Kodi Mudziŵa?
N’cifukwa ciani njiŵa komanso ana a nkhunda zinali kulandilidwa monga nsembe?
PANSI pa Cilamulo, njiŵa komanso ana a nkhunda zinali kulandilidwa monga nsembe kwa Yehova. Mitundu iŵili ya mbalame imeneyi imachulidwa pamodzi m’malamulo okamba za kupeleka nsembe. Ngati munthu analibe njiŵa, anali kupeleka ana a nkhunda. (Lev. 1:14; 12:8; 14:30) Kodi izi zinali zopindulitsa motani? Cifukwa cimodzi n’cakuti, nthawi zina cinali covuta kupeza ana a nkhunda. Cifukwa ciani?
Njiŵa ni mbalame zosamuka-samuka zimene zinali kukhala ku Isiraeli m’miyezi yotentha. Mwezi wa October ukafika, mbalame zimenezi zinali kusamukila ku maiko othuma, ndipo zinali kubwelela ku Isiraeli kukayamba kutentha. (Nyimbo 2:11, 12; Yer. 8:7) Izi zinapangitsa kuti cikhale covuta kwa Aisiraeli kumapeleka njiŵa monga nsembe m’nyengo yozizila.
Koma nkhunda ni mbalame zimene sizisamuka-samuka. Conco, zinali kupezeka ku Isiraeli caka conse. Kuwonjezela apo, mbalamezi zinali zoti munthu akhoza kuweta. (Yelekezelani na Yohane 2:14, 16.) Buku lina lakuti Bible Plants and Animals limati: “Anthu onse m’midzi komanso m’matauni a ku Palestine anali kuweta nkhunda. Mwininyumba aliyense anali kukhala na khola la nkhunda, kapena mphako zimene anali kugoba pacipupa.”—Yelekezelani na Yesaya 60:8.
Yehova anaonetsa kuti ni wacikondi, komanso wololela mwa kulola Aisiraeli kupeleka nsembe mbalame zimene zinali kupezeka caka conse.