Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino

Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino

Maria wa ku Spain anati: “Mwamuna wanga ataniuza kuti akunisiya cifukwa wapeza mkazi wacitsikana, cinaniŵaŵa maningi cakuti n’nali kufuna kuti nife cabe. Zonse zinali zopanda cilungamo kwa ine, makamaka pamene n’naganizila zonse zimene n’nadzimana cifukwa ca iye.”

Bill wa ku Spain anati: “Mkazi wanga atanisiya mosayembekezela, zinali monga kuti ciwalo cina m’thupi langa caleka kugwila nchito. Zolinga zathu, zinthu zimene tinali kuyembekezela kucita, komanso mapulani athu, zonse zinathela pamenepo. Masiku ena n’nali kuona kuti lelo nilibe nkhawa, koma mosayembekezela n’nali kupezeka kuti nayambanso kuvutika maganizo kwambili.”

CIMAŴAŴA kwambili ngati wina sayenda bwino m’cikwati. N’zoona kuti ena amasankha kum’khululukila mnzawo wa m’cikwati amene walapa, na kukonzanso cikwati cawo. * Koma kaya cikwati cidzapitiliza kapena ayi, mwamuna kapena mkazi amene wadziŵa kuti mnzake sanali kuyenda bwino, cimaŵaŵa kwambili. Nanga kodi n’ciani cingathandize anthu otelo?

MAVESI A M’BAIBO AMENE ANGAKUTHANDIZENI

Anthu amene anacitilidwa zosakhulupilika na mnzawo wa m’cikwati, zimawapweteka kwambili. Koma ngakhale n’conco, ambili apeza citonthozo m’Malemba. Iwo tsopano adziŵa kuti Mulungu amaona kulila kwawo ndipo amawamvela cifundo.—Malaki 2:13-16.

“Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”Salimo 94:19.

Bill anati: “Pamene n’nali kuŵelenga vesi imeneyi, n’nali kumvela monga kuti Yehova akunitonthoza mwacikondi, mmene tate wacifundo amacitila.”

“Munthu wokhulupilika, mudzamucitila mokhulupilika.”Salimo 18:25.

Carmen amene mwamuna wake sanali kuyenda bwino kwa miyezi, anati: “Mwamuna wanga sanali wokhulupilika kwa ine. Koma n’nali na cidalilo cakuti Yehova adzakhalabe wokhulupilika kwa ine. Iye sanganisiye.”

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”Afilipi 4:6, 7.

Sasha anati: “Lembali n’naliŵelenga mobweleza-bweleza. Ndipo pamene n’napitiliza kupemphela, Mulungu ananipatsa mtendele wa m’maganizo.”

Onse amene taŵagwila mawu pamwambapa, anafika poona kuti moyo ni wosafunika. Koma iwo anadalila Yehova Mulungu, ndipo anapeza mphamvu m’Mawu ake. Bill anakambanso kuti: “Cikhulupililo cinanithandiza kuona kuti moyo wanga ni wofunikabe, olo pamene zonse zionaoneka monga kuti zawonongeka. Ngakhale kuti kwa kanthawi ‘ninayenda m’cigwa ca mdima wandiweyani,’ Mulungu anali naine.”—Salimo 23:4.

^ Kuti mudziŵe zambili pa nkhani ya kukhululukila mnzanu wa m’cikwati kapena ayi, onani nkhani zopezeka m’magazini ya Galamukani! ya May 8, 1999, za mutu wakuti, “Pamene Mwamuna Kapena Mkazi Akhala Wosakhulupilika.”