndi mtima wosagawanika? Tukwanani Mulungu mufe.” Yobu sanayembekezere kuti mkazi wake yemwe ankamukonda komanso kumudziwa bwino, angalankhule zimenezi. Iye ananena kuti mkazi wakeyo walankhula ngati wopusa. Komabe, Yobu sanatukwane Mulungu ndipo sanachimwe.—Yobu 2:7-10.
Kodi mukudziwa kuti nkhaniyi ikukukhudzaninso inuyo? Sikuti Satana anangonenera zoipa Yobu yekha, koma mtundu wonse wa anthu. Iye ananena kuti: “Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” Apa Satana anasonyeza kuti amakayikira ngati anthufe tingamatumikiredi Yehova mokhulupirika. Iye amanena kuti inuyo simukonda Mulungu ndi mtima wonse ndipo mukhoza kusiya kumutumikira n’cholinga choti mupulumutse moyo wanu ngati mutakumana ndi mavuto. Tinganene kuti Satana amanena kuti ndinu wodzikonda ngati mmene iyeyo alili. Choncho kuti tisonyeze kuti zimene ananenazi ndi zabodza, aliyense payekha ayenera kuchitapo kanthu. (Miyambo 27:11) Tiyeni tione zinanso zomwe Yobu anakumana nazo.
Anzake Analephera Kumulimbikitsa
Amuna atatu omwe ankadziwana ndi Yobu anabwera kudzamuona ndipo Baibulo limanena kuti anthuwa anali anzake. Iwo anamva za mavuto omwe Yobu anakumana nawo ndipo anapita kukamulimbikitsa. Anzakewo atamuona chapatali analephera kumuzindikira chifukwa khungu lake linali litada ndi zilonda moti sankaonekanso ngati mmene analili poyamba. Amuna atatuwo, omwe ndi Elifazi, Bilidadi ndi Zofari anayamba kulira mokweza mawu komanso kuwaza fumbi pamwamba pa mitu yawo ponamizira kuti akumva chisoni kwambiri. Kenako anakhala pansi pambali pa Yobu koma sanalankhule chilichonse. Iwo anakhala pomwepo kwa mlungu umodzi wathunthu, usiku ndi usana, popanda kulankhula chilichonse. Apa sitinganene kuti amuna atatuwo anakhala chete pofuna kulimbikitsa Yobu popeza kuti sanamufunse chilichonse koma anangoona kuti Yobu akumva ululu waukulu.—Yobu 2:11-13; 30:30.
Kenako Yobu anangoyamba yekha kulankhula. Posonyeza kuti ankamva ululu waukulu, anatemberera tsiku limene anabadwa. Anafotokozanso chifukwa chachikulu chomwe chinachititsa kuti azizunzika kwambiri. Iye ankaganiza kuti Mulungu ndi amene wamubweretsera mavuto onsewo. (Yobu 3:1, 2, 23) Ngakhale kuti Yobu sanasiye kukhala wokhulupirika, ankafunikabe kulimbikitsidwa. Koma anzake aja atayamba kulankhula, Yobu anaona kuti zikanakhala bwino akanangokhalabe chete chifukwa sankalankhula zolimbikitsa.—Yobu 13:5.
Elifazi, yemwe n’kutheka kuti anali wamkulu kwa Yobu ndi amene anayamba kulankhula. Patapita nthawi, anzake awiri aja analankhulaponso. Tinganene kuti zimene anzakewa analankhula anatengera zomwe Elifazi ananena. Ndipo zina zomwe ankanena zinkaoneka ngati zilibe vuto. Iwo ankagwiritsa ntchito mfundo zooneka ngati zochokera m’Malemba monga zoti Mulungu amakhala pamalo okwezeka, amalanga anthu oipa koma anthu abwino amawachitira zabwino. Amuna atatuwa atayamba kulankhula, zolankhula zawo zinkaoneka kuti sakumuganizira Yobu. Mwachitsanzo, zimene Elifazi ananena zinkaoneka ngati zomveka. Iye ananena kuti ngati Mulungu ndi wabwino koma amalanga anthu oipa, ndiye kuti Yobu akulangidwa chifukwa choti anachita zinazake zoipa.—Yobu 4:1, 7, 8; 5:3-6.
N’zosadabwitsa kuti Yobu sanagwirizane ndi zimene anzakewo ananena ndipo anatsutsa mwamphamvu. (Yobu 6:25) Koma anzake atatuwo ankakhulupirirabe kuti Yobu akubisa zoipa zinazake zomwe anachita ndipo ankaona kuti mpake kukumana ndi mavuto. Elifazi anaimba mlandu Yobu kuti anali munthu wodzikuza, woipa komanso wosaopa Mulungu. (Yobu 15:4, 7-9, 20-24; 22:6-11) Zofari anamuuza Yobu kuti asiye kuchita zoipa komanso kuti asamasangalale nazo. (Yobu 11:2, 3, 14; 20:5, 12, 13) Ndipo Bilidadi analankhulanso mawu opweteka kwambiri. Ananena kuti ana a Yobu anali atachita zinazake zochimwira Mulungu ndipo n’chifukwa chake anamwalira.—Yobu 8:4, 13.
Chikhulupiriro Chake Chinayesedwa
Amuna atatuwo analankhulanso zinthu zina zoipa kwambiri. Kuwonjezera pa kukayikira za kukhulupirika kwa Yobu, anasonyezanso kuti kukhala ndi mtima wosagawanika kulibe phindu. Mawu oyamba a Elifazi amasonyeza kuti mzimu wina wochititsa mantha unamuonekera. Zimene mzimu woipawo unanena zinachititsa Elifazi kukhulupirira mfundo yakuti Mulungu “sakhulupirira atumiki ake, ndipo angelo ake amawapezera zifukwa.” Mfundo yolakwikayi ikusonyeza kuti n’zosatheka anthufe kusangalatsa Mulungu. Kenako Bilidadi ananenanso kuti kukhulupirika kwa Yobu, Mulungu alibe nako ntchito ndipo amangomuona ngati mphutsi.—Yobu 4:12-18; 15:15; 22:2, 3; 25:4-6.
Kodi nthawi ina munalimbikitsapo munthu wina amene anali pa mavuto aakulu? Kuchita zimenezi si kophweka. Koma tingaphunzire zambiri pa zimene anzake atatu a Yobu anachita, makamaka zimene sitiyenera kulankhula. Ngakhale kuti zimene anzakewo ananena zinkaoneka ngati zothandiza, sizinali zolimbikitsa ndipo pa zonse zomwe analankhula sanatchulepo dzina la Yobu. Iwo sanaone kufunika kolimbikitsa Yobu yemwe anali pa mavuto aakulu komanso sanamulankhule mwachikondi. * Choncho inuyo mukaona kuti mnzanu ali ndi chisoni, muzisonyeza kuti mumamukonda ndipo muzimulankhula mokoma mtima. Muzimulimbikitsa kuti asasiye kukhala wolimba komanso kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu ndiponso kumudalira chifukwa Iye ndi wokoma mtima, wachifundo komanso wachilungamo. Zimenezi ndi zomwe Yobu akanachita zikanakhala kuti anzake atatuwo ndi omwe akumana ndi mavuto. (Yobu 16:4, 5) Koma kodi Yobu anatani anzakewo atakayikira za kukhulupirika kwake?
Yobu Anakhalabe Wolimba
Pamene anzake a Yobu ankayamba kulankhula naye, anali ali kale ndi chisoni chachikulu. Atangoyamba kulankhulana, Yobu anavomereza kuti zinthu zina zomwe analankhula zinali “zopanda pake” ndiponso zinali ngati za “munthu wopanda chiyembekezo.” (Yobu 6:3, 26) Ndipotu mpake kuti analankhula zoterezi chifukwa ankamva ululu mumtima mwake. Mawu amene analankhulawa anasonyezanso kuti sankadziwa chimene chinkachititsa kuti azikumana ndi mavuto. Popeza kuti mavuto omwe Yobu ndi banja lake anakumana nawo anachitika mwadzidzidzi, iye ankaganiza kuti Yehova ndi amene wachititsa. Panali zambiri zomwe Yobu sankadziwa chifukwa chake zikuchitika, n’chifukwa chake anayamba kuganiza molakwika.
Ngakhale zinali choncho, Yobu anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ndipo chikhulupiriro chakechi chinaonekera pa zimene ananena pamene anali ndi anzake aja. Zimene Yobu analankhula zinali zoona, zabwino komanso zolimbikitsa kwa tonsefe. Pa nkhani ya chilengedwe chodabwitsachi, Yobu analemekeza Mulungu pofotokoza zinthu zomwe palibe munthu amene akanatha kuzifotokoza popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, ananena kuti Yehova “anakoloweka dziko lapansi m’malere” ndipo panadutsa zaka zambiri kuti asayansi atulukire zimenezi. * (Yobu 26:7) Komanso pofotokoza za zimene ankayembekezera, Yobu anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chofanana ndi chomwe anthu enanso akale anali nacho. Iye ankakhulupirira kuti ngati atafa, Mulungu adzamukumbukira, adzalakalaka ntchito za manja ake ndipo kenako adzamuukitsa.—Yobu 14:13-15; Aheberi 11:17-19, 35.
Koma kodi nkhani ya kukhala ndi mtima wosagawanika ndi yofunika bwanji? Elifazi ndi anzake awiri aja ananena kuti Mulungu alibe nazo ntchito za kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi Yobu ankaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona? Ayi, Yobu ankaona kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kofunika kwambiri. Ponena za Yehova, iye ananena monyadira kuti: “Adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.” (Yobu 31:6) Ndipotu Yobu anazindikira kuti zinthu zabodza zomwe anzakewo ankanena, zinali zongofuna kusokoneza chikhulupiriro chake. Zimenezi zinamukhudza Yobu ndipo analankhula mawu ambiri moti anzake atatuwo sanalankhulenso chilichonse.
Yobu ankadziwa kuti ayenera kukhala wokhulupirika nthawi zonse. Ndipo zimenezi zinaonekera pa mmene ankachitira zinthu. Mwachitsanzo, Yobu ankapewa kulambira mafano kulikonse, ankalemekeza anthu komanso kuwachitira zinthu mokoma mtima, ankapewa makhalidwe oipa ndiponso ankakonda kwambiri banja lake. Koposa zonse, anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu woona yekha, Yehova. N’chifukwa chake Yobu ananena ndi mtima wake wonse kuti: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5; 31:1, 2, 9-11, 16-18, 26-28.
Tsanzirani Chikhulupiriro cha Yobu
Kodi inunso mumaona kuti kukhala wokhulupirika n’kofunika kwambiri ngati mmene Yobu anachitira? Kukhulupirika ndi mawu osavuta kutchula, koma Yobu anaona kuti kumafuna zambiri. Timasonyeza kuti ndife odzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu tikamamumvera ndiponso tikamachita zoyenera tsiku lililonse, ngakhale pamene takumana ndi mavuto. Tikamachita zimenezi, Yehova amasangalala nafe kwambiri ndipo amachititsa manyazi mdani wake, Satana, ngati mmene Yobu anachitira. Tikatero ndiye kuti tikutsanzira chikhulupiriro cha Yobu.
Komabe nkhani ya Yobu sinathere pomwepa. Iye anasiya kuona zinthu moyenera ndipo anayamba kudziikira kumbuyo n’kumadziona kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Mulungu. Apa Yobu ankafunika kuthandizidwa kuti ayambe kuona zinthu mmene Mulungu ankazionera. Pa nthawiyi Yobu anali akumvabe ululu waukulu komanso anali wachisoni moti ankafunitsitsa wina atamutonthoza. Ndiye kodi Yehova anayenera kuchita chiyani kwa munthu wokhulupirikayu yemwenso anali ndi mtima wosagawanika? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli?
^ ndime 23 Elifazi ankaganiza kuti iyeyo ndi anzakewo akulankhula mwachikondi kwa Yobu popeza kuti sankalankhula mokweza mawu. (Yobu 15:11) Komabe ngakhale munthu atamalankhula motsitsa, mawu akewo akhoza kukhalabe owawa.
^ ndime 26 Zimene tikudziwa n’zakuti patangodutsa zaka 3,000 zokha, asayansi anazindikira kuti palibe chifukwa choti dziko likolowekedwe pa chinthu chinachake. Asayansi sankadziwa zimenezi mpaka pamene anakajambula zithunzi mlengalenga zomwe aliyense ankatha kuziona n’kutsimikizira kuti zimene Yobu ananena ndi zoona.