Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Moseŵenzetsela Ndalama

Moseŵenzetsela Ndalama

Anthu oculuka apewa mavuto ambili a za ndalama, mwa kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo.

PANGANI BAJETI YABWINO

MFUNDO YA M’BAIBO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”—Miyambo 21:5.

TANTHAUZO LAKE: Pangani bajeti, ndipo yesetsani kutsatila zimene zili pa bajeti yanu. Mufunika kuikonza bwino bajeti yanu musanayambe kuseŵenzetsa ndalama. Kumbukilani kuti simungagule zinthu zonse zimene mufuna. Conco, muziseŵenzetsa mwanzelu ndalama zanu.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Tsatilani zimene mwaika pa bajeti yanu. Lembani mndandanda wa zinthu zonse zimene mufuna kuti mukagule, ndiyeno ikani zinthuzo m’magulu. Kenako, lembani kuculuka kwa ndalama zimene mufuna kuseŵenzetsa pa gulu lililonse. Ngati mwapeleŵela ndalama pa gulu limodzi la zinthu zimene mufuna kugula, tengani ndalama pa gulu lina kuti mukwanitse kugula zimene mufuna. Mwacitsanzo, ngati mwafunikila ndalama zambili kuti mugule mafuta a m’galimoto, mungatenge ndalama zimene mumawonongela pa zinthu zosafunika kweni-kweni, monga kukadya zakudya ku lesitilanti.

  • Pewani nkhongole zosafunikila. Yesetsani kupewa nkhongole zosafunikila. Muzisungako pang’ono-pang’ono ndalama zakuti mukagulile zimene mufuna. Ngati mumaseŵenzetsa khadi ya ku banki pogula zinthu, lipilani ndalama zonse mwezi usanathe kuti mupewe kulipila ndapusa. Ngati muli na nkhongole, pangani makonzedwe a mmene mudzalipilila nkhongoleyo, ndipo yesetsani kucita zimenezo.

    Kafuku-fuku wina anaonetsa kuti ngati munthu agula zinthu na khadi ya ku banki, kaŵili-kaŵili amafuna kugula zinthu zambili. Conco ngati muli na khadi ya ku banki, yesetsani kudziletsa pogula zinthu.

PEWANI MAKHALIDWE OSAYENELA

MFUNDO YA M’BAIBO: “Cifukwa ca kuzizila, waulesi salima. Iye azidzapemphapempha nthawi yokolola koma sadzapatsidwa kanthu.” —Miyambo 20:4.

TANTHAUZO LAKE: Ulesi ungabweletse umphawi mu umoyo wa munthu. Conco limbikilani kugwila nchito, ndipo yesetsani kuseŵenzetsa ndalama zanu mwanzelu kuti mukakwanitse kugula zofunikila kutsogolo.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Limbikilani kugwila nchito. Ngati ndimwe wolimbikila komanso wodalilika pa nchito, abwana anu adzakukondani, ndipo adzafuna kuti mupitilize kugwila nchito.

  • Khalani wokhulupilika. Musaŵabele abwana anu. Kusakhulupilika pa nchito kungawononge mbili yanu, ndipo kutsogolo zingakhale zovuta kuti ena akakulembeni nchito.

  • Pewani mtima wadyela. Ngati nthawi zonse mumafuna kukhala na ndalama zambili, m’kupita kwa nthawi mungawononge thanzi lanu, komanso maubwenzi anu ndi ena. Kumbukilani kuti cinthu cofunika kwambili mu umoyo wa munthu si ndalama.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBO

Ŵelengani Baibo pa intaneti, imene ipezeka m’vitundu vofika m’mahandiledi pa webusaiti ya jw.org

MUSAWONONGE NTHAWI YANU NA NDALAMA PA ZIZOLOŴEZI ZOIPA.

“Cidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka, ndipo kuwodzela kudzaveka munthu nsanza.”​—MIYAMBO 23:21.

PEWANI NKHAWA ZOSAFUNIKILA.

“Lekani kudela nkhawa moyo wanu kuti mudzadya ciani, kapena mudzamwa ciani, kapenanso kuti mudzavala ciani.”​—MATEYU 6:25.

PEWANI KADUKA.

“Munthu wanjilu amayesetsa kuti apeze zinthu zamtengo wapatali, koma sadziwa kuti umphawi udzamugwela.”​—MIYAMBO 28:22.