Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
Yankho la m’Baibulo
Ayi. Baibulo silinena kuti ndalama ndi zoipa kapena kuti ndi zomwe zimabweretsa mavuto. Komabe, zimene anthu ambiri amakonda kunena zoti ndalama ndi muzu wa zoipa zonse, zimangosonyeza kuti samvetsa zimene Baibulo limafotokoza. Baibulo limanena kuti “muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.” a—1 Timoteyo 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau A Mulungu.
Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya ndalama?
Baibulo limanena kuti munthu akamagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru, zikhoza kumuthandiza komanso ‘kumuteteza.’ (Mlaliki 7:12) Ndipotu limayamikira anthu owolowa manja omwe amathandiza anzawo, kuphatikizapo kuwapatsa ndalama.—Miyambo 11:25.
Ngakhale zili choncho, Baibulo limatichenjezanso kuti tisamakonde kwambiri ndalama. Limanena kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” (Aheberi 13:5) Apa mfundo ndi yakuti m’malo momangosakasaka chuma, tizigwiritsa ntchito ndalama zimene tili nazo mwanzeru ndipo tizikhala okhutira ndi zinthu zomwe tapeza monga chakudya, zovala ndi pogona.—1 Timoteyo 6:8.
N’chifukwa chiyani Baibulo limati kukonda ndalama n’koipa?
Anthu a umbombo sadzapeza moyo wosatha. (Aefeso 5:5) Tikutero chifukwa umbombo uli ngati kulambira mafano kapena kuti kulambira konyenga. (Akolose 3:5) Komanso anthu a umbombo akafuna kupeza chinthu, sagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Lemba la Miyambo 28:20 limanena kuti munthu “woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.” Anthu amene amafuna kuti apeze zinthu mofulumira, amachita zinthu mwachiphamaso, amalanda zinthu za ena, amaba, kusunga anthu ena mokakamiza ngakhalenso kupha anthu ena.
Ngakhale kuti anthu ena amaganiza kuti kukonda ndalama sikungawachititse kukhala ndi makhalidwe oipa, komabe kuli ndi mavuto ake. Baibulo limanena kuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa.”—1 Timoteyo 6:9.
Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandize bwanji pa nkhani ya ndalama?
Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ndalama, Mulungu adzasangalala nafe ndipo sangatisiye. Ndipotu Mulungu akulonjeza anthu amene amayesetsa kumusangalatsa kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheberi 13:5, 6) Iye amatitsimikiziranso kuti “munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri.”—Miyambo 28:20.
a M’Mabaibulo ena vesili linamasuliridwanso kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”