Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu

Kristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu

“Kristu ndiye mphamvu ya Mulungu.”—1 AKOR. 1:24.

1. N’cifukwa ciani Paulo ananena kuti “Kristu ndiye mphamvu ya Mulungu”?

YEHOVA anaonetsa mphamvu zake kudzela mwa Yesu Kristu ndipo anacita zimenezi m’njila zapadela kwambili. Mabuku anai a Uthenga Wabwino amafotokoza bwino zozizwitsa zolimbikitsa cikhulupililo zimene Kristu anacita. Iye anacitanso zozizwitsa zina zambili. (Mat. 9:35; Luka 9:11) Kunena zoona, Yesu anaonetsadi mphamvu za Mulungu. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anati: “Kristu ndiye mphamvu ya Mulungu.” (1 Akor. 1:24) Koma, kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa ciani?

2. Tingaphunzilepo ciani pa zozizwitsa za Yesu?

2 Mtumwi Petulo ananena kuti Yesu anacita zozizwitsa, kapena kuti “zodabwitsa.” (Mac. 2:22) Zozizwitsa zimene Yesu anacita zimapeleka cithunzi ca madalitso osaneneka amene tidzalandila mu ulamulilo wake. Zili ngati dyonkho cabe poyelekezela ndi zimene adzacite m’dziko latsopano la Mulungu. Zozizwitsa za Yesu zimatithandizanso kudziŵa bwino umunthu wake ndi wa Atate ake. Tsopano tiyeni tikambilane zozizwitsa zina zimene Yesu anacita ndi kuona mmene zimatikhudzila masiku ano ndi mmene zidzatikhudzila mtsogolo.

COZIZWITSA CIMENE CIMATIPHUNZITSA KUKHALA WOOLOWA MANJA

3. (a) Fotokozani zimene zinapangitsa kuti Yesu acite cozizwitsa coyamba. (b) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti ndi woolowa manja ku Kana?

3 Yesu anacita cozizwitsa cake coyamba pa phwando la ukwati ku Kana wa ku Galileya. Mwina pa phwandolo panabwela anthu ambili kuposa amene anali kuyembekezela. Kaya ndi mmene zinthu zinalili kapena ai, cimene tikudziŵa n’cakuti vinyo unatha pa phwandolo. Mariya, amai ake a Yesu, anapezekapo pa phwandolo. Kwa zaka zambili, Mariya ayenela kuti anali kusinkhasinkha maulosi onena za mwana wake. Iye anali kudziŵa kuti Yesu adzachedwa “Mwana wa Wam’mwambamwamba.” (Luka 1:30-32; 2:52) Kodi Mariya anali kudziŵa kuti Yesu ali ndi mphamvu yocita zozizwitsa? Sitinganene motsimikiza. Koma cimene tikudziŵa n’cakuti Mariya ndi Yesu anamvela cifundo mwamuna ndi mkazi amene anali kukwatilana, ndipo anafuna kuwathandiza kuti asacite manyazi. Yesu anadziŵa kuti kulandila alendo n’kofunika kwambili. Motelo anasandutsa madzi okwana malita 380 kukhala “vinyo wabwino.” (Ŵelengani Yohane 2:3, 6-11.) Kodi Yesu anacita zimenezi mokakamizika? Ai. Iye anacita zimenezi cifukwa cakuti amakonda anthu ndiponso anali kutsanzila Atate ake akumwamba amene ndi woolowa manja.

4, 5. (a) N’ciani cimene tikuphunzilapo pa cozizwitsa coyamba ca Yesu? (b) Kodi cozizwitsa ca ku Kana cimaonetsa kuti zinthu zidzakhala bwanji m’dziko latsopano?

4 Mwanjila yozizwitsa, Yesu anapanga vinyo wambili wokwanila anthu onse amene analipo. N’ciani cimene tikuphunzilapo pa cozizwitsa cimeneci? Tikuphunzilapo kuti iye ndi Atate ake amaganizila anthu ena. Yesu ndi Atate ake si omana. M’dziko latsopano, Yehova adzagwilitsila nchito mphamvu zake kupeleka zakudya zambili zabwino kwa “anthu a mitundu yonse” padziko lapansi.—Ŵelengani Yesaya 25:6.

5 Nthawi ikubwela pamene munthu aliyense adzakhala ndi zonse zofunikila monga cakudya copatsa thanzi ndi nyumba yabwino. Tiyenela kukhala osangalala podziŵa kuti Yehova adzatipatsa zinthu zambili zabwino m’Paladaiso.

Tikamagwilitsila nchito nthawi yathu kuthandiza ena, timaonetsa kuti tikutsanzila mtima wa Yesu woolowa manja (Onani ndime 6)

6. Kodi Yesu anagwilitsila nchito mphamvu zake zozizwitsa pothandiza ndani? Nanga ife tingamutsanzile bwanji?

6 Kumbukilani kuti pamene Mdyelekezi anayesa Yesu kuti asandutse miyala kukhala mitanda ya mkate, Kristu anakana kugwilitsila nchito mphamvu zake zozizwitsa kuti akhutilitse zofuna zake. (Mat. 4:2-4) Koma anali kugwilitsila nchito mphamvu zake pothandiza anthu ena. Kodi tingatsanzile bwanji mtima wa Yesu woganizila ena? Iye analimbikitsa atumiki a Mulungu kuti ayenela ‘kukhala opatsa.’ (Luka 6:38) Tingasonyeze mtima wopatsa mwa kuitanila ena kunyumba kwathu kuti tidzadye nao cakudya ndi kucita nao zinthu zakuuzimu. Kodi tingapatule nthawi pambuyo pa misonkhano kuti tithandize munthu wina amene akufunikila thandizo? Mwacitsanzo, tingamvetsele pamene m’bale kapena mlongo akuyeseza kukamba nkhani yake. Kodi anthu amene afunikila thandizo mu utumiki tingawathandize bwanji? Timaonetsa kuti timatsanzila kuolowa manja kwa Yesu mwa kupatsa ena zinthu zakuthupi ndi za kuuzimu ngati tingakwanitse.

“ONSE ANADYA NDI KUKHUTA”

7. Ndi vuto liti limene silidzatha m’dziko loipali?

7 Umphawi ndi vuto limene linayamba kalekale. Yehova anauza Aisiraeli kuti sadzalephela kukhala ndi wosauka m’dziko lao. (Deut. 15:11) Patapita zaka zambili, Yesu anakamba mau otsimikizila mfundo imeneyi. Iye anati: ‘Osauka muli nao nthawi zonse.’ (Mat. 26:11) Kodi Yesu anali kutanthauza kuti nthawi zonse padziko lapansi padzakhala anthu osauka? Iyai. Iye anali kutanthauza kuti malinga ngati dziko loipali lilipo, anthu osauka adzakhalapobe. Conco, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti zozizwitsa za Yesu zimapeleka umboni wakuti umphawi udzatha mu Ufumu wa Mulungu. Panthawiyo aliyense adzakhala ndi cakudya cokwanila.

8, 9. (a) N’ciani cinacititsa kuti Yesu adyetse anthu masauzande ambili mozizwitsa? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizila cozizwitsa ca Yesu cimeneci?

8 Ponena za Yehova, wamasalimo anati: “Mumatambasula dzanja lanu ndi kukhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.” (Sal. 145:16) Potsanzila Atate ake, ‘Kristu, mphamvu ya Mulungu,’ nthawi zambili anali kutambasula dzanja lake ndi kukhutilitsa zokhumba za otsatila ake. Sikuti iye anali kucita zimenezi kuti aoneke kuti ndi wamphamvu. Koma anali kucita izi cifukwa cokonda anthu mocokela pansi pa mtima. Tiyeni tikambilane zimene zili pa Mateyu 14:14-21. (Ŵelengani.) Ophunzila anabwela kwa Yesu kuti amuuze za vuto la cakudya. Mwacionekele io anali ndi njala, koma anali kudela nkhawa anthu amene anali kutsatila Yesu kucokela m’mizinda cifukwa anafooka ndi njala. (Mat. 14:13) Kodi Yesu anacita ciani?

9 Mwa kugwilitsila nchito mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziŵili, Yesu anadyetsa amuna pafupifupi 5,000, osaŵelengela akazi ndi ana. Kodi sicokondweletsa kuona mmene Yesu anagwilitsila nchito mphamvu zake zozizwitsa posamalila amuna ndi akazi, kuphatikizapo ana ang’ono? Malemba amati: “Onse anadya ndi kukhuta.” Zimenezi zionetsa kuti panali zakudya zoculuka kwambili. Yesu sanangowapatsa mkate wocepa, koma anawapatsa cakudya cokwanila kuti onse akhute ndi kupeza mphamvu zoyendela mtunda wautali pobwelela kwao. (Luka 9:10-17) Ndipo zakudya zokwana madengu 12 zinatsalapo.

10. Pankhani ya umphawi, kodi zinthu zidzasintha bwanji posacedwapa?

10 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambilimbili amavutika ndi njala cifukwa ca ulamulilo woipa wa anthu. Ngakhale abale athu ena sakudya mokwanila. Komabe, posacedwapa anthu omvela adzakhala m’dziko labwino lopanda ziphuphu kapena umphawi. Kodi inuyo mukanakhala ndi mphamvu yopatsa anthu zinthu zofunikila pa umoyo, simukanacita zimenezo? Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi mphamvu yocita zimenezo ndipo amafunitsitsa kutelo. Posacedwapa, iye adzathetsa umphawi ndi njala. —Ŵelengani Salimo 72:16.

11. N’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Kristu adzagwilitsila nchito mphamvu zake kuthetsa mavuto padziko lonse? Nanga zimenezi zimakulimbikitsani kucita ciani?

11 Pamene anali padziko lapansi, Yesu analalikila m’madela ocepa kwa zaka zitatu ndi hafu. (Mat. 15:24) Koma tsopano monga Mfumu yaulemelelo, iye adzalamulila dziko lonse lapansi. (Sal. 72:8) Zozizwitsa za Yesu zimatsimikizila kuti iye amafunitsitsa kugwilitsila nchito mphamvu zake kuthetsa mavuto amene tikukumana nao, ndipo posacedwapa adzacita zimenezo. Ngakhale kuti ifeyo sitingacite zozizwitsa, tingathe kuphunzitsa anthu Mau a Mulungu ouzilidwa. Maulosi a m’Baibulo amatitsimikizila kuti zinthu posacedwapa zidzakhala bwino. Pokhala Mboni za Yehova zodzipeleka, timadziŵa zimene zidzacitika mtsogolo, ndipo tili ndi ngongole youzako ena zimene timaphunzila. (Aroma 1:14, 15) Kukumbukila mfundo imeneyi kuyenela kutilimbikitsa kuuzako ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Sal. 45:1; 49:3.

AMATHA KULAMULILA MPHAMVU ZACILENGEDWE

12. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yesu amadziŵa bwino cilengedwe?

12 Pamene Mulungu anali kulenga dziko lapansi ndi zinthu za m’dziko, Mwana wake wobadwa yekha anali pambali pake monga “mmisili waluso.” (Miy. 8:22, 30, 31; Akol. 1:15-17) Motelo, Yesu amacidziŵa bwino cilengedwe. Iye amadziŵa mmene angasamalile zinthu za m’dzikoli ndi kuzigwilitsila nchito bwino. Amadziŵanso mmene angagaŵile zinthuzo kuti aliyense apindule.

N’ciani cimakucititsani cidwi mukaganizila mmene Yesu anali kugwilitsila nchito mphamvu zake zozizwitsa? (Onani ndime 13 ndi 14)

13, 14. Pelekani citsanzo coonetsa kuti Kristu angathe kulamulila mphamvu zacilengedwe.

13 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti iye ndi “mphamvu ya Mulungu” mwa kulamulila mphamvu za cilengedwe. Ganizilani zimene Yesu anacita pamene ophunzila ake anatsala pang’ono kufa ndi cimphepo camkuntho. (Ŵelengani Maliko 4:37-39.) Katswili wina wa Baibulo anati: “Liu lacigiriki [lomasulidwa kuti “cimphepo camphamvu camkuntho” pa Maliko 4:37] limanena za cimphepo coopsa kwambili camkuntho. Liuli silinena za mphepo wamba . . . koma limanena za cimphepo coopsa camkuntho, cophatikizapo cimvula camphamvu ndi mitambo yakuda bii, cimene cingaononge zinthu kwambili.”—Mat. 8:24.

14 Yelekezelani kuti mukuona mmene zinthu zinalili panthawiyo: Kristu watopa pambuyo polalikila kwa nthawi yaitali. Mafunde akuomba ngalawa mwamphamvu kwambili ndipo madzi ena akugwela m’ngalawayo pamodzi ndi vithovu. Koma ngakhale kuti kuli congo cifukwa ca cimphepo ndi kugwedezeka kwa ngalawa, Yesu akugonabe. Iye afunika kupumula. Cifukwa ca mantha, ophunzila akuutsa Yesu ndi kufuula kuti: “Tikufa!” (Mat. 8:25) Kenako Yesu akuuka ndi kulamula mphepo ndi nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” ndipo mphepoyo ikuleka. (Maliko 4:39) Pamenepa, Yesu anali kulamula mphepo ndi nyanja kuti zikhale cete ndipo zisayambenso kucita zimenezo. Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Baibulo limati: “Panacita bata lalikulu.” Zoonadi, Yesu ali ndi mphamvu kwambili.

15. Kodi Mulungu Wamphamvuyonse waonetsa bwanji kuti amatha kulamulila mphamvu za cilengedwe?

15 Yehova ndiye anapatsa Kristu mphamvu yocita zozizwitsa. Conco, sitiyenela kukaikila kuti Mulungu Wamphamvuyonse amatha kulamulila mphamvu za cilengedwe mmene akufunila. Ganizilani zitsanzo izi: Cigumula cikalibe kufika, Yehova anati: “Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse cimvula padziko lapansi kwa masiku 40, usana ndi usiku.” (Gen. 7:4) Mofananamo, pa Ekisodo 14:21 pamati: “Yehova anacititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugaŵa nyanjayo.” Komanso pa Yona 1:4 pamati: “Yehova anabweletsa cimphepo camphamvu panyanjapo, ndipo panacita mkuntho wamphamvu. Cotelo comboco cinatsala pang’ono kusweka.” N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amatha kulamulila mphamvu zacilengedwe. N’zoonekelatu kuti dziko lapansi lidzakhala ndi wolamulila wabwino mtsogolo.

16. N’cifukwa ciani n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Mlengi wathu ndi Mwana wake amatha kulamulila mphamvu zacilengedwe?

16 N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Mlengi wathu ndiponso ‘mmisili wake waluso’ ali ndi mphamvu zosayelekezeka. Iwo akadzayamba kulamulila dziko lapansi m’zaka 1,000, anthu onse adzakhala otetezeka. Sikudzakhalanso ngozi zacilengedwe. M’dziko latsopano, sitidzaopanso mvula yamkuntho, tsunami, kuphulika kwa mapili, kapena zivomezi. Tidzasangalala kwambili pamene anthu sadzaphedwanso kapena kuvulala ndi ngozi zacilengedwe, cifukwa cakuti “cihema ca Mulungu [cidzakhala] pakati pa anthu.” (Chiv. 21:3, 4) Sitikukaikila kuti kudzela mwa Kristu, Yehova adzalamulila mphamvu zacilengedwe m’zaka 1,000 za ulamulilo wa Yesu.

TSANZILANI MULUNGU NDI KRISTU

17. Tingatsanzile bwanji Yehova ndi Kristu?

17 Mosiyana ndi Yehova ndiponso Yesu, ife sitingathe kuthetsa ngozi zacilengedwe, koma tili ndi mphamvu yocita zinthu zina. Kodi mphamvu imeneyo tingaigwilitsile nchito bwanji? Coyamba, tiyenela kutsatila malangizo a pa Miyambo 3:27. (Ŵelengani.) Abale athu akakumana ndi mavuto, tiyenela kuwatonthoza ndiponso kuwapatsa thandizo lofunikila lakuthupi ndi lakuuzimu. (Miy. 17:17) Mwacitsanzo, tingawathandize pa mavuto amene akukumana nao cifukwa ca ngozi yacilengedwe. Mlongo wina anayamikila thandizo limene analandila pambuyo pakuti nyumba yake yaonongeka cifukwa ca cimphepo coopsa camkuntho. Iye anati: “Ndikuyamikila kwambili kukhala m’gulu la Yehova cifukwa ca thandizo lakuthupi ndi lakuuzimu limene ndalandila.” Komanso mlongo wina wosakwatiwa anathedwa nzelu pamene nyumba yake inaonongeka ndi cimphepo camkuntho. Atalandila thandizo, iye anati: “Sindingathe kufotokoza bwinobwino mmene ndikumvela . . . Zikomo kwambili Yehova.” Timayamikila kwambili kukhala m’gulu la abale amene amakondana ndi kuthandizana ndi mtima wonse. Koma cosangalatsa koposa n’cakuti Yehova ndi Yesu Kristu amasamalila anthu a Mulungu.

18. N’ciani cimakucititsani cidwi mukaganizila cifukwa cake Yesu anali kucita zozizwitsa?

18 Pa utumiki wake, Yesu anaonetsa kuti iye ndi “mphamvu ya Mulungu.” Koma n’cifukwa ciani Yesu anali kucita zozizwitsa? Monga mmene taonela, iye sanagwilitsilepo nchito mphamvu zake kuti adzionetsele kwa ena kapena kuti adzipindulitse. Ndithudi, zozizwitsa zimene Yesu anacita zimasonyeza kuti iye amakonda anthu. Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.