Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Maliko 11:24​—“Zinthu Zilizonse Mukazipemphera Ndi Kuzipempha, Khulupirirani Kuti Mwazilandira”

Maliko 11:24​—“Zinthu Zilizonse Mukazipemphera Ndi Kuzipempha, Khulupirirani Kuti Mwazilandira”

 “N’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.”​—Maliko 11:24, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.”​—Maliko 11:24, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Maliko 11:24

 Ponena mawuwa, Yesu ankafuna kusonyeza otsatira ake kufunika kokhulupirira kwambiri mphamvu ya pemphero. Iye anawatsimikizira kuti, sikuti Mulungu amangomvetsera mapemphero awo koma amayankhanso mapempherowo. Munthu amene amapemphera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu amakhala wotsimikiza kuti zomwe wapemphazo mosakayikira Mulungu ayankha. Zimakhala ngati kuti wayankhidwa kale.

 Yesu anatsindika kufunika kopemphera tili ndi chikhulupiriro. Iye ananena kuti amene akupemphera sayenera ‘kukayika mumtima mwake’ koma akhale ‘ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi.’ (Maliko 11:23) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amene amakayikira “asaganize kuti adzalandira kanthu kwa Yehova.” aYakobo 1:5-8.

 Munthu amene ali ndi chikhulupiriro amapemphera m’zochitika zosiyanasiyana. (Luka 11:9, 10; Aroma 12:12) Akamatero, amasonyeza kuti akufunitsitsadi zomwe wapemphazo ndipo akukhulupirira kuti Mulungu ayankha pemphero lake. Komanso amakumbukira kuti Mulungu akhoza kusankha kuyankha pemphero m’njira imene samaganizira ndipo angachitenso zimenezi pa nthawi imene samayembekezera n’komwe.​—Aefeso 3:20; Aheberi 11:6.

 Komabe, mawu a Yesuwa samatanthauza kuti munthu akhoza kumayembekezera kuti angalandire chilichonse chomwe wapempha kwa Mulungu. Yesu ankanena kwa otsatira ake, omwe anali amuna achikhulupiriro amene ankayesetsa kulambira Yehova Mulungu movomerezeka. Baibulo limanena kuti Yehova amamvetsera mapemphero okhawo omwe ali ogwirizana ndi chifuniro chake. (1 Yohane 5:14) Iye samvetsera mapemphero a anthu omwe amanyalanyaza mwadala mfundo zake komanso amene amachita zoipa koma osalapa. (Yesaya 1:15; Mika 3:4; Yohane 9:31) Kuti mudziwe zambiri zokhudza mapemphero omwe Mulungu amamvetsera, onerani vidiyo yaifupi iyi.

Nkhani Yonse ya pa Maliko 11:24

 Kumapeto kwa ulaliki wake wa padziko lapansi, Yesu anakambirana ndi ophunzira ake kufunika kosonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu. Iye anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mafanizo. Popita ku Yerusalemu, anaona mtengo wa mkuyu womwe munali masamba ongophukira kumene. Komabe, zinapezeka kuti mumtengowo munalibe zipatso, choncho Yesu anawutemberera. (Maliko 11:12-14) Maonekedwe opusitsa a mtengowu, ankaimira mtundu wa Aisiraeli omwe ankaoneka ngati akulambira Mulungu koma ankasowa chikhulupiriro. (Mateyu 21:43) Pambuyo pake mtengowu unauma, zomwe zinasonyeza zimene zinali zitatsala pang’ono kuchitikira Aisiraeli opanda chikhulupiriro.​—Maliko 11:19-21.

 Mosiyana ndi zimenezi, Yesu anatsimikizira kuti ophunzira ake adzayamba kukhala ndi chikhulupiriro chomwe chinkafunika kuti athane ndi mavuto komanso kukwaniritsa zinthu zodabwitsa kwambiri. (Maliko 11:22, 23) Malangizo a Yesu pa nkhani ya pemphero, anali a panthawi yake chifukwa chikhulupiriro cha ophunzira ake chinali chitatsala pang’ono kuyesedwa. Ankafunika kupirira imfa ya Yesu komanso kutsutsidwa kwambiri mu utumiki. (Luka 24:17-20; Machitidwe 5:17, 18, 40) Masiku ano, otsatira a Yesu angathenso kupirira mavuto osiyanasiyana akamasonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu komanso akamakhulupirira mphamvu ya pemphero.​—Yakobo 2:26.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mfundo zachidule zokhudza buku la Maliko.

a Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?”