Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Ali na Makhalidwe Abwanji?

Kodi Mulungu Ali na Makhalidwe Abwanji?

Pamene tidziŵa zambili za makhalidwe a munthu, m’pamenenso timam’dziwa bwino, ndipo ubwenzi wathu na iye umalimba. N’cimodzi-modzi na Yehova, pamene tidziŵa zambili za makhalidwe ake, m’pamene timam’dziŵa bwino, ndipo ubwenzi wathu na iye umalimba. Pa makhalidwe onse abwino a Mulungu, anayi ni apadela kwambili: mphamvu zake, nzelu, cilungamo, komanso cikondi.

MULUNGU NI WAMPHAMVU

“Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwilitsa nchito mphamvu yanu.”YEREMIYA 32:17.

Mphamvu za Mulungu zimaonekela m’zinthu zimene analenga. Mwacitsanzo, mukaimilila panja dzuŵa lili lowala, kodi thupi lanu limamva ciani? Inde, kutentha kwa dzuŵa. Kweni-kweni mumamva mphamvu za kulenga za Yehova. Kodi dzuŵa ili na mphamvu zoculuka motani? Pakati peni-peni pa dzuŵa, amati m’potentha kwambili kufika pa 15,000,000°C. Pa sekondi iliyonse, dzuŵa imatulutsa mphamvu zofanana na zimene zingatuluke pakaphulika mabomba a nyukiliya mamiliyoni ambili-mbili.

Komabe, dzuŵa ni yaing’ono poyelekezela na mamiliyoni osaŵelengeka a nyenyezi m’cilengedwe. Asayansi amakamba kuti nyenyezi yochedwa UY Scuti, imene ni imodzi mwa nyenyezi zikulu-zikulu, ni yaikulu kwambili cakuti kukula kwake, dzuŵa ingaloŵemo maulendo pafupi-fupi 1,700. Ngati nyenyezi imeneyi ingakhale pa malo a dzuŵa, ndiye kuti ingameze pulaneti yathu ino ya dziko ndiponso mpita wonse wa pulaneti yaikulu yochedwa Jupiter. Mwina izi zitithandiza kumvetsetsa bwino zimene Yeremiya anakamba kuti, Yehova Mulungu anapanga kumwamba na dziko lapansi, kutanthauza cilengedwe conse, poseŵenzetsa mphamvu zake zoculuka.

Kodi timapindula motani na mphamvu za Mulungu? Kuti tikhale na moyo, timadalila pa zinthu zimene Mulungu analenga, monga dzuŵa na zinthu zonse zimene zimacilikiza moyo padziko lapansi. Kuwonjezela apo, Mulungu amaseŵenzetsa mphamvu zake kuti athandize munthu aliyense payekha-payekha. Motani? M’nthawi ya atumwi, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zocita zinthu zozizwitsa kwambili. Timaŵelenga kuti: “Akhungu akuonanso, olumala akuyendayenda, akhate akuyeletsedwa ndipo ogontha akumva. Akufa akuukitsidwa.” (Mateyu 11:5) Nanga bwanji masiku ano? Baibo imati: “Iye amapeleka mphamvu kwa munthu wotopa.” Imawonjezelanso kuti: “Anthu odalila Yehova adzapezanso mphamvu.” (Yesaya 40:29, 31) Mulungu angatipatse “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti tilimbane na mavuto komanso mayeselo amene tingakumane nawo. (2 Akorinto 4:7) Kodi izi sizikupangitsani kufuna kuyandikila Mulungu, amene mwacikondi amaseŵenzetsa mphamvu zake zazikulu kuti atithandize pa mavuto athu?

MULUNGU NI WANZELU

“Nchito zanu ndi zoculuka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzelu zanu.”SALIMO 104:24.

Pamene tiphunzila za zinthu zambili zimene Mulungu analenga, m’pamene timadabwa na nzelu zake. Pali maphunzilo amene asayansi amacita ochedwa biomimetics kapena kuti biomimicry. Iwo amaphunzila za zolengedwa za Yehova, na kutengelako cipangidwe ca zinthu zimenezo kuti apange zinthu, kucokela pa tunthu tung’ono-tung’ono monga diso la kamela mpaka ku zikulu-zikulu monga ndeke.

Diso la munthu linalengedwa modabwitsa kwambili

Ndipo kudabwitsa kwa nzelu za Mulungu kumaonekelanso bwino kwambili poona mmene munthu amapangikila. Ganizilani cabe za mmene munthu amayambila m’mimba. Coyamba amangokhala kadzila ka mkazi komwe kalumikizana na mbewu ya mwamuna. Kadzilako kamakhala na malangizo obadwila onse ofunikila. Kenako kamagaŵikana n’kukhala maselo ambili-mbili ooneka ofanana. Koma nthawi yake ikafika, maselowo amayamba kuumbika mosiyana-siyana. Ena amakhala maselo a magazi, ena amitsempha, komanso ena maselo amafupa. Kenako ziŵalo zimayamba kupangika n’kuyamba kugwila nchito. Pa miyezi 9 cabe, kadzila koyamba kaja kamafika pokhala khanda lamoyo. Poona mmene mwana amapangikila, anthu ambili afika povomeleza zimene mlembi wa Baibo anakamba kuti: “Ndidzakutamandani cifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandicititsa mantha.”—Salimo 139:14.

Kodi timapindula motani na nzelu za Mulungu? Mlengi wathu amadziŵa zimene tifunikila kuti tikhale acimwemwe. Popeza Mulungu ni wa nzelu kwambili komanso womvetsa zinthu, iye amatipatsa malangizo anzelu kupitila m’Mawu ake Baibo. Mwacitsanzo, imatilimbikitsa kuti: “Pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Kodi amenewa si malangizo anzelu? Inde, ni anzelu. Madokota apeza kuti kukhululuka msanga kungathandize munthu kugona tulo twabwino komanso kubwezako pansi BP. Ndiponso kungathandize munthu kupewa matenda ovutika maganizo komanso matenda ena. Mulungu ali monga bwenzi lathu lacikondi limene nthawi zonse limatipatsa malangizo othandiza. (2 Timoteyo 3:16, 17) Kodi simungakonde kukhala na bwenzi la conco?

MULUNGU NI WACILUNGAMO

“Yehova amakonda cilungamo.”SALIMO 37:28.

Nthawi zonse Mulungu amacita zoyenela. Ndipo ‘Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuzonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.’ (Yobu 34:10) Ziweluzo zake n’zolungama, monga mmene wamasalimo anauzila Yehova kuti: “Mudzaweluza anthu molungama.” (Salimo 67:4) Popeza “Yehova amaona mmene mtima ulili,” iye saputsitsika na cinyengo, koma amadziŵa zoona zeni-zeni na kupeleka ziweluzo zoyenelela. (1 Samueli 16:7) Kuwonjezela apo, Mulungu amadziŵa kupanda cilungamo kulikonse komanso ziphuphu zimene zikucitika padziko lapansi, ndipo walonjeza kuti posacedwa “oipa adzacotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.

Komabe, Mulungu si woweluza wankhanza, amene amakhalila cabe kulanga anthu. Amaonetsa cifundo cake pakafunika kutelo. Baibo imati: “Yehova ndi wacifundo ndi wacisomo,” ngakhale kwa ocita zoipa ngati alapa mocokela pansi pamtima. Kodi cimeneci sindiye cilungamo ceni-ceni?—Salimo 103:8; 2 Petulo 3:9.

Kodi timapindula motani na cilungamo ca Mulungu? Mtumwi Petulo anati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Timapindula na cilungamo ca Mulungu cifukwa alibe tsankho komanso sakondela. Tingakhale pa ubwenzi na iye komanso kukhala olambila ake mosasamala kanthu kuti ndise olemela, osauka, ophunzila, osaphunzila, kaya a mtundu uti kapena ticokela ku dziko liti.

Mulungu alibe tsankho, ndipo tingapindule na cilungamo cake mosasamala kanthu kuti ndise olemela kapena osauka kaya ticokela mtundu uti

Cifukwa cakuti Mulungu afuna kuti timvetsetse komanso tipindule na cilungamo cake, iye anatipatsa cikumbumtima. Malemba amafotokoza cikumbumtima kuti cili monga cilamulo ‘colembedwa m’mitima mwathu,’ cimene “cimacitila umboni” zocita zathu kuti kaya n’zoyenela kapena n’zosayenela. (Aroma 2:15) Kodi cimatipindulitsa motani? Ngati cikumbumtima cathu taciphunzitsa bwino, cingatilimbikitse kupewa kucita zinthu zoipa kapena zopanda cilungamo. Ndipo ngati talakwitsa cingatilimbikitse kuti tilape na kusintha khalidwe lathu. Inde, kumvetsetsa bwino cilungamo ca Mulungu kumatipindulitsa komanso kumatithandiza kukhala naye pa ubwenzi!

MULUNGU NDIYE CIKONDI

“Mulungu ndiye cikondi.”1 YOHANE 4:8.

Mulungu amaonetsa mphamvu, nzelu, komanso cilungamo. Koma Baibo siikamba kuti Mulungu ndiye mphamvu, nzelu, kapena cilungamo. Imakamba kuti iye ndiye cikondi. Cifukwa ciani? Cifukwa mphamvu za Mulungu ndiye zimam’pangitsa kuti akwanitse kucita zinthu, pamene cilungamo na nzelu zake n’zimene zimam’tsogolela kucita zinthu. Koma cikondi ca Yehova ndiye cimam’limbikitsa kucita zonse zimene amacita.

Ngakhale kuti Yehova sanali kusoŵekela ciliconse, cikondi cake cinam’limbikitsa kulenga angelo komanso anthu, amene angapindule na cikondi komanso cisamalilo cake. Mwacikondi cake, Mulungu anakonza dziko lapansi kuti likhale malo abwino okhalapo anthu. Ndipo wapitiliza kuonetsa cikondi cake kwa anthu onse, cakuti “amawalitsila dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsila mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mateyu 5:45.

Kuwonjezela apo, “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo” (Yakobo 5:11) Iye amaonetsa cikondi kwa amene amafunitsitsa kum’dziŵa bwino komanso kukhala naye pa ubwenzi. Mulungu amadziŵa anthu otelo aliyense payekha-payekha. Inde, “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”Machitidwe 17:27.

Kodi timapindula motani na cikondi ca Mulungu? Tikaona kukongola kwa dzuŵa pamene likuloŵa, timakondwela mu mtima. Timakondwelanso tikamvela kuseka kwa mwana wakhanda. Timanyadila kwambili cikondi cimene wacibale wathu angationetse. Zinthu zimenezi sizofunika kweni-kweni, koma zimatisangalatsa kwambili.

Pemphelo ni njila ina imene timapindulila na cikondi ca Mulungu. Baibo imatilimbikitsa kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Mofanana ndi tate wacikondi, iye amafuna kuti tizim’pempha kuti atithandize pa zimene zimatidetsa nkhawa kwambili. Ndipo cifukwa ca cikondi cake copanda dyela, Yehova amatilonjeza kuti adzatipatsa “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7.

Kodi zimene tafotokoza mwacidule zokhudza makhalidwe akulu-akulu a Mulungu monga mphamvu, nzelu, cilungamo, komanso cikondi, zakuthandizani kum’dziŵa bwino Mulungu? Kuti mukulitse cikondi canu pa Mulungu, tikupemphani kuti mudziŵe zimene anakucitilani komanso zimene adzakucitilani kutsogolo kuti mupindule.

KODI MULUNGU ALI NA MAKHALIDWE ABWANJI? Yehova ni wamphamvu kwambili, wanzelu, komanso wacilungamo kuposa wina aliyense. Koma khalidwe lake lalikulu kwambili pa onse ni cikondi