Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?

Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?

Zimene Baibulo Limanena

 Baibulo limanena kuti Mulungu amafuna kuti anthu ‘azipewa dama.’ (1 Atesalonika 4:3) M’Baibulo, mawu akuti “dama” akuphatikizapo kuchita chigololo, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso kugonana kwa mwamuna ndi mkazi omwe sanakwatirane.

 N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikwatirana ngati akufuna kukhalira limodzi?

  •   Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Iye anayambitsa banja pa nthawi imene anakwatitsa mwamuna ndi mkazi oyambirira. (Genesis 2:22-24) Mulungu sankafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikhalira limodzi popanda kukwatirana.

  •   Mulungu amadziwa zomwe zingathandize anthu. Iye anakonza zoti anthu okwatirana azikhala limodzi moyo wawo wonse ndipo ankadziwa kuti zimenezi zidzathandiza komanso kuteteza anthu onse a m’banjalo. Taganizirani chitsanzo ichi: Kampani yopanga zinthu imapereka kabuku ka malangizo kothandiza munthu kudziwa mmene angalumikizire zinthu zomwe wagulazo. Mofananamo, malangizo amene Mulungu amatipatsa amathandiza mabanja kudziwa zoyenera kuchita kuti mabanja awo aziyenda bwino. Nthawi zonse anthu akamatsatira malangizo ochokera kwa Mulungu zinthu zimawayendera bwino.—Yesaya 48:17, 18.

    Kampani yopanga zinthu imapereka kabuku ka malangizo kothandiza munthu kudziwa mmene angalumikizire zinthu zomwe wagulazo. Mofananamo, malangizo amene Mulungu amatipatsa amathandiza mabanja kudziwa zoyenera kuchita kuti mabanja awo aziyenda bwino.

  •   Anthu omwe amagonana asanakwatirane amakumana ndi mavuto aakulu. Mwachitsanzo, amapereka kapena kutenga mimba yosakonzekera, amatenga matenda opatsirana pogonana, komanso amasowa mtendere. a

  •   Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi m’njira yoti azigonana n’cholinga choti azitha kubereka ana. Mulungu amaona kuti moyo ndi wopatulika ndipo kubereka ana ndi mphatso yamtengo wapatali. Iye amafuna kuti nafenso tiziona mphatso imeneyi kuti ndi yamtengo wapatali ndipo tingachite zimenezi mwa kulemekeza dongosolo la ukwati limene iye anakhazikitsa.—Aheberi 13:4.

 Kodi anthu ayenera kukhala kaye limodzi pofuna kuona ngati ali oyenereranadi?

 Kuti anthu akhale ndi banja la chimwemwe, sizoyenera kuti “akhale kaye limodzi kwa kanthawi pofuna kuyeserera” ndipo akaona kuti si oyenererana atha kusiyana. Koma chikondi chimakula ngati mwamuna ndi mkazi akuyesetsa kukhala okhulupirika komanso kuchita zinthu mogwirizana pothana ndi mavuto. b Ukwati ndi umene umathandiza kuti anthu okwatirana azikhala okhulupirika.—Mateyu 19:6.

 Kodi mwamuna ndi mkazi angatani kuti akhale ndi banja lolimba?

 Banja lililonse lili ndi mavuto. Ngakhale zili choncho, anthu okwatirana akamayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo, banja lawo likhoza kumayenda bwino kwambiri. Onani zitsanzo zotsatirazi: