Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

1 Petulo 5:6, 7​—“Mudzichepetse Pamaso pa Mulungu Wamphamvu, . . . Tayani pa Iye Nkhawa Zanu Zonse”

1 Petulo 5:6, 7​—“Mudzichepetse Pamaso pa Mulungu Wamphamvu, . . . Tayani pa Iye Nkhawa Zanu Zonse”

 “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake. Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”​—1 Petulo 5:6, 7, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti panthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa Iye ndiye amakusamalani.”—1 Petulo 5:6, 7, Chipangano Chatsopano mu Chichewa Cha Lero.

Tanthauzo la 1 Petulo 5:6, 7

 Ponena mawu amenewa, mtumwi Petulo ankafuna kutsimikizira Akhristu kuti akhoza kupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kumuuza nkhawa ndi mavuto awo. Mulungu amadalitsa anthu odzichepetsa ndipo adzawapatsa mphoto yayikulu.

 “Dzichepetseni . . . pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.” M’Baibulo, mawu akuti dzanja la Mulungu nthawi zambiri amatanthauza mphamvu zopulumutsa komanso zoteteza. (Ekisodo 3:19; Deuteronomo 26:8; Ezara 8:22) Akhristu amadzichepetsa pansi pa dzanja la Mulungu akamasonyeza kuti amamudalira, amadziwa malire awo ndiponso kuti sangathe kupirira mavuto paokha. (Miyambo 3:5, 6; Afilipi 4:13) Amakhala ndi chikhulupiriro kuti Mulungu ali ndi mphamvu zowathandiza m’njira yoyenerera komanso pa nthawi yake.​​—Yesaya 41:10.

 “Kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.” Amene amapirira mavuto amakhala ndi chikhulupiriro kuti Mulungu adzawadalitsa. Iye sadzalola kuti atumiki ake ayesedwe kufika pamene sangathe kupirira kapena kuti kuyesedwa mpaka kalekale. (1 Akorinto 10:13) Kuonjezera pamenepo, akamapitiriza kuchita zoyenera, Mulungu adzawadalitsa “pa nyengo yake.”​—Agalatiya 6:9.

 “Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.” Akhristu akhoza kutulira kapena kutaya nkhawa zawo zonse kwa Mulungu popemphera modzichepetsa kwa iye. Buku lina linanena kuti: “Mawu akuti ‘kutaya’ amaimira kuyesetsa kugwetsa chinachake chomwe tachinyamula. Amafotokoza za chinthu chomwe munthu wina wachitira dala.” Ngati Mkhristu watula nkhawa zake kwa Mulungu, akhoza kuchepetsa nkhawazo komanso kupeza zomwe Baibulo limanena kuti ndi “mtendere wa Mulungu.” (Afilipi 4:6, 7) Sangakayikire kuti Mulungu akufuna kumuthandiza chifukwa akudziwa kuti Mulunguyo amasamala za iye komanso akhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zake zosatha kumuchirikiza.—Salimo 37:5; 55:22.

Nkhani yonse ya pa 1 Petulo 5:6, 7

 Chaputala 5 chimamaliza ndi kalata yomwe mtumwi Petulo analembera Akhristu. (1 Petulo 1:1) Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi yakale, Akhristu a masiku anonso akukumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe amayesa chikhulupiriro chawo ndipo zimapangitsa kuti akhale ndi nkhawa. (1 Petulo 1:6, 7) Kudziwa mavuto awo, kunapangitsa Petulo kuti alembe kalata yowalimbikitsa komanso yosonyeza kuti amawakonda cha m’ma 62-64 C.E.​—1 Petulo 5:12.

 Petulo anamaliza kalata yake polimbikitsa anthu amene an’kakumana ndi mavuto chifukwa cha chikhulupiriro chawo, kuti ngati angakhalebe odzichepetsa ndi kudalira Mulungu, sangakayikire kuti iye adzawathandiza kukhala olimba. (1 Petulo 5:5-10) Mawu a Petulowa, akhozanso kulimbikitsa Akhristu omwe akuzunzidwa masiku ano.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la1 Petulo.