Yembekezelanibe!
“Ngakhale masomphenyawa atazengeleza, uziwayembekezelabe.”—HAB. 2:3.
1, 2. Ndi khalidwe lotani limene atumiki a Yehova akhala nalo kuyambila kalekale?
ATUMIKI a Yehova akhala akuyembekezela kwa nthawi yaitali kukwanilitsidwa kwa maulosi ouzilidwa. Mwacitsanzo, Yeremiya analosela kuti mzinda wa Yuda udzaonongedwa ndi Ababulo, ndipo zimenezo zinacitikadi mu 607 B.C.E. (Yer. 25:8-11) Yesaya amene anauzilidwa kulemba kuti Yehova adzabwezeletsa Ayuda m’dziko lao anati: “Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.” (Yes. 30:18) Nayenso Mika amene anakamba maulosi okhudza anthu akale a Mulungu anati: “Ine ndidzadikilila Yehova.” (Mika 7:7) Kwa zaka zambili, atumiki a Mulungu anali kuyembekezela kukwanilitsidwa kwa maulosi okhudza Mesiya kapena kuti Kristu.—Luka 3:15; 1 Pet. 1:10-12. *
2 Atumiki a Mulungu a masiku ano naonso akuyembekezela kukwanilitsidwa kwa maulosi ena okhudza Mesiya. Yehova adzagwilitsila nchito Ufumu wa Mesiya kuthetsa mavuto a anthu. Adzacita zimenezo mwa kuononga anthu oipa ndi kupulumutsa anthu ake ku dziko loipa la Satana. (1 Yoh. 5:19) Conco, tiyeni tikhalebe maso ndi kukumbukila kuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili.
3. Ndi funso liti limene lingakhalepo ngati tayembekezela mapeto kwa nthawi yaitali?
3 Popeza ndife atumiki a Yehova, timalakalaka kuona cifunilo ca Mulungu ‘cikucitika, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.’ (Mat. 6:10) Pamene tiyembekezela mapeto a dzikoli amene akuoneka ngati akucedwa, ena angafunse kuti, ‘Kodi tifunika kuyembekezelabe?’ Tiyeni tione.
N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKA KUYEMBEKEZELABE?
4. N’cifukwa ciani tiyenela kukhalabe maso?
4 Baibulo limakamba mosapita m’mbali za khalidwe limene tifunika kuonetsa pamene mapeto akuyandikila. Yesu anauza otsatila ake kuti ayenela ‘kukhalabe maso.’ (Mat. 24:42; Luka 21:34-36) Pa cifukwa cimeneci, tifunika kupitiliza kuyembekezela. Gulu la Yehova lapeleka citsanzo cabwino pankhani imeneyi. Mabuku athu akhala akutilimbikitsa kuti tiyenela ‘kuyembekezela ndi kukumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Amatilimbikitsanso kuika maganizo athu pa dziko latsopano limene Mulungu watilonjeza.—Ŵelengani 2 Petulo 3:11-13.
5. N’cifukwa ciani kukhalabe maso n’kofunika kwambili masiku ano?
5 Akristu a m’nthawi yakale anafunika kuyembekezela tsiku la Yehova, ndipo kucita zimenezi n’kofunika kwambili kwa ife masiku ano. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa tikukhala m’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu. Cizindikilo ca kukhalapo kwake cakhala cikuonekela kuyambila mu 1914. Cizindikilo cimeneco cimene ciphatikizapo zinthu zimene zikuipilaipila m’dzikoli ndiponso nchito yolalikila Ufumu padziko lonse, cikuonetsa kuti tikukhala m’nthawi ya “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3, 7-14) Popeza Yesu sanakambe utali wa nthawi ya mapeto imeneyi, tifunika kukhalabe maso.
6. N’cifukwa ciani tiyenela kuyembekezela kuti zinthu padzikoli zidzaipa kwambili pamene mapeto akuyandikila?
6 Mwina tingafunse kuti: Kodi “mapeto a nthawi ino” satanthauza nthawi yamtsogolo imene zinthu padzikoli zidzaipa kwambili? Baibulo lionetsa kuti zinthu zidzaipilaipila ‘m’masiku otsiliza.’ (2 Tim. 3:1, 13; Mat. 24:21; Chiv. 12:12) Conco, tiyenela kuyembekezela kuti zinthu padzikoli zidzaipa kwambili mtsogolo kuposa masiku ano.
7. Kodi lemba la Mateyu 24:37-39 limaonetsa ciani ponena za mmene zinthu padzikoli zidzakhalila m’masiku otsiliza?
7 Koma kodi muona kuti zinthu zidzaipa kufika pati ‘cisautso cacikulu’ cisanayambe? (Chiv. 7:14) Mwacitsanzo, kodi mukuyembekezela kuti m’dziko lililonse mudzakhala nkhondo, munthu aliyense adzasoŵelatu cakudya, ndipo panyumba iliyonse padzakhala wodwala? Ngati zinthu zingakhale conco, ndiye kuti anthu amene sakhulupilila Baibulo angavomeleze kuti ulosi wa m’Baibulo ukukwanitsidwa. Komabe, Yesu anakamba kuti anthu ambili ‘adzanyalanyaza’ kapena kuti sadzadziŵa za kukhalapo kwake, ndi kuti adzatangwanika ndi zocitika za paumoyo mpaka zinthu zitafika pa mwana wakana phala. (Ŵelengani Mateyu 24:37-39.) Motelo, sitiyenela kuyembekezela kuti zinthu padzikoli zidzafika poipitsitsa cisautso cacikulu cisanayambe.—Luka 17:20; 2 Pet. 3:3, 4.
8. Popeza tili chelu, kodi ndife otsimikiza mtima za ciani?
8 Colinga cimene Yesu anauzila otsatila Mat. 24:27, 42) Kuyambila mu 1914 mbali zosiyanasiyana za cizindikilo cimene Yesu ananena zikukwanilitsidwa. Sitikukaikila kuti tikukhaladi m’nthawi ya “mapeto a nthawi ino.” Ndipo Yehova anaika kale nthawi imene adzaononga dziko loipali la Satana.
ake za cizindikilo ca kukhalapo kwake cinali cakuti adzakhale maso. Conco, kuyambila kale otsatila a Yesu apitilizabe kukhala chelu. (9. N’cifukwa ciani tiyenela kuyembekezelabe mapeto a dziko loipali?
9 Nanga n’cifukwa ciani Akristu masiku ano afunika kuyembekezelabe? Tifunika kuyembekezelabe cifukwa comvela Yesu Kristu, ndiponso cifukwa coona cizindikilo ca kukhalapo kwake. Ciyembekezo cathu si copanda maziko, koma n’cozikidwa zolimba pa umboni wa m’Malemba umene umaticititsa kukhalabe maso ndi kuyembekezela mapeto a dziko loipali.
TIDZAYEMBEKEZELA MPAKA LITI?
10, 11. (a) Kodi Yesu anakonzekeletsa ophunzila ake kaamba ka nchito yotani? (b) N’ciani cimene Yesu anauza otsatila ake kucita ngati io akuona kuti mapeto akucedwa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
10 Ambili a ife takhala maso mwakuuzimu kwa zaka zambili. Komabe, tifunika kuyembekezelabe ngakhale kuti tacita zimenezo kwa nthawi yaitali. Yesu adzabwela kudzaononga dzikoli. Conco, tifunika kukonzekela. Musaiŵale kuti Yesu analangiza otsatila ake kuti: “Khalani maso, khalani chelu, pakuti simukudziŵa pamene nthawi yoikidwilatu idzafika. Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina, amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa nchito yake, ndi kulamula mlonda wa pacipata kuti azikhala maso. Conco khalani maso, pakuti simukudziŵa nthawi yobwela mwininyumba. Simukudziŵa ngati adzabwele madzulo, pakati pa usiku, atambala akulila, kapena m’maŵa, kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona. Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”—Maliko 13:33-37.
11 Pozindikila kuti kukhalapo kwa Kristu kunayamba mu 1914, otsatila a Yesu anadziŵa kuti mapeto ali pafupi. Conco, anayamba kukonzekela. Anacita zimenezo mwa kugwila nchito yolalikila Ufumu mwacangu. Yesu ananena kuti mwina adzabwela “atambala akulila, kapena m’maŵa.” Ngati zinalidi conco, kodi otsatila ake anafunika kucita ciani? Iye anati: “Khalani maso.” Conco, ngakhale tione kuti tayembekezela nthawi yaitali, zimenezo sizitanthauza kuti mapeto ali kutali kapena kuti sadzabwela ife tili moyo.
12. Ndi funso lotani limene Habakuku anafunsa Yehova? Nanga Mulungu anayankha bwanji?
12 Ganizilani citsanzo ca Habakuku, amene anauzidwa kuti alosele za kuonongedwa kwa Yerusalemu. Nthawi imene iye anali kulengeza zimenezo, macenjezo okhudza kuonongedwa kwa mzindawo anali atapelekedwa kwa zaka zambili. Zinthu zinafika poipa cakuti ‘anthu oipa anali kupondeleza anthu olungama.’ Mpake kuti Habakuku anafunsa kuti: “Inu Yehova, kodi ndidzalilila thandizo koma inu osandimva kufikila liti?” M’malo moyankha funso limenelo mwacindunji, Yehova anatsimikizila mneneli wake wokhulupilikayo kuti cionongeko cimene anakambilatu ‘sicidzacedwa.’ Yehova anauza Habakuku kuti ayenela ‘kuyembekezelabe.’—Ŵelengani Habakuku 1:1-4; 2:3.
13. Ndi maganizo otani amene Habakuku akanakhala nao? N’cifukwa ciani kukanakhala kupanda nzelu kuganiza conco?
13 Bwanji ngati Habakuku akanakhumudwa ndi kuyamba kuganiza kuti: ‘Kwa zaka
zambili, ndakhala ndikumva kuti Yerusalemu adzaonongedwa. Nanga bwanji ngati zimenezo sizidzacitika posacedwapa? Ndidzivutila ciani kulosela za cionongeko ngati kuti mzindawu udzaonongedwa maŵa. Lekani ndingosiila ena nchitoyi.’ Habakuku akanakhala ndi maganizo amenewa, Yehova akanasiya kumukonda, ndipo mwacionekele akanaonongedwa panthawi imene Ababulo anaononga Yerusalemu.14. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza mtima kuti sitidzagwilitsidwa mwala ngati tikuyembekezelabe?
14 Yelekezelani kuti muli m’dziko la tsopano. Zinthu zonse zimene Yehova analosela ponena za masiku otsiliza zakwanilitsidwa. Mukudalila Yehova kwambili, ndipo simukaikila kuti adzakwanilitsanso zinthu zina zimene walonjeza. (Ŵelengani Yoswa 23:14.) Zoonadi, tidzayamikila kwambili kuti Mulungu amene ‘anaika nthawi kapena nyengo pansi pa ulamulilo wake, anatilangiza kukhala maso popeza ‘mapeto a zinthu zonse anali atayandikila.’—Mac. 1:7; 1 Pet. 4:7.
KHALANI OTANGWANIKA PAMENE MUKUYEMBEKEZELA
15, 16. N’cifukwa ciani tifunika kucita zilizonse zimene tingathe pamene tikulalilkila m’masiku otsiliza ano?
15 Gulu la Yehova lidzapitilizabe kutikumbutsa kuti tizitumikila Mulungu modzipeleka kwambili. Zikumbutso zimenezo zimatilimbikitsa kukhala otangwanika mu utumiki wa Mulungu, ndiponso zimatithandiza kudziŵa kuti cizindikilo ca kukhalapo kwa Kristu cikukwanilitsidwa. Tifunika kupitiliza kufunafuna Ufumu coyamba ndi cilungamo ca Mulungu mwa kutengako mbali panchito yolalikila uthenga wabwino.—Mat. 6:33; Maliko 13:10.
16 Tikamalalikila uthenga wabwino kwa anthu ena, timawathandiza kuti asakaonongeke pamene dziko la Satanali likuonongedwa. Mu 1945, kunacitika ngozi yoopsa pa madzi pamene ngalawa yochedwa Wilhelm Gustloff inamila ndipo anthu masauzande ambili anafa. Pokumbukila zimene zinacitika, Mlongo wina amene anapulumutsidwa pamodzi ndi mwamuna wake ananena kuti pamene ngalawayo inali kumila mayi wina anali kulila uku akukuwa kuti: “Masutikesi anga! Masutikesi anga ine! Mama ine mphete zanga! Ndolo zanga! Zibangili zanga! Zanga zonse zataika!” Koma anthu ena anadziŵa kuti moyo ndiwo unali wofunika kwambili cakuti anacita zomwe angathe kuti apulumutse anthu. Masiku anonso miyoyo ya anthu ili pangozi. Mofanana ndi anthu aja amene anapulumutsa anthu ena, ifenso timagwila nchito yolalikila mwakhama cifukwa ifunika kucitidwa mwamsanga.
Tiyeni ticite zimene tingathe kuti tithandize anthu kuti akapulumuke pamene dzikoli likuonongedwa.17. Ndi zifukwa ziti zimene zimaticititsa kukhulupilila kuti mapeto adzafika nthawi iliyonse?
17 Zinthu zimene zikucitika padzikoli zikuonetsa kuti ulosi wa m’Baibulo ukukwanilitsidwa ndiponso kuti mapeto a dongosolo loipali ayandikila. Conco, tisaganize kuti kukali nthawi yaitali kuti “Nyanga 10, komanso cilombo” zochulidwa pa Chivumbulutso 17:16 ziukile Babulo wamkulu amene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Tisaiŵale kuti Mulungu ndiye ‘adzaika maganizo m’mitima yao kuti cilomboco ciukile zipembezo zonyenga. Ndipo zimenezi zidzacitika modzidzimutsa ndiponso panthawi iliyonse. (Chiv. 17:17) Mapeto adongosolo lino sali patali. Conco, ndi pofunika kumvela cenjezo la Yesu lakuti: “Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambili, kumwa kwambili, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikileni modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34, 35; Chiv. 16:15) Tiyeni titumikile Yehova modzipeleka tili ndi cidalilo cakuti iye ‘amathandiza anthu amene amamuyembekezela’—Yes. 64:4.
18. Tidzakambilana funso liti m’nkhani yotsatila?
18 Pamene tikuyembekezela mapeto a dongosolo loipali, tiyenela kumvela mau ouzilidwa a mtumwi Yuda akuti: “okondedwa, podzilimbitsa pamaziko a cikhulupililo canu coyela kopambana, ndi kupemphela mu mphamvu ya mzimu woyela, pitilizani kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kukukondani. Citani zimenezi pamene mukuyembekezela kuti cifundo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cidzakutsegulileni njila yoti mulandilile moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Nanga tingaonetse bwanji kuti tikuyembekezela mwacidwi lonjezo la Mulungu la paladaiso? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.
^ par. 1 Kuti mudziŵe maulosi ena a m’Baibulo okhudza Mesiya ndi mmene anakwanilitsidwila, onani patsamba 200 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceniceni.