Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungacite Ciani Kuti Mukapeze Moyo Weni-Weni?

Mungacite Ciani Kuti Mukapeze Moyo Weni-Weni?

MULUNGU sanali kufuna kuti umoyo ukhale mmene ulili masiku ano. Dziko linafunika kudzala ndi anthu ofuna kulamulilidwa na Mlengi, anthu amene amapindula na citsogozo cake, komanso kuonetsa makhalidwe ake abwino. Mulungu anali kufuna kuti iwo akhale acimwemwe pamene asamalila mabanja awo, kutulukila zinthu zatsopano, na kupanga dziko lonse kukhala paradaiso.

MULUNGU ANALONJEZA KUSINTHA ZINTHU PA DZIKO LAPANSI KUTI UMOYO UKHALE MMENE ANALI KUFUNILA

  • “Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”Salimo 46:9.

  • “Inafikanso nthawi yoikidwilatu . . . yowononga amene akuwononga dziko lapansi.”Chivumbulutso 11:18.

  • “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”Yesaya 33:24.

  • “Anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja awo.”Yesaya 65:22.

Kodi maulosi amenewa adzakwanilitsika bwanji? Mulungu anasankha Mwana wake Yesu, kukhala Mfumu ya boma langwilo limene lidzalamulila dziko lapansi kucokela kumwamba. Baibo imachula bomalo kuti Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44) Pokamba za Yesu, Baibo imati: “Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu. . . , iye adzalamulila monga Mfumu.”—Luka 1:32, 33.

Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anacita zozizwitsa zambili. Anacita izi pofuna kuonetsa kuti monga Wolamulila, adzakonza zinthu kuti anthu akhale na umoyo wabwino kuposa umene tili nawo lomba.

YESU ANAPELEKA DYONKHO LA ZINTHU ZABWINO ZIMENE ADZACITILA ANTHU OMVELA

  • Iye anacilitsa matenda a mtundu uliwonse, kuonetsa kuti adzacotsapo matenda onse pa dziko lapansi.Mateyu 9:35.

  • Analamula nyanja kuti ikhale bata, kuonetsa mmene adzatetezele anthu mwa kulamulila mphamvu za cilengedwe.Maliko 4:36-39.

  • Anadyetsa anthu masauzande, kuonetsa kuti adzapatsa anthu zofunikila pa umoyo wawo.Maliko 6:41-44.

  • Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo pa cikwati, kutsimikizila kuti adzathandiza anthu kusangalala na moyo.Yohane 2:7-11.

Mungacite ciani kuti mukakhale na moyo umene Mulungu akukonzela anthu amene amam’konda? Pali “msewu” wina wake umene mufunika kuyendamo. Baibo imafotokoza kuti msewu umenewu ni ‘wotsogolela ku moyo, ndipo amene akuupeza ndi owelengeka.’—Mateyu 7:14.

MMENE MUNGAPEZELE MSEWU WOPITA KU MOYO WENI-WENI

Kodi msewu wa ku moyo n’ciani? Mulungu akuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.” (Yesaya 48:17) Kuyenda mu msewu umenewu kudzakuthandizani kukhala na umoyo wabwino.

Yesu anati: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo.” (Yohane 14:6) Ngati timakhulupilila coonadi cimene Yesu anaphunzitsa na kutengela citsanzo cake, tidzakhala pa ubwenzi na Mulungu, komanso kukhala na umoyo wopindulitsa.

Kodi mungaupeze bwanji msewu wa ku moyo? Pali zipembedzo zambili, koma Yesu anacenjeza kuti: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 7:21) Iye anakambanso kuti: “Mudzawazindikila ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:16) Baibo ingakuthandizeni kuzindikila kuti cipembedzo ca zoona ni citi.—Yohane 17:17.

Mungacite ciani kuti muyambe kuyenda pa msewu wa ku moyo? Mufunika kuphunzila za amene anapatsa anthu onse moyo. Kodi iye n’ndani? Kodi dzina lake ndani? Kodi ali na makhalidwe abwanji? Kodi wakucitilani ciani? Kodi afuna kuti ife ticite ciani? *

Mulungu safuna kuti tizigwila cabe nchito, kudya, kuseŵela, na kusamalila mabanja athu ayi. Amafunanso kuti tiphunzile za iye monga Mlengi wathu na kukhala mabwenzi ake. Komanso amafuna tizionetsa kuti timam’konda mwa kucita cifunilo cake. Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.”—Yohane 17:3.

KUPITILA M’BAIBO, MULUNGU AMAKUPHUNZITSANI “KUTI ZINTHU ZIKUYENDELENI BWINO.”—YESAYA 48:17

YAMBANI KUYENDA PA MSEWU UMENEWU

Tikadziŵa zimene Mulungu afuna kuti tizicita, tingafunike kusintha zinthu zina mu umoyo wathu. Kucita izi kungaoneke kovuta. Koma m’ceni-ceni, mukayamba kuyenda pa msewu wa ku moyo, umoyo wanu udzakhala wopindulitsa. Pokuthandizani kupeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili ponena za Mulungu, Mboni za Yehova n’zokonzeka kuphunzila na imwe Baibo mahala, pa nthawi na malo amene mungakonde. Mungapemphe kuphunzila nafe Baibo kupitila pa webusaiti yathu ya www.mt1130.com.