Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 1 2023 | Kodi Dziko Lapansi Lidzapulumuka?—Zifukwa Zokhalila na Ciyembekezo

Simuyenela kucita kukhala asayansi kuti mudziŵe kuti cinacake cikuwononga dziko lapansi. Madzi abwino, nyanja zamcele, nkhalango, ngakhale mpweya zikuwonongedwa. Kodi dziko lapansi lidzapulumuka? Onani zifukwa zimene tingakhalile na ciyembekezo.

 

Madzi Abwino

Ni njila ziti zam’cilengedwe zimene zimathandiza kuti madzi asathe padziko?

Nyanja Zamcele

Kodi nyanja zamcele zingakhalenso zabwino?

Nkhalango

Kodi oona za nkhalango apeza zotani zokhuza nkhalango zimene zinadulidwa?

Mpweya

Kuwonongeka kwa mpweya kumaika paciwopsezo za moyo padziko lapansi. Ni njila ziti zam’cilengedwe zimene Mulungu anapanga kuti ziziyeletsa mpweya umene timapuma?

Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya

N’cifukwa ciyani timakhulupilila kuti dziko lapansi lidzapulumuka komanso kukhalapo kwamuyaya?

M’kope ino ya Galamuka!

Ŵelengani nkhani zofotokoza zimene zikucitikila dziko lapansi komanso cifukwa cake tingakhale na ciyembekezo.