Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?
Yankho la m’Baibulo
Inde. (Aroma 15:4) Mwachitsanzo, taonani mfundo za m’Baibulo zomwe zili m’munsimu zomwe zathandiza anthu ambiri omwe akulimbana ndi mavuto komanso nkhawa zosiyanasiyana.
Zimene zili munkhaniyi
Mavuto
Salimo 23:4: “Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani, sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine.”
Mfundo yake: Tikamapemphera kwa Mulungu komanso kudalira Mawu ake opezeka m’Baibulo kuti atitsogolere, tikhoza kulimbana ndi mavuto athu.
Afilipi 4:13: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”
Mfundo yake: Mulungu akhoza kutipatsa mphamvu kuti tilimbane ndi vuto lililonse.
Imfa ya munthu amene tinkamukonda
Mlaliki 9:10: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”
Mfundo yake: Anthu omwe anamwalira sakuvutika ndipo sangativulaze chifukwa sadziwa chilichonse.
Machitidwe 24:15: “Kudzakhala kuuka.”
Mfundo yake: Mulungu ali ndi mphamvu zodzaukitsa omwe anamwalira kuti adzakhalenso ndi moyo.
Kudziimba mlandu
Salimo 86:5: “Inu Yehova a ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.”
Mfundo yake: Mulungu amakhululukira anthu omwe amadzimvera chisoni chifukwa cha zinthu zomwe analakwitsa ndiponso omwe ndi ofunitsitsa kuti asadzabwerezenso zomwe anachita.
Salimo 103:12: “Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.”
Mfundo yake: Mulungu akatikhululukira, amatiikira kutali machimo athu. Ndipo sakhalira kutikumbutsa zomwe tinalakwa ndi cholinga chofuna kutiimba mlandu kapena kutilanga.
Kukhumudwa
Salimo 31:7: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.”
Mfundo yake: Mulungu akudziwa bwino za mavuto omwe mukudutsamo. Amadziwanso bwino mmene mavutowo amakukhudzirani mumtima ngakhale pamene anthu ena sakuona zimenezo.
Salimo 34:18: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”
Mfundo yake: Mulungu akulonjeza kuti ndi wokonzeka kukuthandizani pamene muli wokhumudwa. Iye angathe kukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Kudwala
Salimo 41:3: “Yehova adzachirikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.”
Mfundo yake: Mulungu akhoza kukuthandizani pamene mukudwala kwambiri. Angachite zimenezi pokupatsani mtendere wamumtima, mphamvu zoti muthe kupirira komanso nzeru kuti mukwanitse kusankha bwino zoti muchite.
Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”
Mfundo yake: Mulungu analonjeza kuti m’tsogolomu anthu onse adzakhala ndi moyo wathanzi.
Nkhawa komanso kuvutika maganizo
Salimo 94:19 “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”
Mfundo yake: Tikamadalira Yehova pamene tili ndi nkhawa, Iye angatithandize kuti tikhazikitse maganizo athu m’malo.
1 Petulo 5:7: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’
Mfundo yake: Mulungu amatidera nkhawa tikamavutika. Iye amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye n’kumuuza zomwe zikutidetsa nkhawa.
Nkhondo
Salimo 46:9: “Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”
Mfundo yake: Posachedwa, Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo zonse.
Salimo 37:11, 29: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka. . . . Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”
Mfundo yake: Anthu abwino adzakhala mwamtendere padziko lapansi mpaka kalekale.
Kudera nkhawa zam’tsogolo
Yeremiya 29:11: “Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.”
Mfundo yake: Mulungu akutsimikizira anthu ake kuti adzawapatsa tsogolo labwino kwambiri.
Chivumbulutso 21:4: “Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”
Mfundo yake: Mulungu akulonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zoipa zomwe timaziona komanso kukumana nazo masiku ano.
a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?”