2
Nimadelanji Nkhawa na Mmene Nimaonekela?
KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?
Ganizila cocitika ici: Julia akadziyang’ana pa gilasi amangoonapo cidumbo, kapena kuti dugude. Ngakhale kuti makolo ake na anzake amamunena kuti ni “dayonda,” mumtima mwake iye amati: “Nifuna mpaka niyonde.”
Posacedwa, Julia anaganiza zocita ciliconse cotheka kuti ayonde. Conco, anayamba kukhala na njala kwa masiku angapo . . .
Ngati iwenso umamvela ngati Julia, kodi uyenela kucita ciani?
YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!
Si kulakwa ngati ukuda nkhawa na mmene umaonekela. Ngakhale Baibo imakambapo za maonekedwe abwino a akazi ndi amuna ena, monga Sara, Rakele, Yosefe, Davide, ndi Abigayeli. Baibo imakamba kuti mtsikana wina dzina lake Abisagi “anali ciphadzuŵa.”—1 Mafumu 1:4.
Atsikana ambili amada nkhawa na maonekedwe awo. Zimenezi zimabweletsa mavuto akulu. Mvelako izi:
-
Kafuku-fuku wina anaonetsa kuti atsikana 58 pesenti anali kudziona kuti ni onenepa kwambili, koma kweni-kweni onenepa kwambili anali 17 pesenti cabe.
-
Kafuku-fuku winanso anaonetsa kuti azimayi 45 pesenti amene anali oyonda anali kudziona kuti ni onenepa kwambili.
-
Atsikana ena pofuna kuyonda afika mpaka podwala matenda okana kudya (anorexia), amene munthu akhoza kufa nawo.
Miyambo 17:17.
Ngati uona zizindikilo za matenda amenewa, peza cithandizo. Yamba mwa kuuzako kholo lako kapena wacikulile wina amene umam’dalila. Baibo imakamba kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—KUKONGOLA KWA ZOONA!
Kukamba zoona, kukongola kweni-kweni ni kuja kwa munthu wamkati. Ganizila za Abisalomu, mwana wa Davide. Baibo imakamba kuti:
“Munalibe mwamuna wina wotamandika kwambili koposa Abisalomu cifukwa ca kukongola kwake. Iye analibe cilema ciliconse.”—2 Samueli 14:25.
Ngakhale n’conco, mnyamata ameneyu anali wonyada, wofuna kuchuka, ndi waciwembu. Conco, Baibo siipeleka cithunzi cabwino ca Abisalomu. Imaonetsa kuti anali munthu wosakhulupilika, komanso wacidani cokhoza kupha naco munthu.
Ndiye cifukwa cake Baibo imatilangiza kuti:
“Valani umunthu watsopano.”—Akolose 3:10.
“Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, . . . Koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima.”—1 Petulo 3:3, 4.
Sikulakwa kufuna kuoneka bwino. Koma cofunika kwambili ni mtundu wa munthu amene uli. Potsilizila pake, cimene cidzakupangitsa kuoneka wokongola ni makhalidwe ako abwino, osati maonekedwe. Mtsikana wina dzina lake Phylicia anati: “Anthu ambili angakopeke msanga na maonekedwe ako okongola. Koma cimene adzakukumbukila naco kwa nthawi yaitali ni makhalidwe ako abwino.”
MAONEKEDWE AKO
Kodi nthawi zambili umakhumudwa na mmene uonekela?
Kodi unaganizapo zoyamba kudzola mafuta oyeletsa, kapena kuyamba dayati (diet) yonyanya kuti uyonde?
N’ciani cimene ukanakonda kusintha pa maonekedwe ako? (Conga n’ziti pansi apa)
-
KUTALIMPHA KUFUPIKA
-
TSITSI
-
KUNENEPA
-
KUDA
-
ZINA
Ngati wayankha inde pamafunso aŵili oyambilila, na kuconga zinthu ziŵili kapena kuposapo pa funso lacitatu, dziŵa izi: N’kutheka kuti ena sakuona mmene udzionela. N’kuthekanso kuti umada nkhawa na maonekedwe ako mopitilila malile.—1 Samueli 16:7.