DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU
4 | Limbitsani Ciyembekezo Canu
CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA
Nkhawa yobwela cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, imakhudza anthu m’njila zosiyanasiyana. Ambili amene akumanapo na mavuto aakulu, sakhala na ciyembekezo ciliconse. Kodi zotulukapo zake zakhala zotani?
-
Ena safuna n’komwe kuganizila zakutsogolo.
-
Enanso amamwa moŵa kapena kugwilitsa nchito mankhwala osokoneza bongo kuti aiŵaleko mavuto.
-
Komanso ena amaona kuti zili bwino kufa cabe.
Zimene Muyenela Kudziŵa
-
Ena mwa mavuto amene mukukumana nawo angakhale a kanthawi kocepa, ndipo angathe mosayembekezeleka.
-
Ngakhale ngati mavuto anu sangathe palipano, pali zinthu zimene mungacite kuti mukwanitse kupilila.
-
Baibo imapeleka ciyembekezo ceniceni cakuti mavuto onse a anthu adzathelatu.
Zimene Mungacite Pali Pano
Baibo imati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.
Pewani kudela nkhawa kwambili zakutsogolo. Musalole kuti nkhawa ya zakutsogolo ikulepheletseni kucita zinthu zimene muyenela kucita palipano.
Kuganizila kwambili zinthu zoipa zimene zingacitike kapena ayi, kungawonjezele nkhawa yanu na kukutayitsani ciyembekezo ca tsogolo labwino.
Baibo Imapeleka Ciyembekezo Codalilika
Popemphela kwa Mulungu, wamasalimo wina anati: “Mawu anu ndi nyale younikila ku mapazi anga ndi kuwala kounikila njila yanga.” (Salimo 119:105) Onani mmene Baibo, Mawu a Mulungu, imatithandizila monga nyale.
Usiku pamene kuli mdima, nyale imatithandiza kudziŵa poyenela kuponda poyenda. Mofananamo, m’Baibo muli malangizo anzelu amene angatitsogolele pamene tifuna kupanga cisankho covuta.
Cina, nyale imatiunikila njila kuti tikwanitse kuona zimene zili kutsogolo. Mofanana na zimenezi, Baibo imatithandiza kudziŵa zimene zidzacitika kutsogolo.